bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 37
Jeremiah 37
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 36
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 38 →
1
Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adakhazika Zedekiya pa mpando waufumu wa ku Yuda, kuloŵa m'malo mwa Yehoyakini mwana wa Yehoyakimu.
2
Koma Zedekiyayo ndi aphungu ake, pamodzi ndi anthu onse a m'dzikomo, sadamvere mau amene Chauta adalankhula kudzera mwa mneneri Yeremiya.
3
Tsono mfumu Zedekiya adatuma Yehukala, mwana wa Semaliya ndi wansembe Zefaniya, mwana wa Maseiya, kwa mneneri Yeremiya kukamuuza kuti, “Mutipempherere kwa Chauta, Mulungu wathu.”
4
Pa nthaŵi imeneyo nkuti Yeremiya asanaponyedwe m'ndende, choncho anali ndi ufulu wotha kuyenda pakati pa anthu.
5
M'menemonso nkuti gulu lankhondo la Farao litatuluka ku Ejipito. Ndipo pamene Ababiloni ozinga mzinda wa Yerusalemu ndi zithando zankhondo adamva zimenezo, adachokako ku Yerusalemuko.
6
Tsono Chauta adauza mneneri Yeremiya kuti,
7
“Ine Chauta, Mulungu wa Israele, ndikunena kuti mfumu ya ku Yuda imene idakutuma kuti udzapemphe nzeru kwa Ine, uiwuze kuti, ‘Gulu lankhondo la Farao limene lidaabwera kuti lidzakuthandize, posachedwa libwerera kwao ku Ejipito, dziko lake.
8
Ndipo Ababiloni adzabwerera kudzathira nkhondo mzinda uno. Adzaugonjetsa ndi kuutentha.’
9
Zimene akunena Chauta ndi izi, akuti musadzinyenge ndi kumaganiza kuti Ababiloni adzachoka ndi kukusiyani. Pepani sadzachoka ai.
10
Ngakhale mutagonjetsa gulu lonse la Ababiloni limene mukumenyana nalo nkhondo, ngakhalenso mwa iwowo mutatsala ovulala okhaokha m'mahema mwao, iwo omwewo adzadzambatuka nkuutentha mzindawu.”
11
Pamene gulu lankhondo la Ababiloni lidaleka kuthira nkhondo mzinda wa Yerusalemu, chifukwa choopa gulu lankhondo la Farao,
12
Yeremiya adanyamuka kuchoka ku Yerusalemu kupita ku dziko la Benjamini kuti akalandire gawo lake la minda ya makolo ake.
13
Pamene adafika pa Chipata cha Benjamini, mlonda wina wapamenepo, dzina lake Iriya, mwana wa Selemiya, mwana wa Hananiya, adagwira Yeremiya, nati, “Iwetu ukuthaŵira kwa Ababiloni ati!”
14
Yeremiya adati, “Zimenezo ai, si zoona. Ine sindikuthaŵira kwa Ababiloni.” Koma Iriyayo sadamumvere ndipo adamgwira nabwera naye kwa akuluakulu.
15
Akuluakulu aja adamkwiyira Yeremiya. Adamkwapula, namtsekera m'nyumba ya mlembi Yonatani imene adaaisandutsa ndende.
16
Yeremiya adaikidwa m'ndende ya pansi pa nthaka, nakhala m'menemo nthaŵi yaitali.
17
Tsiku lina mfumu idatuma anthu kuti akaitane Yeremiya, ndipo idamlandira. Idamufunsa paseri m'nyumba mwake kuti, “Kodi pali mau amene Chauta wakuuza?” Yeremiya adayankha kuti, “Inde, alipo. Inu amfumu mudzaperekedwa m'manja mwa mfumu ya ku Babiloni.”
18
Ndipo adafunsa mfumu Zedekiya kuti, “Kodi ndakulakwirani chiyani inuyo, aphungu anu, kapena anthu anu kuti mundiponye m'ndende?
19
Kodi ali kuti aneneri anu aja amene adakuloserani kuti mfumu ya ku Babiloni sidzakuthirani nkhondo inuyo ndi dziko lanu?
20
Tsono ndikukupemphani inu mfumu mbuyanga, kuti mumve pempho langa. Musandibwezere ku nyumba ya mlembi Yonatani, kuwopa kuti ndingakafereko.”
21
Pamenepo mfumu Zedekiya adalamula kuti Yeremiya asungidwe ku bwalo la alonda. Tsono ankamupatsa chakudya tsiku ndi tsiku, mtanda umodzi wa buledi. Ankamugula kwa anthu opanga buledi, mpaka buledi yense mumzindamo adatha. Motero Yeremiya adakhala m'bwalo la alonda.
← Chapter 36
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 38 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52