bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 48
Jeremiah 48
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 47
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 49 →
1
Ponena za Mowabu, Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuti, “Tsoka kwa mzinda wa Nebo, wasanduka chipululu. Kiriyataimu wachititsidwa manyazi, wagonjetsedwa. Linga lake lankhondo alinyoza ndipo aligumula.
2
Mowabu sakutchukanso. Adampanganirana zachiwembu ku Hesiboni, adati, ‘Tiyeni timuwononge, asakhalenso mtundu wa anthu.’ Ndipo inu okhala ku Madimeni, adzakukhalitsani chete, adzakupirikitsani ndi lupanga.
3
“Imvani kulira kwachisoni kwa anthu a ku Horonaimu, akuti, ‘Chisakazo ndi chiwonongeko chachikulutu!’
4
Mowabu waonongeka, ana ake akulira kwambiri.
5
Anthu akupita nalira kwambiri pa chikwera cha ku Luhiti. Kulira kwa chiwonongeko kukumveka ku matsitso a ku Horonaimu.
6
Thaŵani, mudzipulumutse. Thamangani ngati mbidzi yam'chipululu.
7
Inunso mudzagwidwa chifukwa choti munkadalira ntchito zanu ndi chuma chanu. Kemosi, mulungu wanu, adzatengedwa ukapolo, pamodzi ndi ansembe ake ndi akalonga ake.
8
Woononga uja adzasakaza mzinda uliwonse, palibe mzinda ndi umodzi womwe umene udzapulumuke. Malo am'zigwa adzaonongeka, malo okwera nawonso adzasakazika. Zidzachitika monga momwe Chauta adanenera.
9
“Mowabu mchenjezeni, chifukwa posachedwa asakazika. Mizinda yake isanduka mabwinja, ikhala yopanda anthu.
10
“Ndi wotembereredwa amene amagwira ntchito ya Chauta mwaulesi. Ndi wotembereredwa amene amaletsa lupanga lake kutema ndi kupha anthu.
11
Mowabu wakhala pa mtendere kuyambira unyamata wake, ngati vinyo wokhazikika pa masese ake, osapungulidwa kuchoka mu mtsuko wina kuthira mu mtsuko wina. Sadatengedwe ukapolo. Nchifukwa chake khalidwe lake lili losasinthika, ndipo fungo lake lili lomwe lija.”
12
Chauta akunena kuti, “Chenjerani tsono, akubwera masiku pamene ndidzatuma anthu oti Mowabuyo adzamkhuthule ngati vinyo. Kenaka mitsuko yake itasanduka yopanda kanthu m'kati, ndidzaiphwanya.
13
Motero Mowabu adzachita manyazi ndi Kemosi, mulungu wake, monga momwe Israele adachitira naye manyazi Betele, mulungu amene ankamukhulupirira.
14
“Kodi mungathe kunena bwanji kuti, ‘Ife ndife ngwazi, asilikali olimba mtima pa nkhondo?’
15
Woononga Mowabu ndi mizinda yake wabwera. Anyamata ake asee akupita kukaphedwa. Ikutero mfumu imene dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse.
16
Kugwa kwa Mowabu kuli pafupi. Chiwonongeko changokhala pang'onong'ono kuti chimugwere.
17
Mumvereni chisoni kwambiri inu nonse anansi ake, anzake nonse amene mumamdziŵa. Ndipo munene kuti, ‘Ogo, taonani m'mene yathyokera ndodo yachifumu yamphamvu ija! Taonani m'mene yathyokera ndodo yaulemu ija!’
18
“Inu anthu a ku Diboni, tsikanipo pa ulemerero wanu, khalani pansi poumapa. Woononga Mowabu wafika kudzamenyana nanu, wapasula malinga anu ankhondo.
19
Inu amene mumakhala ku Aroere, imani m'mbali mwa mseu muziwonerera. Mufunse mwamuna amene wathaŵa ndiponso mkazi amene wapulumuka, munene kuti, ‘Kodi kwagwanji?’
20
Iwo adzayankha kuti, ‘Ukutu Mowabu wagwa, amchititsa manyazi, mlireni mofuula. Mulengeze ku mtsinje wa Arinoni kuti Mowabu wasanduka bwinja.’
21
“Chiweruzo chafika ku dziko lakumapiri, ndiye kuti mizinda iyi: Holoni, Yaza, Mefati
22
ndi Diboni, Nebo ndi Betedibilataimu,
23
Kiriyataimu, Betegamuli, Betemeoni,
24
Keriyoti, Bozira ndi mizinda yonse ya ku Mowabu, yakutali ndi yakufupi.
25
Mphamvu za Mowabu zaonongeka, mkono wake wolimba wathyoka,” akutero Chauta.
