bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 15
Jeremiah 15
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 16 →
1
Pambuyo pake Chauta adandiwuza kuti, “Ngakhale Mose ndi Samuele akadaima pamaso panga akupempherera anthu ameneŵa, sindikadaŵamvera chisoni. Achotseni, ndisaŵaonenso, apite basi.
2
Akakufunsa kuti, ‘Kodi tipite kuti?’ Uŵauze kuti Ine ndati, “ ‘Oyenera mliri adzafa ndi mliri, oyenera lupanga adzafa ndi lupanga, oyenera njala adzafa ndi njala, oyenera ukapolo, adzapita ku ukapolo.’
3
“Ndidzaŵagwetsera zinthu zinai izi zoŵaononga: lupanga loŵapha, agalu oŵaluma, mbalame zamumlengalenga ndiponso zilombo zoti ziŵaphe ndi kuŵadya.
4
Ndidzaŵasandutsa chinthu chochititsa nyansi kwa anthu a m'maufumu onse a dziko lapansi, chifukwa cha zimene Manase mwana wa Hezekiya, mfumu ya ku Yuda, adachita ku Yerusalemu.”
5
Chauta akuti, “Kodi inu a ku Yerusalemu adzakumverani chisoni ndani? Adzakulirani ndani? Ndani adzapatuke kuti akufunseni za moyo wanu?
6
Ine mudandikana, mukupitirirabe kundifulatira. Motero ndidakweza mkono wanga nkukukanthani. Ndidatopa nako kukhululuka.
7
Ndidaŵabalalitsira uku ndi uku, monga momwe amachitira ndi mankhusu popeta ndi lichero. Ndidaŵaliritsa anthu anga ndi kuŵaononga, chifukwa sadafune kusiya makhalidwe ao oipa.
8
Akazi amasiye ndidaŵachulukitsa, kupambana mchenga wakunyanja. Amai ndidaŵaonongera ana ao akali anyamata abiriŵiri. Mwadzidzidzi ndidaŵagwetsera chisoni ndi nkhaŵa.
9
Mai wa ana asanu ndi aŵiri wakomoka, akupuma mwabefu. Mdima wamgwera kukadali masana. Adamchititsa manyazi ndipo wataya mtima. Otsala onse ndidzaŵapereka kwa adani kuti aŵaphe ndi lupanga,” akuterotu Chauta.
10
Inu mai wanga, tsoka kwa ine kuti mudandibala ine munthu wokangana ndi wotsutsana ndi anthu pa dziko lonse. Sindidakongole kanthu kwa munthu kapena kukongoza munthu kanthu. Komabe anthu onse akunditukwana.
11
Chauta adayankha kuti, “Koma zoonadi ndidzakulanditsa kuti upeze bwino. Ndithudi, adani ako adzakupemba pa nthaŵi ya tsoka ndi ya mavuto.
12
Kodi munthu angathe kudula chitsulo, chitsulo chochokera kumpoto chosakaniza ndi mkuŵa?
13
“Anthu inu, chuma chanu chonse pamodzi ndi katundu wanu ndidzazipereka kwa ofunkha popanda malipiro, chifukwa cha machimo anu ambiri m'dziko lonse.
14
Ndidzakusandutsani akapolo a adani anu m'dziko limene simulidziŵa. Ndithudi, mkwiyo wanga wayaka, ndipo udzakutenthani kosalekeza.”
15
Ine ndidati, “Inu Chauta, mumadziŵa zonse. Mundikumbukire ndipo mundithandize. Mundilipsirire anthu ondizunza. Mundilezere mtima, musandilande moyo. Onani mavuto amene ndikupeza chifukwa cha Inu.
16
Nditamva mau anu, ndidaŵalandira bwino, mauwo adandipatsa chimwemwe ndi chisangalalo. Paja Inu Chauta Wamphamvuzonse, ndimadziŵika ndi dzina lanu.
17
Sindidakhale nao m'gulu la anthu amadyera, sindidasangalale nawo anthu amenewo. Ndidakhala ndekha chifukwa choti dzanja lanu linali pa ine, ndipo mumtima mwanga mudadzaza mkwiyo.
18
Nanga chifukwa chiyani mavuto anga sakutha? Chilonda changa nchosatha, sichikupola. Monga nkuti mwandinyenga ngati chitsime chouma kapena ngati mtsinje wopanda madzi?”
19
Chauta adayankha kuti, “Ukabwerera kwa Ine, ndidzakulandiranso, ndipo udzanditumikiranso. Ukamalankhula zenizeni, osati zachabe, udzakhala wondilankhulira. Anthu ameneŵa ayenera kudzabweranso kwa iwe, koma iwe usabwerere kwa iwowo.
20
Ndidzakusandutsa wolimba ngati linga lamkuŵa kwa anthuwo. Iwo adzalimbana nawe, koma sadzakupambana, pakuti Ine ndili nawe, ndidzakulanditsa ndi kukupulumutsa.
21
Ndidzakulanditsa kwa anthu oipa, ndipo ndidzakuwombola kwa anthu ankhanza,” akuterotu Chauta.
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52