bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 6
Jeremiah 6
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 7 →
1
Inu anthu a ku Benjamini thaŵani, tulukanimo m'Yerusalemu. Lizani lipenga ku Tekowa, kwezani mbendera ku Betehakeremu. Tsoka likudzakugwerani kuchokera kumpoto, ndipotu nchiwonongeko chachikulu.
2
Ndidzauwononga mzinda wa Ziyoni, mzinda wooneka bwino ndi wokongola.
3
Mafumu adzabwera ndi asilikali ao. Adzamanga zithando momzinga Yerusalemu, ndipo aliyense adzakhazika anthu ake pamalo pake.
4
Adzanena kuti, “Konzekani kuti muuthire nkhondo mzindawu. Bwerani tiwuthire nkhondo masana ano.” “Koma tili ndi tsoka, dzuŵa lapendeka, zithunzithunzi zakumadzulo zikunka zitalika.”
5
“Bwerani tsono tiwuthire nkhondo usiku uno, tiwononge malinga ake.”
6
Mau a Chauta Wamphamvuzonse akuti, “Gwetsani mitengo ya mu Yerusalemu, ndipo mzindawu muumangire nthumbira zankhondo. Mzinda umenewu ndi woyenera kulangidwa, anthu ake amangokhalira kuzunzana.
7
Monga momwe chitsime chimasungira madzi ake, ndimonso m'mene mzindawo umasungira zoipa zake. Zimene mukumva ndi za chiwonongeko ndi za nkhondo. Ndikuwonamonso matenda ndi zilonda.
8
Iwe Yerusalemu, tengapo phunziro, kuwopa kuti chikondi changa pa iwe chingathe, ndipo ndingakusandutse dziko lachipululu, dziko lopanda anthu.”
9
Mau a Chauta Wamphamvuzonse akuti, “Akunkheni ndi kuŵalanda zonse anthu otsala a Aisraele, monga momwe anthu amachitira, populula mphesa ku nthambi zake.”
10
Kodi ndilankhule ndi yani, ndipo ndichenjeze yani, kuti amve? Makutu ao ndi otsekeka, sangathe kumva. Mau a Chauta amaŵanyoza kwambiri, saŵalabadira konse.
11
Nchifukwa chake ndadzazidwa ndi mkwiyo wa Chauta, sindingathenso kudzimanga kuti usatulukire kunja. Chauta akuti, “Mkwiyo umenewu ukauthire pa ana oyenda mu mseu, ndi pa achinyamata kumene amasonkhanira. Mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa, ngakhale aimvi ndi okalamba kwambiri.
12
Nyumba zao zidzapatsidwa kwa ena pamodzi ndi minda yao ndi akazi ao omwe. Ndithuditu, ndi dzanja langali ndidzakantha anthu okhala m'dzikomo.
13
“Pakuti onse, ang'onoang'ono ndi akuluakulu omwe, ali ndi khwinthi la phindu lopeza mwakuba. Aneneri pamodzi ndi ansembe ao, onsewo ndi onyenga.
14
Iwo amapoletsa mabala a anthu anga pamwamba pokha. Amangonena kuti, ‘Kuli mtendere, kuli mtendere,’ chonsecho kulibe konse mtendere.
15
Kodi akamachita zonyansa, amachita manyazi ngati? Iyai, sachita manyazi mpang'ono pomwe. Sadziŵa nkugwetsa nkhope komwe. Nchifukwa chake adzagwera pakati pa anzao amene adagwa kale. Adzagweratu pa tsiku limene ndidzaŵalanga!” Akutero Chauta.
16
Mau a Chauta ndi aŵa, “Imani pa mphambano, ndipo mupenye. Mufunse kumene kuli njira zakale ndi kumene kuli njira yabwino. Tsono mutsate njira yabwinoyo, ndipo mudzakhala pa mtendere. Koma inuyo mudati, ‘Sitidzaitsata.’
17
Chauta adakupatsani alonda oti akutsogolereni nati, ‘Imvani kulira kwa lipenga lokuchenjezani.’ Koma inu mudati, ‘Sitidzasamalako.’
18
Nchifukwa chake imvani inu anthu a mitundu ina, penyetsetsani, inu mwasonkhana panonu, zimene zidzaŵagwere anthuwo.
19
Tamvani inu okhala pa dziko lapansi, anthuwo ndidzaŵaononga. Komatu zimenezo nzotsatira za kunyenga kwao, chifukwa sadamvere mau anga ndipo sadamvere malamulo anga.
20
Kodi pali phindu lanji kwa Ine, ngakhale abwere ndi lubani kuchokera ku Sheba, kapena zonunkhira zina kuchokera ku maiko akutali? Sindidzalandira zopereka zao zopsereza, nsembe zao sizindikondwetsa.
21
Nchifukwa chake anthu ameneŵa ndidzaŵaikira zoŵakhumudwitsa. Atate ndi ana ao aamuna, anansi ndi abwenzi ao, onsewo adzaonongeka.”
22
Chauta akunena kuti, “Onani, anthu a mtundu wina akubwera kuchokera ku dziko lakumpoto. Mtundu wa anthu amphamvu wanyamuka kuchokera mbali zakutalitali za dziko lapansi.
23
Atenga mauta ndi mikondo, ndi anthutu ankhalwe ndi opanda chifundo. Phokoso lao lili ngati mkokomo wa nyanja. Akwera pa akavalo, akonzekera ngati munthu wankhondo, akudzamenyana nawe, iwe Ziyoni.”
24
A ku Yerusalemu akuti, “Mbiri ya iwowo taimva, m'nkhongono mwati zii. Nkhaŵa yatigwira, ndipo tikumva ululu wonga wa mkazi panthaŵi yake yochira.”
25
Musayesere kupita ku minda, kapena kuyenda pa mseu, pakuti adani akubwera ndi nkhondo ndipo ponseponse pali mantha okhaokha.
26
Inu anthu anga, valani ziguduli, gubuduzikani pa phulusa. Lirani kwamphamvu, ngati munthu wolira mwana wake mmodzi yekha, pakuti mwadzidzidzi woononga adzabwera kudzakuphani.
27
“Iwe Yeremiya, ndakusankha kuti ukhale choyesera zitsulo. Uŵayese anthu anga kuti uwone m'mene aliri makhalidwe ao.
28
Onsewo ali ndi upandu wokanika, onsewo ndi akazitape, ndi olimba ngati mkuŵa ndi chitsulo. Onse amangochita zoipa zokhazokha.
29
Mvukuto zikuuzira kwambiri, mtovu wasungunuka ndi moto. Koma ntchito yosungunulayo sikupindula, chifukwa choti dothi loipa silikuchokapo.
30
Iwo ali ngati siliva wotaya, pakuti Chauta waŵakana.”
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52