26
“Mledzeretseni Mowabu chifukwa adadzikuza poukira Chauta. Avimvinizike m'masanzi ake omwe. Akhale chinthu chomachiseka.
27
Kodi suja Israele adaali chinthu chonyozeka kwa iwe? Kodi adapezeka pakati pa mbala, kuti nthaŵi zonse polankhula za iye uzimpukusira mutu momunyoza?”
28
Chauta akuti, “Inu okhala ku Mowabu, siyani mizinda yanu. Kapezeni pokhala pakati pa mathanthwe. Mukhale ngati nkhunda yomanga chisa kukamwa kwa phanga.
29
Tamva za kunyada kwa Mowabu, ndi wonyadadi kwabasi. Ndi wodzikweza, wodzitama, wodzitukumula, ndipo ndi wa mtima wodzimva zedi.
30
Ndikudziŵa kudzikuza kwake. Mau ake odzitama ngachabechabe, ntchito zake nzopanda pake.
31
Motero ndikulira chifukwa cha Mowabu. Ndikulira mwachisoni chifukwa cha anthu onse a ku Mowabu. Ndikulira anthu a ku Kiriheresi.
32
Ndikulira anthu a ku Sibima kupambana m'mene ndidalirira anthu a ku Yazere. Iwe mzinda wa Sibima, uli ngati mpesa umene nthambi zake zidatambalala mpaka ku nyanja, kukafika mpaka ku Yazere. Woononga wasakaza zipatso zako zam'chilimwe, wasakaza mipesa yako yonse.
33
Kusangalala ndi kukondwa kwa dziko lachonde la Mowabu kwatha. Ndaletsa kuchucha kwa vinyo mopondera mphesa. Palibe amene akufuula mokondwa akamaponda mphesa. Kufuula kulipo, koma si kufuula kokondwa ai.
34
“A ku Hesiboni ndi a ku Eleale akulira movutika. Kulira kwao kukumveka mpaka ku Yaza, kuchokera ku Zowari mpaka ku Horonaimu ndi ku Egilati-Selisiya. Ngakhale madzi a ku Nimurimu aphwa.
35
Ndidzaŵaphadi Amowabu amene amapereka nsembe ku akachisi ku mapiri, ndi kufukiza lubani kwa milungu yao,” akutero Chauta.
36
“Nchifukwa chake mtima wanga ukulira Mowabu ngati chitoliro. Mtima wanga ukulira anthu a ku Kiriheresi ngati chitoliro, chifukwa chuma chao chonse chimene adaachipata chatheratu.
37
Kumutu kwa munthu aliyense nkometa, ndevu nazonso nzometa, manja onse ndi ochekekachekeka, ndipo m'chiwuno mwao avala ziguduli.
38
Pa madenga onse a ku Mowabu ndiponso m'miseu yake simukumvekanso kanthu kena, koma kulira kokha. Ndamtswanya Mowabu ngati chiŵiya chopanda ntchito.
39
Taonani m'mene watswanyikira! Tamvani m'mene akulirira anthu ake! Taonani m'mene wakhalira chofulatira mwamanyazi! Mowabu wasanduka chinthu chonyozeka, chinthu chochititsa mantha kwa anzake okhala nawo pafupi,” akutero Chauta.
40
Chauta akunena kuti, “Mtundu wina udzachita kuuluka nkudzagwera Mowabu ngati nkhwazi ya mapiko otambalitsa.
41
Mizinda idzagwidwa, malinga adzalandidwa. Tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Mowabu idzakhala ili thithithi ndi mantha, ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira.
42
Mowabu adzaonongeka, sadzakhalanso mtundu wa anthu, pakuti adadzikuza poukira Chauta.
43
Nkhaŵa, dzenje ndi msampha zikuyembekeza inu anthu okhala ku Mowabu,” akutero Chauta.
44
“Wothaŵa nkhaŵa, adzagwa m'dzenje. Wotuluka m'dzenje, adzakodwa mu msampha. Zimenezi nzimene ndidzamgwetsere Mowabu pa nthaŵi ya chilango chake,” akutero Chauta.
45
“Amene akuthaŵa, amaima pa mthunzi wa Hesiboni, chifukwa chotopa kwambiri. Koma moto wayaka kuchokera ku Hesiboni, malaŵi a moto abuka kuchokera ku nyumba ya mfumu Sihoni, ndipo motowo ukuwononga mapiri a ku Mowabu, dziko la anthu andeu.
46
Tsoka kwa iwe Mowabu! Anthu opembedza Kemosi atha. Ana ako onse aamuna ndi aakazi adatengedwa ukapolo.
47
Komabe masiku akutsogolo ndidzambwezeranso ufulu Mowabu,” akutero Chauta. Chiweruzo cha Mowabu chathera pamenepa.
← Chapter 47
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 49 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52