bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 13
Jeremiah 13
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 14 →
1
Chauta adandiwuza kuti, “Pita ukagule mpango wa nsalu yabafuta, ukavale m'chiwuno, koma osakauviika m'madzi.”
2
Choncho ndidakagula mpango, monga momwe Chauta adaandiwuzira, ndipo ndidauvala m'chiwuno.
3
Chauta adandiwuzanso mau kachiŵiri kuti,
4
“Tenga mpango uja udagula nkuvala m'chiwuno mwakowu. Unyamuke nkupita msanga ku mtsinje wa Yufurate. Kumeneko ukabise mpangowo m'ming'alu yam'mathanthwe.”
5
Tsono ndidapitadi kukaubisa mpangowo ku Yufurate, monga momwe Chauta adaandiwuzira.
6
Patapita masiku ambiri Chauta adandiwuza kuti, “Nyamuka, pita ku Yufurate, ukatenge mpango wam'chiwuno uja umene ndidaakuuza kuti ukaubise kumeneko.”
7
Ine ndidapita ku Yufurate, ndipo ndidakumba pa malo amene ndidaubisa paja, nkuutenga. Koma ndidaona kuti ndi woonongeka kotheratu, wopandanso ntchito.
8
Apo mau a adandifikanso:
9
Chauta adandiwuza kuti, “Ndimotu m'mene ndidzaonongere zimene a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu amanyadira.
10
Anthu oipaŵa akana kumvera mau anga. Atsata milungu ina, namaitumikira nkumaipembedza. Iwowo adzakhala ngati mpango wopanda ntchitowu.
11
Monga mpango umakanirira m'chiwuno mwa munthu, chonchonso ndidakonza kuti banja lonse la Israele ndi la Yuda lindikangamire kuti onse akhale anthu anga, kuti adzatamande dzina langa ndi kundilemekeza. Koma iwowo sadamvere.
12
“Ukaŵauze anthu mau amene Ine Chauta Mulungu wa Israele ndikunena, akuti: Mtsuko uliwonse wa vinyo adzaudzaza ndi vinyo. Iwowo adzakuyankha kuti, ‘Tikudziŵa bwino kuti mtsuko uliwonse wa vinyo adzaudzaza ndi vinyo.’
13
Tsono ukaŵauze kuti, Chauta akuti, Ndidzaŵamwetsa vinyo anthu onse am'dzikomo mpaka kuledzera. Anthuwo ndi aŵa: mafumu okhala pa mpando wa Davide, ansembe, aneneri, ndi onse okhala mu Yerusalemu.
14
Ndidzaŵagundanitsa mitu kuti aphwanyane okhaokha, atate ndi ana ao!” Akuterotu Chauta. “Sindidzaŵachitira chifundo kapena kuŵamvera chisoni, kapena kukhululuka mtima mpaka nditaŵaononga.”
15
Inu Aisraele, imvani ndipo tcherani khutu. Musakhale odzimva chifukwa ndi Chauta amene akulankhula.
16
Mlemekezeni Chauta, Mulungu wanu, asanagwetse mdima, mapazi anu asanakhumudwe m'chisisira cham'mapiri, asanasandutse kuŵala, kumene mukukufuna, kuti kukhale mdima wandiweyani.
17
Koma mukapanda kumvera, mtima wanga udzalira m'seri chifukwa cha kunyada kwanu. M'maso mwanga mudzadzaza misozi yoŵaŵa chifukwa choti nkhosa za Chauta zatengedwa ukapolo.
18
Uza mfumu pamodzi ndi mai wake kuti, “Tsikani pa mipando yaufumu, poti zisoti zanu zokongola zaufumu zagwa pansi.
19
Mizinda yanu ya ku Negebu aitsekera kunja, palibe wina woti nkuitsekula. Yuda yense watengedwa ukapolo, watengedwa yense ukapolo.
20
“Ŵeramukani, inu a ku Yerusalemu, muwone adani amene akuchokera kumpoto. Kodi nkhosa zimene adakusungitsani zili kuti, nkhosa zanu zokongola zija?
21
Kodi mudzatani akadzakuikirani kuti azikulamulirani anthu amene munkaŵayesa abwenzi anu? Kodi simudzamva zoŵaŵa zonga za mkazi pa nthaŵi yochira?
22
Mukamadzifunsa kuti, ‘Kodi zimenezi zatigwera bwanji?’ Nchifukwa cha machimo anu ambiri kuti zovala zanu zikwinzidwe, ndipo kuti akuchiteni zankhanza.
23
Kodi munthu wakuda nkusintha khungu lake? Kodi kambuku nkusintha maŵanga ake? Ndiye kuti inuyo, ozoloŵera kuchimwanu, mungathe kumachita zabwino ngati?
24
Chifukwa cha kuipa kwanuko, ndidzakumwazani ngati mankhusu, onka nauluka ndi mphepo yakuchipululu.
25
Zokuyenerani nzimenezi, chilango chimene ndakukonzerani chifukwa choti mwandiiŵala, mwakhala mukudalira milungu yonama,” akuterotu Chauta.
26
“Ine Chauta ndidzakwinza zovala zanu mpaka kumaso, ndipo maliseche anu adzaoneka.
27
Ndaona zonyansa zanu, zigololo zanu, kutchetcherera kwanu, ndi ziwerewere zanu zochitika pa mapiri, kuthengo. Tsoka kwa inu a ku Yerusalemu! Mudzakhala osayeretsedwabe pa zachipembedzo mpaka liti?”
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52