bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 46
Jeremiah 46
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 45
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 47 →
1
Chauta adauza mneneri Yeremiya mau onena za anthu a mitundu ina.
2
Kunena za Ejipito, adanena za gulu lankhondo la Farao Neko, mfumu ya ku Ejipito, limene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adaligonjetsa ku Karikemisi ku mtsinje wa Yufurate pa chaka chachinai cha ufumu wa Yehoyakimu, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda. Adati,
3
“Konzani zishango ndi malihawo, yambanipo wa ku nkhondo.
4
Mangani akavalo, ndipo amene amakwerapo akwere. Khalani pa mzere mutavala zisoti zanu. Nolani mikondo yanu, valani malaya anu achitsulo.
5
Koma tsopano ndikuwona chiyani? Achita mantha, abwerera. Ankhondo ao agonjetsedwa. Akuthaŵa kaŵeraŵera, osacheukanso m'mbuyo. Agwidwa ndi mantha ponseponse,” akutero Chauta.
6
Waliŵiro sangathe kupulumuka. Ngakhale wankhondo wamphamvu sangathe kudzipulumutsa. Akunka naphunthwa, kumagwa kumpoto kwa mtsinje wa Yufurate.
7
“Kodi ndani akukwera ngati mtsinje wa Nailo, ngati mitsinje ya madzi achigumula?
8
Ejipito akukwera ngati mtsinje wa Nailo, ngati mitsinje ya madzi achigumula. Akuti, ‘Ndidzambatuka ndi kuliphimba dziko lapansi. Ndiwononga mizinda ndi anthu ake.’
9
Tiyeni inu akavalo, thamangani inu magaleta. Pitani patsogolo inu ankhondo, inu anthu a ku Etiopiya ndi a ku Puti, ogwira zishango, ndiponso inu anthu a ku Ludi, akatswiri pogwira uta.
10
Koma tsikulo ndi tsiku la Chauta Wamphamvuzonse, tsiku lolipsira, lolipsira adani ake. Lupanga lake lidzaŵaononga, lidzakhuta magazi, lidzachita kuledzera nawo. Ambuye Chauta Wamphamvuzonse akukonzera nsembe ku dziko lakumpoto, pafupi ndi mtsinje wa Yufurate.
11
Pita ku Giliyadi, ukatenge mankhwala, namwali iwe Ejipito. Wayesayesa mankhwala ambiri koma walephera, matenda akowo sadzachira.
12
Anthu a mitundu ina amva za manyazi ako, kulira kwako kwadzaza dziko lapansi. Ankhondo akunka nagwetsanagwetsana, onse pansi ndu kugwera limodzi.”
13
Naŵa mau amene Chauta adalankhula ndi mneneri Yeremiya za kubwera kwa Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, kudzathira nkhondo dziko la Ejipito:
14
“Mulengeze ku Ejipito, mulalike ku Migidoli, ku Memfisi ndi ku Tapanesi. Anthu akumeneko muŵauze kuti, ‘Imani pamalo panu, mukhale okonzeka chifukwa chakuti nkhondo idzaononga zonse pokuzungulirani.’
15
Chifukwa chiyani mulungu wanu Apisi wathaŵa? Chifukwa chiyani nkhunzi yanu yoipembedza ija sidalimbike? Nchifukwa choti Chauta waigwetsa.
16
Anthu ako akukhumudwa, akugwerana. Aliyense akunena kuti, ‘Nyamukani, tiyeni tizibwerera kwathu, kudziko kumene tidabadwira, tithaŵe lupanga la adani athuŵa!’
17
Farao, mfumu ya ku Ejipito, mpatseni dzina lakuti ‘Waphokoso, wotaya mwai wake.’
18
“Pali Ine ndemwe!” Ikutero Mfumu, imene dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse. Wina wamphamvu adzabwera wonga ngati Tabori phiri lopambana mapiri ena, wonga ngati phiri la Karimele, loti joo m'mbali mwa nyanja.
19
Konzani katundu wanu wopita naye ku ukapolo, inu anthu a ku Ejipito, pakuti Memfisi adzasanduka chipululu, ngati bwinja, mopanda anthu.
20
“Ejipito ali ngati mwanawang'ombe wokongola. Koma chimphanga chochokera kumpoto chidzamtera.
21
Ankhondo aganyu amene ali nawo, ali ngati anaang'ombe onenepa. Nawonso abwerera m'mbuyo nathaŵa pamodzi, palibe amene walimbikira. Ndithu, nthaŵi ya tsoka yaŵafikira, ndiyo nthaŵi yoŵalanga!
22
“Liwu la Ejipito likunga ngati la njoka yothaŵa, chifukwa choti adani ake abwera ndi zida zao, kubwera ndi nkhwangwa, ngati anthu odula mitengo.
23
Adzaduladi nkhalango ya ku Ejipito ngakhale njoŵirira, chifukwa anthuwo ndi ochuluka ngati dzombe, sangathe kuŵerengeka.
24
Anthu a ku Ejipito adzachitadi manyazi, adzatengedwa ukapolo ndi anthu akumpoto,” akutero Chauta.
25
Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, wanena kuti, “Ndidzalanga Amoni, mulungu wa Thebesi. Ndidzalanganso Farao ndi Ejipito pamodzi ndi milungu yake ndi akalonga ake. Ndidzalanga Farao ndi onse amene amamkhulupirira.
26
Ndidzaŵapereka kwa amene afuna kuŵaononga, ndiye kuti kwa Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, ndi atsogoleri ake a ankhondo. Komabe patapita nthaŵi, Ejipito adzakhalanso ndi anthu monga kale,” akutero Chauta.
27
“Koma iwe Yakobe, mtumiki wanga, usachite mantha, Iwe Israele, usataye mtima, chifukwa ndidzakupulumutsa kuchokera ku maiko akutali. Ndidzapulumutsanso zidzukulu zako kuchokera kumaiko kumene adapita nazo ku ukapolo. Yakobe adzabwerera, nadzapumula pabwino, ndi pa mtendere. Palibe winanso amene adzamuwopsa.”
28
Chauta akunena kuti, “Iwe Yakobe, mtumiki wanga, usachite mantha, pakuti Ine ndili nawe. Ndidzaonongeratu mitundu yonse ya anthu a kumaiko kumene ndidakupirikitsira. Koma iweyo sindidzakuwononga kotheratu ai. Kulanga ndidzakulanga monga m'mene kuyenera, sindingakulekelere osakulanga konse.”
← Chapter 45
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 47 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52