bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 35
Jeremiah 35
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 34
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 36 →
1
Pa nthaŵi imene Yehoyakimu, mwana wa Yosiya, anali mfumu ya ku Yuda, Chauta adalankhula nane ine Yeremiya. Adati,
2
“Pita ku banja la Arekabu, ukaŵaitane anthu akumeneko kuti abwere m'chipinda chimodzi cha Nyumba ya Chauta. Atafika, uŵapatse vinyo kuti amwe.”
3
Motero ndidabwera ndi Yazaniya (mwana wa Yeremiya winanso, mwana wa Habaziniya,) pamodzi ndi abale ake ndiponso ana ake onse aamuna, ndiye kuti banja lonse la Arekabu.
4
Ndidabwera nawo ku nyumba ya Chauta, ku chipinda cha ophunzira a Hanani, mwana wa Igadaliya, munthu womvera Mulungu. Chipinda chimenechi chinali pafupi ndi chipinda cha akuluakulu, pamwamba pa chipinda cha Maseiya, mwana wa Salumu, mlonda wapakhomo.
5
Tsono ndidaika mbiya zodzaza ndi vinyo ndi zikho zomwera pamaso pa Arekabuwo, ndipo ndidaŵauza kuti, “Nayu vinyo, imwani.”
6
Koma iwowo adati, “Ife sitimwa vinyoyu, poti kholo lathu Yonadabu mwana wa Rekabu adatilamula kuti, ‘Musadzamwe vinyo, inuyo ndi ana anu omwe.
7
Musadzamange nyumba kapena kubzala mbeu, kapena kulima minda yamphesa. Zinthu zimenezi musadzakhale nazo. M'malo mwake muzidzangokhala m'mahema pa moyo wanu wonse, kuti mukhale nthaŵi yaikulu m'dziko limene mukukhalamo.’
8
Takhala tikutsata malamulo a kholo lathu Yonadabu, mwana wa Rekabu, ndipo pa moyo wathu wonse sitidamwe vinyo ifeyo, akazi athu, ana athu aamuna ndi ana athu aakazi.
9
Sitidamange nyumba kuti tizikhalamo, kapena kulima minda yamphesa kapena minda ina iliyonse.
10
Tangokhala m'mahema basi. Motero tamvera ndi kusunga malamulo onse a kholo lathu Yonadabu.
11
Koma pamene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adathira nkhondo dziko lino, tidanena kuti, ‘Tiyeni tichoke, tipite ku Yerusalemu kuti tithaŵe magulu ankhondo a Ababiloni ndi a Asiriya.’ Nchifukwa chake tikukhala kuno ku Yerusalemu.”
12
Tsono mau a Chauta adadza kwa Yeremiya onena kuti,
13
Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele akuti, “Pita ukafunse anthu a ku Yuda ndi anthu a ku Yerusalemu kuti, ‘Kodi simungatengeko nzeru ndi kumvera mau anga?’
14
Lamulo la Yonadabu, mwana wa Rekabu, limene adalamula zidzukulu zake kuti asadzamwe vinyo, iwowo asungadi. Samwa vinyo mpaka lero lino chifukwa chomvera lamulo la kholo lao. Ndakhala ndikulankhula nanu kaŵirikaŵiri kukuchenjezani, komabe simudandimvere.
15
Ndidatuma atumiki anga aneneri kuti adzakuuzeni kuti, ‘Aliyense mwa inu asiye ntchito zake zoipa. Konzani makhalidwe anu, ndipo muleke kutsata milungu ina, musamaipembedza. Motero mudzakhala m'dziko limene ndakupatsani inu ndi makolo anu.’ Komabe inu simudalabadeko, simudandimvere.
16
Ana a Yonadabu, mwana wa Rekabu, adatsata lamulo limene kholo lao lidaŵapatsa. Koma inuyo simudandimvere ai.
17
Nchifukwa chake Ine Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, ndikuti ndidzaŵaononga Ayuda ndi anthu onse okhala ku Yerusalemu, chifukwa chakuti sadandimvere pamene ndidaŵalankhula, sadandiyankhe nditaŵaitana.”
18
Yeremiya adauza Arekabu aja mau a Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuti, “Chifukwa chakuti mudamvera lamulo la Yonadabu kholo lanu, ndipo mudatsata malangizo ake ndi kuchita zonse zimene adakuuzani kuti muchite,
19
tsono Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, ‘Yonadabu mwana wa Rekabu sadzasoŵa mdzukulu wonditumikira mpaka muyaya.’ ”
← Chapter 34
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 36 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52