bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 2
Jeremiah 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 3 →
1
Chauta adandiwuza kuti
2
ndikalengeze kwa anthu a ku Yerusalemu mau ake akuti, “Ndikukumbukira m'mene munkakhulupirikira pa unyamata wanu, m'mene poyamba paja munkandikondera monga amachitira mkwati wamkazi. Mudanditsata m'chipululu, m'dziko losabzalamo kanthu.
3
Iwe Israele udaali wopatulika wa Chauta. Udaali ngati chipatso chake choundukula. Ndidaika zoŵaŵa ndi mavuto aakulu, pa onse amene adakuzunza, ndipo tsoka linkaŵagwera,” akutero Chauta.
4
Inu zidzukulu za Yakobe, mabanja onse a Israele, mverani mau a Chauta.
5
Iye akukufunsani kuti, “Kodi makolo anu adandipeza ncholakwa chanji kuti andithaŵe? Adatsata milungu yachabechabe, iwonso nkusanduka achabechabe.
6
Sadalabadeko za Ine Chauta, ngakhale ndine amene ndidaŵatulutsa m'dziko la Aejipito, ndi kuŵatsogolera m'chipululu, m'dziko louma ndi lokumbikakumbika, m'dziko lachilala ndi la mdima wandiweyani, m'dziko limene munthu sadutsamo, kumene sikukhala munthu konse.
7
Ndidakufikitsani ku dziko lachonde kuti mudye zipatso zake ndi zabwino zake zina. Koma mutangoloŵa m'dzikolo, mudaliipitsa, dziko limene ndidakupatsani mudalisandutsa lonyansa.
8
Nawonso ansembe sadafunse kuti, ‘Chauta ali kuti?’ Akatswiri a malamulo sadandidziŵe. Olamulira adandipandukira. Aneneri ankalosa m'dzina la Baala, ndipo ankatsata milungu yachabechabe.
9
“Tsono ndidzakuimbanibe mlandu,” akuterotu Chauta. “Ndidzaimbanso mlandu zidzukulu zanu.
10
Pitani chakuzambwe, ku chilumba cha Kitimu, mukaone, tumani anthu chakuvuma, ku Kedara, akafufuze. Mudzaona kuti zoterezi sizidachitikepo nkale lonse.
11
Kodi ulipo mtundu wa anthu uliwonse umene udasinthapo milungu yake, ngakhale kuti si milungu konse? Komabe anthu anga asinthitsa Mulungu wao waulemerero ndi milungu yachabechabe.
12
Inu maiko akumwamba, dabwa nazoni zimenezi, njenjemerani ndi mantha, akuterotu Chauta.
13
Anthu anga achita machimo aŵiri: andisiya Ine kasupe wa madzi opatsa moyo, adzikumbira okha zitsime, zitsime zake zong'aluka, zosatha kusunga madzi.
14
“Israele si kapolotu ai, sadabadwire mu ukapolo. Nanga chifukwa chiyani amuwononga chotere?
15
Anthu a mitundu ina ambangulira ndi kumuwopsa ngati mikango. Dziko lake alisandutsa chipululu. Mizinda yake adaiwononga, idasanduka mabwinja.
16
Aejipito a ku Memfisi ndi a ku Tapanesi akuphwanyani mitu.
17
Zimenezi zakuwonekerani chifukwa mudasiya Chauta, Mulungu wanu, pamene Iye adakuikani pa njira yabwino.
18
Nanga tsopano mudzapindulanji mukadzapita ku Ejipito, kukamwa madzi a m'Nailo? Mudzapeza phindu lanji mukadzapita ku Asiriya kukamwa madzi a mu mtsinje wa Yufurate?
19
Mudzalangidwa ndi machimo anu omwe: poti mwandikana, ndidzakuimbani mlandu. Muganizire bwino za kuipa kwake kwa kundisiya Ine, Chauta, Mulungu wanu. Mulingalire kuŵaŵa kwake kwa kukhala osandiwopa,” akuterotu Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse.
20
“Kuyambira masiku amakedzana inu mudathyola goli lanu ndi kudula nsinga zanu. Mudati, ‘Sitidzakutumikirani!’ Ndithu inu mwakhala ngati mkazi wadama, mukupembedza milungu ina pochita zadama pa phiri lililonse ndiponso pansi pa mtengo wogudira uliwonse.
