bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 42
Jeremiah 42
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 41
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 43 →
1
Atsogoleri onse a ankhondo, pamodzi ndi Yohanani mwana wa Kareya, Azariya mwana wa Hesaya, kudzanso anthu onse ang'onoang'ono ndi akuluakulu omwe, adapita kwa mneneri Yeremiya. Adamuuza kuti,
2
“Ife tabwera ndi dandaulo lathu. Chonde, mutipempherere kwa Chauta, Mulungu wanu, ife amene tatsala oŵerengeka. Tangotsalatu ochepa chabe pa anthu ambiri, monga mukutiwoneramu.
3
Mupemphere kuti Chauta, Mulungu wanu atiwuze kumene tiyenera kupita ndi zimene tikachite.”
4
Apo mneneri Yeremiya adaŵauza kuti, “Ndamva zimene mwanenazi, ndidzapemphera kwa Chauta, Mulungu wanu monga mukufunira. Ndipo zonse zimene Chauta Mulungu wanu ati anene, ndidzakuuzani, sindidzakubisirani kanthu.”
5
Iwowo adauza Yeremiya kuti, “Chauta akhale mboni yoona ndi yokhulupirika yodzatitsutsa ngati sitichita zimene Chauta Mulungu wanu wakutumani kuti mudzatiwuze.
6
Kaya nzabwino, kaya zoipa, tidzamvera ndithu mau a Chauta Mulungu wathu, amene takutumani kuti mukampemphe kanthu m'dzina lathu. Tidzamvera Chauta Mulungu wathu, kuti zinthu zitiyendere bwino.”
7
Atatha masiku khumi, Chauta adalankhula ndi Yeremiya.
8
Tsono Yeremiya adaitana Yohanani mwana wa Kareya, pamodzi ndi atsogoleri onse a ankhondo amene anali nawo, ndiponso anthu onse, ang'onoang'ono ndi akuluakulu omwe.
9
Adaŵauza kuti, “Chauta, Mulungu wa Israele, amene mudaandituma kuti ndikampemphe kanthu m'dzina lanu, akunena kuti,
10
‘Ngati mukhala m'dziko lino, ndiye kuti mudzakhazikika, sindidzakuchotsani. Zoonadi, ndidzakukhazikitsani, osakuchotsani konse. Ndikumva chisoni chifukwa cha mazunzo amene ndidagwetsa pa inu.
11
Musaiwope mfumu ya ku Babiloni imene mukuiwopa tsopano. Musaiwope mfumuyo, chifukwa Ine ndili nanu, kuti ndikupulumutseni ndi kukuchotsani m'manja mwake, ndatero Ine Chauta.
12
Ndidzakuchitirani chifundo, kotero kuti iyenso adzakuchitirani chifundo ndi kukulolani kuti mukhale m'dziko lanu lino.’
13
Koma mwina simumvera mau a Chauta, nkunena kuti,
14
‘Ai, tipita ndithu ku Ejipitoko, kopanda nkhondo, kosamva kulira kwa lipenga, kosasoŵa chakudya, ndipo tidzakhala kumeneko.’
15
Tsono mukatero, inu otsala a ku Yuda, imvani mau aŵa a Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele. Akunena kuti, ‘Mukatsimikiza za kupita ku Ejipitozi, nkupitadi kukakhala kumeneko,
16
ndiye kuti nkhondo mukuiwopayo idzakugonjetsani ku Ejipito komweko. Njala mukuiwopayo idzakuvutanibe ngakhale ku Ejipitoko, ndipo mudzafera kumeneko.
17
Anthu onse amene akutsimikiza za kupitadi ku Ejipito, ndi kukakhala kumeneko, adzafa ndi nkhondo, njala ndiponso mliri. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzatsale kapena kupulumuka ku zoopsa zimene ndidzaŵagwetsere.’ ”
18
“Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunenanso kuti, ‘Monga momwe anthu okhala ku Yerusalemu ndidaŵakwiyira mwaukali, momwemonso ndidzakukwiyirani inuyo mukadzapita ku Ejipito. Mudzasanduka chinthu chonyansa ndi chochititsa mantha, chomachiseka ndi chonyozeka. Malo ano simudzaŵaonanso.
19
Inu otsala a ku Yuda, musapite ku Ejipito. Ndithudi ndakuchenjezani lero, kusokera kwanu kungakutayitseni moyo.’
20
Paja mudaandituma kwa Chauta Mulungu wanu ndi kunena kuti, ‘Mutipempherere kwa Chauta Mulungu wathu, ndipo mutiwuze chilichonse chimene Chauta Mulungu wathu ati anene, ife tidzazichita.’
21
Ndakuuzani zonse lero, koma simudamvere Chauta Mulungu wanu pa zonse zimene adandituma kuti ndikuuzeni.
22
Tsono mudziŵe kuti mudzafadi ndi nkhondo, njala ndiponso mliri, ku malo amene mufuna kupita kuti mukakhaleko.”
← Chapter 41
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 43 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52