bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 36
Jeremiah 36
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 35
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 37 →
1
Chaka chachinai cha ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya ku Yuda, Chauta adauza Yeremiya kuti,
2
“Tenga buku ndipo ulembepo mau onse amene ndalankhula nawe za Israele ndi Yuda ndi za mitundu yonse ya anthu, kuyambira tsiku limene ndidalankhula nawe nthaŵi ya Yosiya mpaka lero lino.
3
Mwina mwake banja la Yuda lidzamva za zoopsa zonse zimene ndikuti ndiŵagwetsere. Choncho munthu aliyense adzasiya makhalidwe ake oipa. Motero ndidzaŵakhululukira zolakwa zao ndi machimo ao.”
4
Tsono Yeremiya adaitana Baruki mwana wa Neriya. Ndipo Barukiyo adalemba m'bukumo mau onse amene Yeremiya ankamuuza, ndiye kuti mau onse amene Chauta adalankhula ndi Yeremiyayo.
5
Adauza Baruki kuti, “Ine andiletsa kupita ku Nyumba ya Chauta.
6
Ndiye tsono upite ndiwe kumeneko m'malo mwanga pa tsiku losala chakudya, ukaŵerenge mau a Chauta amene ndidakulembetsa m'bukumu, anthu onse alikumva. Udzaŵaŵerenge kwa anthu onse a ku Yuda amene abwera kuchokera ku mizinda yao.
7
Tsono mwina mwake adzapemba kwa Chauta, ndipo munthu aliyense adzasiya makhalidwe ake oipa. Ndithu Chauta waŵakwiyira anthu ameneŵa, ukali wake ndi woyaka kwabasi.”
8
Motero Baruki mwana wa Neriya adachita zonse zimene mneneri Yeremiya adamuuza kuti achite. Adaŵerenga mau a Chauta olembedwa m'buku aja m'Nyumba ya Chauta.
9
Pa mwezi wachisanu ndi chinai wa chaka chachisanu cha ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, anthu onse a ku Yerusalemu ndi onse amene adaabwera kumeneko kuchokera ku mizinda ya Yuda, adapangana za kusala chakudya kuti apepese Chauta.
10
Tsono onse ataloŵa m'Nyumba ya Chauta, Baruki adaŵerenga mau a Chauta olembedwa m'buku aja, anthu onse alikumva. Adaŵerengera m'chipinda cha Gemariya, mwana wa mlembi Safani, chimene chinali m'bwalo lapamwamba, pafupi ndi Chipata Chatsopano choloŵera ku Nyumba ya Chauta.
11
Mikaya mwana wa Gemariya, mdzukulu wa Safani, atamva mau onse a Chauta olembedwa m'buku aja,
12
adapita ku nyumba ya mfumu, nakaloŵa m'chipinda cha mlembi. Akuluakulu onse anali atasonkhana m'menemo: mlembi Elisama, Delaya mwana wa Semaya, Elinatani mwana wa Akobori, Gemariya mwana wa Safani, Zedekiya mwana wa Hananiya, pamodzi ndi akuluakulu ena onse.
13
Tsono Mikaya adaŵauza mau onse amene adamva pamene Baruki ankaŵerenga buku anthu alikumva.
14
Pamenepo akuluakulu adatuma Yehudi mwana wa Netaniya, mwana wa Selemiya, mwana wa Kusi, kwa Baruki kukamuuza kuti abwere nalo buku limene ankaŵerengera anthu. Motero Baruki mwana wa Neriya, adapita nalo bukulo kwa iwo.
15
Iwowo adati, “Khala apa, ndipo utiŵerengere.” Baruki adaŵaŵerengeradi.
16
Atamva zimene adaaŵerengazo, adayamba kuyang'anitsitsana ali njenjenje ndi mantha. Tsono adauza Baruki kuti, “Tiyenera kuŵauza amfumu mau onseŵa.
17
Koma tatiwuza, m'mene udalembera mau onseŵa. Kodi ndi Yeremiya adakulembetsa zimenezitu ati?”
18
Baruki adayankha kuti, “Inde, ndi Yeremiyadi amene ankanditchulira mau ameneŵa, ine nkumalemba ndi inki m'buku.”
19
Akuluakulu aja adauza Baruki kuti, “Iweyo ndi Yeremiyayo mukabisale, pasakhale munthu wodziŵa kumene muli.”
20
Tsono iwo adaloŵa m'bwalo napita kwa mfumu ataika bukulo m'chipinda cha mlembi Elisama. Adaiwuza mfumuyo mau onsewo.
21
Mfumu itamva zimenezi, idatuma Yehudi kukatenga buku lija. Atakalitenga ku chipinda cha mlembi Elisama, Yehudi adaŵerengera mfumu ndi akuluakulu onse amene adasonkhana.
22
Unali mwezi wachisanu ndi chinai ndipo mfumu inali m'nyumba ya pa nyengo yachisanu, ikuwotha moto umene ankasonkha chifukwa cha kuzizira.
23
Yehudi ankati akaŵerenga masamba atatu kapena anai a bukulo, mfumu inkaŵagwira nkuŵadula ndi mpeni, niŵaponya m'malaŵi a moto. Idapitirira kuchita zimenezi mpaka buku lonse lidapsa ndi moto.
24
Komabe mfumu kapena wina aliyense mwa aphungu ake amene adamva mau ameneŵa, sadachite mantha kapena kung'amba zovala zao.
25
Ndipo pamene Elinatani, Delaya ndi Gemariya adapempha mfumu kuti isatenthe bukulo, iyoyo sidaŵamvere.
26
Kenaka mfumu idalamula Yerahamele mwana wa mfumu, Seraya mwana wa Aziriele ndi Selemiya mwana wa Abideele kuti akagwire mlembi Baruki ndi mneneri Yeremiya. Koma Chauta anali ataŵabisa.
27
Tsono mfumu itatentha bukulo m'mene munali zonse zimene Yeremiya adaalembetsa Baruki, Chauta adauza Yeremiya kuti,
28
“Tsopano tenga buku lina kuti ulembemo mau onse amene adaali m'buku loyamba, limene Yehoyakimu, mfumu ya ku Yuda, adatentha.
29
Ndipo za Yehoyakimu, mfumu ya ku Yuda, ukamuuze kuti, ‘Chauta akuti, Paja iwe udatentha buku lija, nkumanena kuti, “Chifukwa chiyani walemba kuti mfumu ya ku Babiloni idzafika kudzaononga dziko lino ndi kuwononga anthu ndi nyama zomwe?”
30
Nchifukwa chake za Yehoyakimu, mfumu ya ku Yuda, Chauta akunena kuti sipadzaoneka wina woloŵa m'malo mwake pa mpando waufumu wa Davide. Akadzafa, mtembo wake masana udzakhala pa dzuŵa, ndipo usiku udzakhala pa chisanu.
31
Ndidzamlanga pamodzi ndi zidzukulu zake ndi aphungu ake chifukwa cha zoipa zao. Ndidzaŵagwetsera iwowo ndi anthu onse a ku Yerusalemu ndi a ku Yuda zoopsa zonse zimene ndidanena, chifukwa iwo sadamvere mau anga.’ ”
32
Tsono Yeremiya adatenga buku lina napatsa mlembi Baruki, mwana wa Neriya, namlembetsa mau onse a m'buku limene Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda adatentha lija. Ndipo adaonjezerapo mau ambiri monga omwewo.
← Chapter 35
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 37 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52