bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 9
Jeremiah 9
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 10 →
1
Ndikadakonda kuti mutu wanga ukhale ngati chitsime cha madzi, kuti maso anga akhale ngati kasupe wa misozi, kuti ndilire usana ndi usiku, kulirira onse amene adafa a mtundu wa anthu anga?
2
Ndani adzandipatse pogona m'chipululu, kuti ndiŵasiye anthu anga ndi kuŵathaŵa. Paja onsewo ngachigololo, ndiponso ndi gulu la anthu onyenga.
3
Amapinda lilime ngati uta. Dziko ladzaza ndi zabodza osati zoona. “Amanka naonjezeraonjezera zoipa, ndipo sandidziŵa Ine,” akuterotu Chauta.
4
“Aliyense achenjere ndi mnzake, asakhulupirire ngakhale mbale wake. Zoona, aliyense amafuna kulanda malo a mbale wake. Aliyense amachitira mnzake ugogodi.
5
Aliyense amanyenga mnzake, ndipo sanena zoona. Pakamwa pao adapazoloŵeza kulankhula zonama. Amakonda zoipa kwambiri, kotero kuti sangathenso kulapa.
6
Amasanjikiza tchimo pa tchimo linzake, chinyengo pa chinyengo chinzake. Amakana kundidziŵa,” akuterotu Chauta.
7
Nchifukwa chake Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ndithu, anthu angaŵa ndidzaŵasungunula ngati chitsulo, ndipo ndidzaŵayesa. Iwowo ndi ochimwa, ndingathe bwanji kuŵalekerera?
8
Lilime lao lili ngati muvi wakuthwa. Aliyense pakamwa pake pamatuluka mau aubwenzi, m'menemo mumtima mwake akukonzekera zomchita mnzake chiwembu.
9
Kodi zimenezi ndipanda kuŵalanga nazo? Monga ndisaulipsire mtundu wotere wa anthu?” Akutero Chauta
10
Ine ndidati, “Ndidzamva chisoni ndi kulira mokweza chifukwa cha mapiri. Ndidzadandaula chifukwa cha mabusa am'chipululu popeza kuti malo onsewo aonongeka. Palibe amene amapitako, sikumveka nkulira kwa ng'ombe komwe. Mbalame zonse zouluka ndiponso nyama zakuthengo zathaŵa, osaonekanso.”
11
Apo Chauta adati, “Yerusalemu ndidzamsandutsa bwinja, ndidzamusandutsa mokhala nkhandwe. Mizinda ya ku Yuda idzasiyidwa, simudzakhala anthu.”
12
Ine ndidati, “Kodi wanzeru ndani, amene angamvetse zimenezi? Chauta adazifotokozera yani, kuti iyeyo akafotokozere ena? Nanga chifukwa chiyani dziko laonongeka ndi kusanduka chipululu, m'mene anthu sapitamo?”
13
Apo Chauta adayankha kuti, “Nchifukwa chakuti anthu angawo sadatsate malamulo amene ndidaŵapatsa, ndipo sadamvere mau anga ndi kuŵasamala.
14
Koma ankangotsata zolakwa za mitima yao yokanika. Ankapembedza Abaala monga momwe makolo ao adaŵaphunzitsira.
15
Tamvani tsono zimene Ine Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, ndidzachite. Anthu ameneŵa ndidzaŵadyetsa ziphe ndi kuŵamwetsa madzi azumu.
16
Ndidzaŵabalalitsa pakati pa mitundu ya anthu imene iwowo kapena makolo ao sadaidziŵe. Ndidzaŵalondola ndi ankhondo mpaka kuŵatheratu onse.”
17
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Muziganize bwino, muitane akazi olira maliro kuti abwere. Akaziwo akhale aja amadziŵa kwambiri kuliraŵa.”
18
Anthu akuti, “Abwere mofulumira adzatilire kuti m'maso mwathu mudze misozi nsidze zathu zinyowe.”
19
Kukumveka kulira kwa Ziyoni, akuti, “Kalanga ife! Taonongeka! Manyazi aakulu atigwera. Tiyenera kusiya dziko lathu, chifukwa nyumba zathu azigwetsa.”
20
Ine ndidati, “Inu azimai, mverani mau a Chauta. Tcherani makutu kuti mumve zimene akunena. Ana anu aakazi muŵaphunzitse kulira. Aliyense aphunzitse mnzake nyimbo yamaliro.
21
Imfa yatifikira kudzera m'mawindo, yaloŵa ngakhale m'nyumba zathu zaufumu. Idapha ana athu m'miseu, ndipo idatha anyamata m'mabwalo.”
22
Chauta adandiwuza kuti ndinene izi: “Mitembo ya anthu idzagwa, kuchita kuti mbwembwembwe ngati ndoŵe m'minda, ngati mitolo pambuyo pa anthu ovuna. Koma palibe amene adzaitole.”
23
Chauta akunena kuti, “Munthu wanzeru asanyadire nzeru zake, munthu wamphamvu asanyadire mphamvu zake, ndipo munthu wolemera asanyadire chuma chake.
24
Koma ngati wina afuna kunyadira, anyadire ichi chakuti amamvetsa za Ine, ndipo amandidziŵa. Amadziŵa kuti Ine ndine Chauta wokonda chifundo, chilungamo, ndi ungwiro pa dziko lapansi. Ndithudi, pazimenezi ndipo pali mtima wanga.”
25
Chauta akunena kuti, “Nthaŵi ikubwera pamene ndidzalanga onse oumbalidwa, amene mu mtima sasamalako.
26
Ndidzalanga Aejipito, Ayuda, Aedomu, Aamoni, Amowabu ndiponso onse amene amakhala m'chipululu namameta cham'mbali. Mitundu ina yonseyi njosaumbalidwa, ngakhale banja lonse la Israele nalonso nlosaumbalidwa mu mtima.”
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52