bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 41
Jeremiah 41
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 40
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 42 →
1
Pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri, Ismaele mwana wa Netaniya, mdzukulu wa Elisama, wa m'banja la mfumu, mmodzi mwa atsogoleri akuluakulu a mfumu, adafika ndi anthu khumi ku Mizipa kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu. Pamene ankadya naye kumeneko,
2
Ismaele, mwana wa Netaniya, pamodzi ndi anthu khumi aja, adadzambatuka napha Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani. Adamupha ndi malupanga ao munthu amene mfumu ya ku Babiloni idaamuika kuti akhale bwanamkubwa wa dziko.
3
Ismaele adaphanso Ayuda onse amene anali ku Mizipa ndiponso ankhondo a Ababiloni amene anali kumeneko.
4
M'maŵa mwake, anthu asanadziŵe kuti Gedaliya waphedwa,
5
kudafika anthu makumi asanu ndi atatu kuchokera ku Sekemu, ku Silo ndi ku Samariya. Ndevu zao adaameta, zovala zao zinali zong'ambikang'ambika, ndipo matupi ao anali otemekatemeka. Adatenga nsembe zaufa ndi lubani, kukapereka ku Nyumba ya Chauta.
6
Tsono Ismaele, mwana wa Netaniya, adabwera akulira kuchokera ku Mizipa kudzakumana nawo. Atakumana nawo, adati, “Bwerani, mudzaonane ndi Gedaliya mwana wa Ahikamu.”
7
Atangofika pakati pa mudzi, Ismaele mwana wa Netaniya ndi anthu ake, adaŵapha onsewo naŵataya m'chitsime.
8
Koma pa gulu limenelo panali anthu khumi amene adaauza Ismaele kuti, “Ifeyo musatiphe, tili ndi tirigu, barele, mafuta, ndi uchi, zimene tidabisa m'minda.” Motero adaŵaleka osaŵaphera kumodzi ndi anzao aja.
9
Chitsime chimene Ismaele adatayamo anthu amene adaŵapha aja chinali chitsime chachikulu chija chimene adaakumba ndi mfumu Asa, ataopsedwa ndi Basa mfumu ya ku Israele. Ismaele, mwana wa Netaniya adachidzaza ndi mitembo.
10
Pambuyo pake Ismaele adaŵatenga ukapolo anthu onse amene adatsala ku Mizipa. Anthuwo ndi aŵa: ana aakazi a mfumu, ndi onse otsala ku Mizipa, amene Nebuzaradani mtsogoleri wa nkhondo adaŵapatsa Gedaliya mwana wa Ahikamu kuti akhale bwanamkubwa wao. Ndipo anthu ameneŵa adachoka nawo ndi cholinga choti akaloŵe nawo m'dziko la Aamoni.
11
Pamene Yohanani, mwana wa Kareya, ndi atsogoleri a ankhondo, adamva zoipa zimene Ismaele mwana wa Netaniya adaachita,
12
adasonkhanitsa anthu onse amene anali nawo, napita kukamenyana naye nkhondo. Adakampeza ku chidziŵe cha ku Gibiyoni.
13
Ndipo anthu onse amene Ismaele adaaŵagwira ataona Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri a magulu ankhondo aja, adasangalala.
14
Anthu onse amene Ismaele adaaŵatenga ukapolo kuchoka nawo ku Mizipa, adabwerera napita kwa Yohanani mwana wa Kareya.
15
Koma Ismaele mwana wa Netaniya, pamodzi ndi anthu ake asanu ndi atatu, adathaŵa Yohanani, kuthaŵira kwa Aamoni.
16
Pamenepo Yohanani mwana wa Kareya pamodzi ndi atsogoleri a magulu ankhondo, adatenga otsala a ku Mizipa amene Ismaele mwana wa Netaniya, adaaŵatenga ukapolo, atapha Gedaliya mwana wa Ahikamu. Amene adaŵatengawo anali ankhondo, akazi, ana ndi otumikira bwalo la mfumu, amene Yohanani adaabwera nawo kuchokera ku Gibiyoni.
17
Adanyamuka ulendo wao nakaima ku Geruti-Kimuhamu, pafupi ndi Betelehemu. Ankafuna kupita ku Ejipito,
18
chifukwa choopa Ababiloni. Anali ndi manthadi chifukwa choti Ismaele mwana wa Netaniya, adaapha Gedaliya, mwana wa Ahikamu, amene mfumu ya ku Babiloni idaamuika kuti akhale bwanamkubwa wa dziko.
← Chapter 40
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 42 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52