bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 38
Jeremiah 38
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 37
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 39 →
1
Tsono Sefatiya mwana wa Matani, Gedaliya mwana wa Pasuri, Yukala mwana wa Selemiya, ndi Pasuri mwana wa Malakiya, adamva zimene Yeremiya ankauza anthu zoti
2
Chauta akunena kuti, “Aliyense amene atsalire mu mzinda uno adzafa ndi nkhondo, njala ndiponso mliri. Koma aliyense amene atuluke kukadzipereka kwa Ababiloni adzakhala moyo, adzapulumutsa moyo wake.
3
Mzinda uno udzaperekedwadi kwa ankhondo a mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzaulanda.”
4
Tsono akuluakulu adauza mfumu kuti, “Munthuyu ayenera kuphedwa. Akutayitsa mtima ankhondo ndi anthu onse otsalira mu mzinda, chifukwa cha zolankhula zakezi. Munthu ameneyu sakuŵafunira zabwino anthu, angofuna kuti aonongedwe basi.”
5
Mfumu Zedekiya adati, “Suyu, ali m'manja mwanu. Ine mfumu sindingakuletseni ai.”
6
Choncho iwo aja adatenga Yeremiya, nakamponya m'chitsime chimene adaakumba Malakiya mwana wa mfumu, m'bwalo la alonda a mfumu. Adamtsitsira m'menemo ndi chingwe. M'chitsimemo munalibe madzi, munali matope okhaokha. Ndipo Yeremiya adamira m'matopemo.
7
Tsono Ebedemeleki, Mkusi wina wofulidwa wogwira ntchito ku nyumba ya mfumu, adamva kuti Yeremiya amponya m'chitsime. Nthaŵi imeneyo nkuti mfumu ili ku Chipata cha Benjamini.
8
Ebedemeleki adatuluka ku nyumba ya mfumu kukaiwuza kuti,
9
“Mfumu mbuyanga, anthu aŵa amchita zoipa kwambiri mneneri Yeremiya. Amponya m'chitsime, ndipo poti buledi adatha mu mzinda, adzafa ndi njala m'menemo.”
10
Tsono mfumu idalamula Mkusi Ebedemeleki kuti, “Tenga anthu atatu, mukamtulutse mneneri Yeremiya asanafe.”
11
Apo Ebedemeleki adapita ku nyumba ya mfumu ndi anthuwo, nakatenga nsanza m'chipinda cha zovala. Nsanzazo adazitsitsa ndi zingwe m'chitsime m'mene munali Yeremiya.
12
Ebedemeleki Mkusi uja adauza Yeremiya kuti, “Ikani nsanzazi m'kwapa mwanu kuti zingwe zingakupwetekeni.” Yeremiya adachitadi zimenezo.
13
Tsono adamtulutsira kunja ndi zingwe, ndipo Yeremiya adakakhalanso konkuja ku bwalo la alonda.
14
Tsiku lina mfumu Zedekiya adaitana mneneri Yeremiya namlandira pa chipata chachitatu cha ku Nyumba ya Chauta. Adamuuza kuti, “Ndifuna kukufunsa kanthu, usati undibisire ai.”
15
Yeremiya adayankha kuti, “Ndikakuuzani, mosapeneka konse mundipha. Ndikakulangizani simumvera.”
16
Apo mwachinsinsi mfumu Zedekiya adalumbira pamaso pa Yeremiya kuti, “Pali Chauta wamoyo amene adatipatsa moyo, ine sindikupha. Ndipo sindikupereka kwa anthu amene afuna kukuphaŵa.”
17
Yeremiya adauza Zedekiya kuti, “Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, ‘Ngati mutuluka kukadzipereka kwa akuluakulu a mfumu ya ku Babiloni, mudzakhala ndi moyo, ndipo mzinda uno sadzautentha. Inuyo pamodzi ndi banja lanu mudzakhala moyo.
18
Koma mukangopanda kudzipereka kwa akuluakulu a mfumu ya ku Babiloni, mzindawu udzaperekedwa m'manja mwa Ababiloni, ndipo adzautentha, tsono inu simudzapulumuka m'manja mwao.’ ”
19
Mfumu Zedekiya adauza Yeremiya kuti, “Ndikuwopa Ayuda amene adathaŵira kale kwa Ababiloni. Ndikuwopa kuti Ababiloni adzandipereka kwa Ayudawo, ndipo iwowo adzandichita zoipa.”
20
Yeremiya adayankha kuti, “Iyai, sadzakuperekani. Ngati mumvera Chauta pa zonse, ndikukuuzani kuti zinthu zonse zidzakuyenderani bwino, ndipo mudzakhala ndi moyo.
21
Koma mukakana kutuluka kuti mukadzipereke, Chauta wandiwululira kuti
22
akazi onse otsala m'nyumba ya mfumu ya ku Yuda, adzaperekedwa kwa akuluakulu a mfumu ya ku Babiloni. Popita ku Babiloniko, akazi amenewo azidzaimba kuti, “ ‘Abwenzi ako okhulupirika aja adakunyenga, ndipo adakugonjetsa. Tsopano poti miyendo yako yazama m'matope, abwenzi akowo akusiya.’
23
Akazi anu onse pamodzi ndi ana adzaŵapereka m'manja mwa Ababiloni. Ndipo inuinuyo simudzalephera kugwa m'manja mwao. Mudzagwidwa ndi mfumu ya ku Babiloni, kenaka mzinda uno adzautentha.”
24
Pamenepo Zedekiya adauza Yeremiya kuti, “Usauze munthu wina aliyensetu zimenezi, kuti ungaphedwe.
25
Akuluakulu akamva kuti ndakhala ndikulankhula nawe, makamaka abwera kwa iwe kudzanena kuti, ‘Utiwuze zimene wauza amfumu, ndi zimene iwowo akuuza, usatibisire, ndipo sitidzakupha.’
26
Tsono udzaŵayankhe kuti, ‘Ndinalikupempha kwa amfumu kuti asandibwezenso ku nyumba ya Yonatani, kuti ndikafe kumeneko.’ ”
27
Akuluakulu onse adabweradi kwa Yeremiya kudzamufunsa. Iye adaŵayankha monga momwe mfumu idamuuzira. Motero nkhani zao zidathera pomwepo, chifukwa mau aja anali asanamveke kwa munthu wina aliyense.
28
Tsono Yeremiya adakhalabe m'bwalo la alonda, mpaka tsiku limene mzinda wa Yerusalemu udagonjetsedwa.
← Chapter 37
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 39 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52