bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 4
Jeremiah 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 5 →
1
“Ngati mukufuna kubwerera, inu Aisraele, bwererani kwa Ine,” akuterotu Chauta. “Chotsani mafano anu amene akundinyansaŵa, ndipo musasokerenso.
2
Muzilumbira moona kuti, ‘Pali Chauta wamoyo.’ Muzichita zimenezi mwachilungamo ndi mokhulupirika. Mukatero, anthu a mitundu yonse adzandipempha kuti ndiŵadalitse, ndipo adzanditamanda.”
3
Chauta akuuza anthu a ku Yuda ndi anthu okhala ku Yerusalemu kuti, “Limani masala anu, musabzale pakati pa minga.
4
Muzikhala okhulupirika ndi kumanditumikira Ine Chauta ndi mtima wanu wonse. Muzichita zimenezi inu anthu a ku Yuda ndi inu okhala ku Yerusalemu, kuwopa kuti mkwiyo wanga ungabuke ngati moto, ndi kukuyakirani chifukwa cha ntchito zanu zoipa, osapezeka wina aliyense wotha kuuzimitsa.”
5
Lalika ku Yuda, lengeza ku Yerusalemu kuti, “Lizani lipenga m'dziko lonse, ndi kufuula kuti, ‘Sonkhanani, tiyeni tipite ku mizinda ku Ziyoni.’
6
Kwezani mbendera ku Ziyoni. Musachedwe, thaŵani kuti mupulumuke. Chauta akubweretsa chilango kuchokera kumpoto, kudzakhala chiwonongeko chachikulu.
7
Monga momwe mkango umatulukira m'ngaka yake, momwemonso woononga maiko wanyamuka. Watuluka m'malo mwake kuti asakaze dziko lanu. Mizinda yanu idzakhala mabwinja popanda okhalamo.
8
Motero valani ziguduli, mudandaule ndi kulira kwambiri. Pakuti mkwiyo woopsa wa Chauta sudatichoke.”
9
Chauta akuti, “Pa tsiku limenelo mfumu ndi nduna zake, onse adzataya mtima. Ansembe adzaopsedwa, ndipo aneneri adzangoti kakasi.”
10
Tsono ndidati, “Ha, Ambuye Chauta, ndithu mudaŵanyenga anthu aŵa pamodzi ndi a mu Yerusalemu! Mudaŵauza kuti, ‘Mudzakhala pa mtendere,’ koma chonsecho lupanga lili pamutu pao.”
11
Nthaŵiyo ikadzafika, anthu a mu Yerusalemu adzaŵauza kuti, “Mphepo yotentha yochokera ku magomo am'chipululu ikukuntha pa anthu anga, osatitu mphepo yopetera kapena kuyeretsera zinthu ai.
12
Imeneyo ndi mphepo yamphamvu zedi yochokera kwa Ine Mulungu. Ndipo ndi Ineyo amene ndikuŵaimba mlandu.”
13
Onani, adani akubwera mwaliŵiro ngati mitambo, magaleta ao akuthamanga ngati kamvulumvulu. Akavalo ao ngaliŵiro kuposa chiwombankhanga. Kalanga ine, taonongeka.
14
Iwe Yerusalemu, chotsa zoipa mumtima mwako kuti upulumuke. Kodi maganizo ako oipa udzakhala nawobe mpaka liti?
15
Pakuti amithenga a ku Dani akulalika mau, akulengeza zoopsa kuchokera ku Phiri la Efuremu.
16
Akuti, “Muchenjeze mitundu ya anthu kuti mdani akubwera. Mulengeze kwa anthu a mu Yerusalemu kuti ankhondo akubwera kuchokera ku dziko lakutali, akufuula ndi kudzathira nkhondo mizinda ya Yuda.
17
Akuzinga Yerusalemu ngati alonda a munda, chifukwa choti anthu andipandukira,” akuterotu Chauta.
18
“Zimenezi zakugwerani, inu Ayuda, chifukwa cha makhalidwe anu oipa ndi zochita zanu. Chimenechi ndiye chilango chanu, nchoŵaŵa kwambiri, chokalasa mpaka ku mtima.”
19
Mayo, mayo, ati kupweteka ati! Ha, mtima wanga ukuŵaŵa, ukugunda moti thithithi. Sindingathe kukhala chete. Ndikumva kulira kwa lipenga ndi mfuu yankhondo.
20
Tsoka limatsata tsoka linzake, ndipo dziko lonse lasanduka bwinja. Mwadzidzidzi mahema athu aonongeka, machinga ake agwetsedwa pa kanthaŵi kang'onong'ono.
21
Kodi ndikhale ndikuwona mbendera yankhondo mpaka liti? Kodi ndikhale ndikumva lipenga mpaka liti?
22
Chauta akuti “Paja anthu anga ndi opusa, Ine sandidziŵa. Ali ngati ana opulukira, osamvetsa chilichonse. Ali ndi luso pochita zoipa, koma kuchita zabwino sadziŵa.”
23
Ndidayang'ana dziko lapansi, linali lopanda anthu ndi lopanda kanthu kalikonse. Ndidayang'ana thambo, linalibe konse kuŵala.
24
Ndidayang'ana mapiri, ankagwedezeka, ndipo magomo onse ankangosunthira uku ndi uku.
25
Ndidayang'ana, osaona ndi munthu mmodzi yemwe, ndipo mbalame zonse zamumlengalenga zinali zitathaŵa.
26
Ndidayang'ana, dziko la chonde linali litasanduka chipululu, mizinda yake yonse inali itasanduka mabwinja, chifukwa cha mkwiyo wa Chauta.
27
Chauta akunena kuti, “Dziko lonse lidzasanduka chipululu, komabe sindidzaliwononga kotheratu.
28
Chifukwa cha zimenezi dziko lonse lapansi lidzalira ndipo zakumwamba zidzachita mdima. Pakuti Ine ndalankhula, ndipo ndili ndi cholinga. Sindidafeŵe mtima, ndipo sindidzabwerera konse m'mbuyo.”
29
Anthu a m'mudzi uliwonse adzathaŵa, pakumva phokoso la ankhondo okwera pa akavalo ndi oponya mivi. Azikati uku ena akuloŵa m'nkhalango, ena akukwera m'mathanthwe. Mizinda yonse kuisiya, popanda ndi mmodzi yemwe wokhalamo.
30
Iwe Yerusalemu, ndiwe bwinja. Ukuti utani m'mene ukuvala zofiira, m'mene ukuvala zokongoletsa zagolide, m'mene ukukuza maso ako poŵapaka zokometsera? Ukungodzivuta poyesa kudzikongoletsa. Zibwenzi zako zikukunyoza, zikufuna kulanda moyo wako.
31
Ndidamva kulira ngati kwa mkazi pa nthaŵi yake yochira, kubuula ngati kwa mkazi pa uchembere wake woyamba. Kumeneku kunali kulira kwa anthu a mu Ziyoni, ŵefuŵefu, atatambalitsa manja ao, akunena kuti, “Tsoka ife! Tikukomoka, moyo wathu waperekedwa kwa anthu otipha.”
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52