bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 40
Jeremiah 40
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 39
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 41 →
1
Chauta adalankhula ndi Yeremiya pa nthaŵi imene Nebuzaradani mtsogoleri wa alonda ankhondo adammasula ku Rama. Adaampeza ali womangidwa ndi unyolo pamodzi ndi am'ndende ena a ku Yerusalemu ndi a ku Yuda opita nawo ku Babiloni.
2
Mtsogoleriyo adatenga Yeremiya namuuza kuti, “Chauta, Mulungu wako, adanena kuti adzaononga malo ano.
3
Ndipo zimenezi wazichitadi monga momwe adaanenera, chifukwa chakuti inu anthu mudachimwira Chauta, simudamumvere.
4
Koma iwe Yeremiya, lero ndikukumasula maunyolo m'manjamu. Tiye ku Babiloni ngati ufuna, ndipo ndidzakusamala bwino. Koma ngati sufuna kupita, palibe kanthu. Dziko ndi lonseli monga ukuwonera, upite kumene uwona kuti nkoyenera.
5
Ngati supita, ubwerere kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani amene mfumu ya ku Babiloni idaamsankha kuti akhale bwanamkubwa wa mizinda ya ku Yuda. Ukakhale ndi iyeyo pakati pa anthu, kapena upite kulikonse kumene ufuna.” Tsono mtsogoleri wa nkhondo uja adampatsa chakudya, nampatsanso mphatso, ndipo adamuuza kuti, “Ai, pita bwino!”
6
Pamenepo Yeremiya adapita kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa. Ndipo adakhala naye pakati pa anthu otsala m'dzikomo.
7
Panali atsogoleri ena ankhondo amene sadadzipereke nao. Iwowo pamodzi ndi anthu ao adamva kuti mfumu ya ku Babiloni idaika Gedaliya, mwana wa Ahikamu, kuti akhale bwanamkubwa wa dzikolo, aziyang'anira anthu osauka kwambiri aja, amuna, akazi ndi ana, amene sadaŵatenge ukapolo kupita nawo ku Babiloni.
8
Tsono amene adapita kwa iye ku Mizipa ndi aŵa: Ismaele mwana wa Netaniya, Yohanani ndi Yonatani ana a Kareya, Seraya mwana wa Tanihumeti, ana aamuna a Efayi a ku Netofa, ndi Yezaniya mwana wa Maaka, iwowo pamodzi ndi anthu ao.
9
Onsewo, Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani, adaŵalonjeza molumbira kuti, “Musaope kuŵagwirira ntchito Ababiloniwo. Khalani m'dzikomu, muzimera mfumu ya ku Babiloni, ndipo zinthu zonse zidzakuyenderani bwino.
10
Ine nditsalira ku Mizipa kuti ndizikuimirirani kwa Ababiloni akamabwera. Koma inu mutenge zipatso zanu, vinyo wanu, mafuta anu, ndipo muzisunge ndithu. Muzikhala m'mizinda imene mwalandayo.”
11
Nawonso Ayuda a ku Mowabu, ku Amoni ndi ku Edomu ndi a ku maiko ena, adamva kuti mfumu ya ku Babiloni idasiyako anthu ena ku Yuda, ndipo kuti idaŵaikira Gedaliya, mwana wa Ahikamu mdzukulu wa Safani, kuti akhale bwanamkubwa wao.
12
Tsono Ayuda onsewo adabwera kuchokera ku maiko onse kumene adaabalalikira. Adabwerera ku Yuda nakadziwonetsa kwa Gedaliya ku Mizipa. Ndipo minda yao idabereka zipatso zambiri ndi vinyo wambiri.
13
Tsiku lina Yohanani mwana wa Kareya, pamodzi ndi atsogoleri ankhondo amene sadadzipereke aja, adapita kwa Gedaliya ku Mizipa.
14
Adamufunsa kuti, “Kodi mukudziŵa kuti Baalisi mfumu ya Aamoni watuma Ismaele, mwana wa Netaniya kuti adzakupheni?” Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sadaŵakhulupirire.
15
Tsono Yohanani mwana wa Kareya, mwachinsinsi adauza Gedaliya kuti, “Loleni kuti ndikaphe Ismaele mwana wa Netaniyayu, ndipo wina aliyense sadzadziŵa. Nanga inu akuphereninji ndi kulola kuti Ayuda onse okuzunguliraniŵa amwazikane, ndipo otsala a ku Yuda adzaonongedwe?”
16
Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu adayankha Yohanani mwana wa Kareya kuti, “Iyai, usachite zotero. Zimene ukunena za Ismaele nzabodza.”
← Chapter 39
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 41 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52