bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 17
Jeremiah 17
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 18 →
1
Chauta akuti, “Uchimo wa Yuda ndi wolembedwa ndi cholembera chachitsulo, cha nsonga ya mwala wadaimondi. Uchimowo walembedwa pa mitima yao ndiponso pa maguwa ao.
2
Chonsecho ana ao amakumbukira maguwa ao aja ndi zoimiritsa zao zansembe, patsinde pa mtengo wogudira uliwonse, pa mapiri am'dzikomo.
3
Chuma chanu ndi katundu wanu yense ndidzazipereka kwa ofunkha, kuti zikhale dipo la machimo anu ochitika m'dziko lanu lonse.
4
Mudzataya dziko limene ndidakupatsani kuti likhale ngati choloŵa chanu. Ndidzakusandutsani akapolo otumikira adani anu m'dziko limene simulidziŵa. Ndithu mkwiyo wanga uli ngati moto woyaka, ndipo udzayakadi mpaka muyaya.”
5
Chauta akunena kuti, “Tsoka kwa munthu wodalira munthu mnzake, amene amagonera pa munthu mnzake kuti amthandize, pamene mtima wake wafulatira Chauta.
6
Woteroyo adzakhala ngati chitsamba m'chipululu, ndipo sadzapeza zabwino. Adzakhala m'chipululu mopanda madzi, m'dziko lamchere m'mene anthu sangathe kukhalamo.
7
“Koma ndi wodala munthu wokhulupirira Chauta, amene amagonera pa Chautayo.
8
Adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m'mphepete mwa mtsinje, umene umatambalitsa mizu yake m'mbali mwa madzi. Suwopa kukamatentha, chifukwa masamba ake safota. Pa chaka chachilala sukuda nkhaŵa, ndipo suleka kubala zipatso.”
9
Mtima wa munthu ndi chinthu chonyenga kwambiri kupambana zinthu zonse. Kuipa kwake nkosachizika. Kodi ndani angathe kuumvetsa?
10
“Koma Ine Chauta ndimafufuza maganizo ndi kuuyesa mtimawo. Ndimamchitira munthu aliyense molingana ndi makhalidwe ake ndiponso moyenerera ntchito zake.”
11
Munthu wopeza chuma pobera anthu ena, ali ngati nkhwali yokonkhomola mazira amene sidaikire. Masiku asanachuluke, chumacho chimamthera, potsiriza amasanduka ngati chitsilu.
12
Nyumba yathu yopembedzeramo ili ngati mpando waufumu waulemerero, wokhazikika pa phiri lalitali chiyambire.
13
Inu Chauta, amene Aisraele amagonera pa Inu, onse okukanani adzaŵachititsa manyazi. Onse okusiyani adzafafanizika ngati maina olembedwa pa dothi, chifukwa chokana Chauta, kasupe wa madzi opatsa moyo.
14
Inu Chauta, chiritseni ndipo ndidzachiradi. Pulumutseni ndipo ndidzapulumukadi. Ndinu amene ndimakutamandani.
15
Anthu akundifunsa kuti, “Zija ankanena Chautazi zili kuti? Zitachitikatu kuti tiziwone!”
16
Ine sindidakukakamizeni kuti mufikitse zovuta. Mukudziŵa kuti tsiku la tsoka sindinkalilakalaka. Zonse zimene ndidalankhula mukuzidziŵa.
17
Musandichititse mantha. Inu nokha ndiye pothaŵira panga, tsoka likandigwera.
18
Koma ondizunza ndiwo achite manyazi, osati ineyo. Ade nkhaŵa ndi iwowo, osati ineyo. Tsiku la tsoka liŵafikire, ndipo muŵaononge kotheratu.
19
Chauta adandiwuza kuti, “Pita ukaime pa chipata chachikulu chodzerapo anthu ambiri, chimene mafumu a ku Yuda amaloŵerapo ndi kutulukirapo. Upitenso ku zipata zonse za Yerusalemu.
20
Ukanene kuti: Imvani mau a Chauta, inu mafumu a ku Yuda, inu anthu a ku Yuda, ndi inu nonse okhala mu Yerusalemu amene mumaloŵera pa zipata zimenezi.
21
M'mau a Chautawo ndi aŵa: Kuti musunge moyo wanu, samalani bwino kuti pa tsiku la Sabata musanyamule katundu, kapena kuloŵa naye pa zipata za Yerusalemu.
22
Musanyamule katundu aliyense kutuluka naye m'nyumba mwanu, kapena kugwira ntchito iliyonse pa Sabata. Koma muzilisunga tsiku la Sabatalo kuti likhale lopatulika, monga ndidalamulira makolo anu.
23
Iwowo sadamvere kapena kusamalako, koma ndi mitima yokanika adakana kumva ndi kulandira malangizo anga.”
24
Tsono Chauta akunena kuti, “Koma inu muzindimvera Ine, ndi kuleka kunyamula katundu kapena kumatuluka naye pa zipata za mzinda uno pa Sabata, ndipo muzisunga tsiku la Sabata osagwira ntchito pa tsiku limenelo.
25
Mukatsata zimenezi, ndiye kuti pa zipata za mzinda umenewu pazidzaloŵera mafumu odzakhala pa mpando waufumu wa Davide. Azidzaloŵa atakwera pa magareta ndi pa akavalo, ali pamodzi ndi akalonga ao ndi anthu a ku Yuda ndiponso anthu a mu Yerusalemu. Ndipo anthu adzakhazikika mu mzinda umenewu mpaka muyaya.
26
Anthu adzachokera ku mizinda ya Yuda ndi dziko lonse lozungulira Yerusalemu, dziko la Benjamini, dziko lazidikha, dziko lazitunda, ndiponso ku Negebu, atatenga nsembe zopsereza, nsembe zaufa, nsembe zalubani, ndiponso nsembe zothokozera, kupita nazo ku Nyumba ya Chauta.
27
Koma inu mukapanda kundimvera, mukapanda kusunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika, ndipo mukamanyamula katundu aliyense nkumakaloŵa pa zipata za Yerusalemu pa tsiku la Sabata, ndiye kuti ndidzazitentha zipata zimenezo. Moto udzapsereza nyumba zaufumu za ku Yerusalemu, moto wake wosazimika.”
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52