bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 7
Jeremiah 7
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 8 →
1
Chauta adauza Yeremiya mau aŵa akuti,
2
“Ima pa chipata cha Nyumba ya Chauta ndipo kumeneko ukalalike kuti: Imvani mau a Chauta, inu nonse anthu a ku Yuda, amene mumaloŵa pa chipata ichi kudzapembedza Chauta.
3
Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akukuuzani kuti, Konzani makhalidwe ndi zochita zanu, ndipo ndidzakulolani kumakhala pa malo ano.
4
Musamangodzinyenga ndi maganizo akuti muli pabwino ponena kuti, ‘Malo ano ndi Nyumba ya Chauta, Nyumba ya Chauta, Nyumba ya Chauta!’
5
“Konzani makhalidwe anu ndi zochita zanu. Muzichitirana zolungama.
6
Musazunze alendo kapena ana amasiye kapena akazi amasiye. Musaphe anthu osachimwa pa malo ano. Musamatsate milungu ina, kuti ingakuwonongeni.
7
Mukamvera mau anga, ndidzakulolani kuti mukhale pa malo ano, m'dziko limene ndidapatsa makolo anu mpaka muyaya.
8
“Koma onani, inu mumakhulupirira mabodza.
9
Mumaba, mumapha, mumachita zigololo, mumalumbira zonama, mumapereka nsembe zopsereza kwa Baala, mumatsata milungu ina imene kale simunkaidziŵa.
10
Pambuyo pake mumabwera kudzaima pamaso panga m'Nyumba ino, Nyumba imene imadziŵika ndi dzina langa. Mumanena kuti, ‘Tapulumuka ife,’ koma mumapitirirabe kumangochita zonyansa zonsezi.
11
Kodi tsopano Nyumba ino, Nyumba imene imadziŵika ndi dzina langayi, yasanduka phanga lobisalamo mbala zachifwamba, inu mukuwonerera? Mwiniwakene ndaziwona zonsezi,” akuterotu Chauta.
12
“Pitani ku malo anga ku Silo, malo amene poyamba ankadziŵika ndi dzina langa. Mukaone zimene ndidachita kumeneko chifukwa cha kuipa kwa anthu anga Aisraele.
13
Munkachita zoipa zonsezi, mudakana kundimvera nditakulankhulani kosalekeza, ndipo simudayankhe pamene ndidakuitanani.
14
Nchifukwa chake zomwe ndidachita ku Silo, ndidzachitanso ku Nyumba ino, imene imadziŵika ndi dzina langa, malo amene inu mumaŵakhulupirira, malo amene ndidakupatsani inu pamodzi ndi makolo anu.
15
Ndidzakuchotsani pamaso panga monga momwe ndidachotsera abale anu onse, zidzukulu zonse za Efuremu.
16
“Iwe Yeremiya, usaŵapempherere anthu ameneŵa. Usaŵapepesere kwa Ine kapena kuŵadandaulira mondiwumiriza chifukwa Ine sindikumvera.
17
Kodi sukuwona zimene zikuchitika m'mizinda ya ku Yuda ndi m'miseu ya m'Yerusalemu?
18
Ana akutolera nkhuni, atate akusonkha moto, akazi akukanda ufa kuti aphike makeke, kuchitira ulemu amene amati ndi mfumukazi yakumwamba. Iwowo amathira nsembe yazakumwa kwa milungu ina, kuti andipsetse mtima.
19
Amati atani! Amayesa kuti akuvuta Ine, koma akungodzivuta okha ndi kumadzichititsa manyazi.
20
Nchifukwa chake ndidzaŵalanga koopsa mwaukali. Mkwiyo wanga udzagwera Nyumba yangayi, anthu, nyama, mitengo ndi mbeu zomwe. Mkwiyowo udzayaka ngati moto wosazimika.”
21
Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, “Muwonjeze zopereka zanu zopsereza pa nsembe zanu zinazo, ndipo mudye nyama yake.
22
Pamene ndidatulutsa makolo anu ku dziko la Ejipito, sindidaŵalamule kuti azipereka nsembe zopsereza kapena nsembe zina.
23
Koma chimene ndidaalamula nchimodzi, ndidati, ‘Mukamandimvera, ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga. Muzitsata malamulo anga onse kuti zinthu zikukomereni!’
24
Koma anthuwo sadamvere, sadasamaleko, ndipo adapitirira kukhala osamvera ndi mitima yao yoipa. Adayang'ana zam'mbuyo osati zakutsogolo.
25
Kuyambira tsiku limene makolo anu adatuluka ku dziko la Ejipito mpaka lero lino, ndakhala ndikukutumizirani atumiki anga aneneri kaŵirikaŵiri.
26
Komabe inu simudandimvere, simudasamaleko. Ndi mitima yanu yokanika, mwaipa kupambana makolo anu.
27
“Iwe ungaŵauze zimenezi, sadzakumvera. Ungaŵaitane, sadzakuyankha.
28
Nchifukwa chake udzaŵauze kuti, ‘Uwu ndi mtundu wa anthu uja sadamvere mau a Chauta Mulungu wao, ndipo sadafune kukonzeka. Mau oona atheratu ndipo pakamwa pamangonena zonama zokhazokha.’
29
“Meta tsitsi lako, ndipo ulitaye. Ulire kwambiri pa zitunda zopanda zomera, poti Chauta waukana mbadwo uwu umene wamkwiyitsa. Anthu amenewo Iye waŵasiyadi.”
30
Chauta akuti, “Anthu a ku Yuda achita zoipa Ine ndikuwona. Aimika mafano ao onyansa m'Nyumba ino imene imadziŵika ndi dzina langa, ndipo aiipitsa.
31
Amanga nsanja yotchedwa Tofeti m'chigwa cha Benihinomu, kuti atenthereko ana ao aamuna ndi aakazi. Zimenezo sindidalamule konse, ngakhale kuziganiza komwe.
32
Nchifukwa chake nthaŵi ikubwera pamene malo ano sadzatchedwanso Tofeti, kapena za Chigwa cha Benihinomu, koma za Chigwa cha Chipheiphe, pakuti anthu akufa adzaŵaika ku Tofeti, chifukwa choti sikudzapezekanso malo owaika.
33
Tsono mitembo ya anthu ameneŵa idzakhala chakudya cha mbalame zamumlengalenga ndi zilombo zakuthengo. Ndipo palibe wina amene adzazipirikitse.
34
Sikudzamvekanso mau achisangalalo ndi achimwemwe ku mizinda ya ku Yuda ndi ku miseu ya mu Yerusalemu. Sikudzamvekanso mau achikondwerero, a mkwati wamwamuna ndi wamkazi. Ndithudi dzikolo lidzasanduka chipululu.”
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52