21
Komabe ndidaakuwoka iwe Israele ngati mtengo wa mphesa wosankhidwa, udaali mpesa wabwino kwambiri. Nanga wasanduka bwanji mpesa wachabechabe, wonga wakutchire?
22
Ngakhale usambire soda, ngakhale usambire sopo wambiri, kuthimbirira kwa tchimo lako kumaonekabe pamaso panga,” akuterotu Ambuye Chauta.
23
“Uneneranji kuti, ‘Ine sindidadziipitse, sindidatsate Baala?’ Kumbukira m'mene udachimwira m'chigwamo, zindikira zimene wachita. Wakhala ngati ngamira yaikazi, yothamanga uku ndi uku.
24
Wakhala ngati mbidzi yaikazi yozoloŵera m'chipululu, yonka nipunika pa nthaŵi yake yachisika. Kodi angailetse chilakolako chakecho ndani? Mphongo iliyonse yoikhumba sidzavutika, idzaipeza pa nthaŵi yakeyo.
25
Iwe Israele, lekatu, nsapato zingakuthere ku phazi, kukhosi kwako kungaume ndi ludzu potsatira milungu ina. Koma iwe ukuti, ‘Ai toto, sindingathe kuchitira mwina, ndimakonda milungu yachilendoyi, sindingaleke kuitsata.’
26
“Banja la Israele lidzachita manyazi, monga momwe mbala imachitira manyazi akaigwira. Aisraele, mafumu ao ndi akalonga ao, ansembe ao ndi aneneri ao, onsewo adzachita manyazi.
27
Amauza mtengo kuti ‘Iwe ndiwe bambo wathu,’ amauza mwala kuti ‘Iwe ndiwe amene udatibala.’ Koma Ine amandifulatira, m'malo motembenukira kwa Ine. Tsono akakhala pa mavuto amati, ‘Dzambatukani, mutithandize.’
28
Nanga milungu yanu ili kuti, milungu ija mudadzipangira ija? Idzambatuketu, ngati ingathe kukupulumutsani pa nthaŵi yanu ya mavuto. Inu anthu a ku Yuda, milungu yanu ndi yambiri, kuchuluka kwake monga momwe iliri mizinda yanu.”
29
Chauta akuti, “Kodi mukundiimbiranji mlandu? Nonsenu mwandipandukira.
30
Ndidalanga ana anu popanda phindu, sadaphunzirepo nkanthu komwe. Monga mkango wolusa mudapha aneneri anu ndi lupanga.”
31
Inu anthu amakono, imvani mau a Chauta. “Kodi ndakhala ngati chipululu kwa Israele, kapena ngati dziko la mdima wandiweyani? Chifukwa chiyani tsono anthu anga akunena kuti, ‘Ndife mfulu, sitidzabweranso kwa Inu?’
32
Kodi namwali amaiŵala zokongoletsera zake, kapena mkwati kuiŵala zovala zake zaukwati? Komabe anthu anga andiiŵala Ine masiku osaŵerengeka.
33
“Mumadziŵa bwino njira zopezera zibwenzi zam'seri. Ngakhale akazi oipa kwambiri omwe mumaŵaphunzitsa ndinu.
34
Zovala zanu zili psu ndi magazi a anthu osauka osachimwa. Anthuwo simudaŵapeze nathyola nyumba. Komabe, ngakhale zinthu zili choncho,
35
inu mukunena kuti, ‘Ndife osalakwa, mkwiyo wa Chauta wapola tsopano!’ Ine ndidzakuimbanibe mlandu chifukwa chonena kuti simudachimwe.
36
Bwanji mukudzipeputsa nokha posinthasintha njira zanu! Ejipito adzakugwiritsani mwala monga muja adakuchititsirani manyazi Aasiriya.
37
Mudzatuluka kumeneko aliyense atagwirira manja ku mutu. Ine Chauta ndidaŵakana amene inu mumagonerapo, ndipo anthuwo sadzakuthandizani mpang'ono pomwe.”
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52