bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 11
Jeremiah 11
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 12 →
1
Chauta adauza Yeremiya kuti,
2
“Imva mau a chipangano ichi, ndipo ulankhule nawo anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu.
3
Uŵauze kuti mau a Chauta, Mulungu wa Israele, ndi aŵa: Atembereredwe munthu amene sasunga mau a chipangano,
4
chimene ndidachita ndi makolo anu, nditaŵatulutsa ku dziko la Ejipito. Nditaŵachotsa m'ng'anjo ya moto ija, ndidati, ‘Mukamandimvera ndi kumachita zimene ndikuuzani, inu mudzakhala anthu anga, Ine ndidzakhala Mulungu wanu.
5
Choncho ndidzachita zimene ndidalonjeza makolo anu molumbira, zakuti ndidzaŵapatsa dziko lamwanaalirenji, dziko limene mukukhalamoli.’ ” Tsono ine ndidayankha kuti, “Zikhale momwemo, Inu Chauta.”
6
Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Ulalike mau onseŵa ku mizinda ya ku Yuda ndi m'miseu ya mu Yerusalemu. Uŵauze kuti, ‘Imvani mau a chipangano ichi, ndipo muŵasunge.
7
Nthaŵi ndi nthaŵi ndakhala ndikuŵachenjeza makolo anu kuyambira pamene ndidaŵatulutsa ku dziko la Ejipito mpaka lero lino. Ndakhala ndikuŵauza kuti, “Mverani mau anga.”
8
Koma sadamvere, sadalabadeko. Aliyense adangoti nkhongo gwa, kutsata makhalidwe a mtima wake woipa. Ndidaŵalamula kuti asunge chipangano changa, koma iwo sadachisunge. Nchifukwa chake ndidaŵalanga monga m'mene ndidaanenera.’ ”
9
Kenaka Chauta adandiwuza kuti, “Anthu a ku Yuda ndi anthu a mu Yerusalemu andiwukira.
10
Abwereranso ku machimo a makolo ao amene adakana kundimvera. Akutsata milungu ina ndi kumaipembedza. A ku Israele ndi a ku Yuda aphwanya chipangano chimene ndidapangana ndi makolo ao.
11
Nchifukwa chake Ine Chauta ndikunena kuti ndidzaŵagwetsa m'mavuto amene sangathe kuŵalewa. Ngakhale alire kwa Ine, sindidzamvera.
12
Anthu a m'mizinda ya ku Yuda ndi a mu Yerusalemu adzapita kukalirira chithandizo kwa milungu imene ankaperekako nsembe. Koma singathe kuŵapulumutsa pa nthaŵi ya mavuto ao.
13
Zoonadi, iwe Yuda, milungu yako yachuluka ngati chiŵerengero cha midzi yako. Maguwa ootcherapo nsembe kwa Baala achuluka ngati miseu ya mu Yerusalemu.
14
Tsono iwe Yeremiya, usaŵapempherere anthu ameneŵa. Usaŵapepesere kwa Ine kapena kuŵadandaulira. Ndithu, Ine sindidzaŵamvera akadzandiitana pa nthaŵi ya mavuto ao.
15
Kodi anthu anga okondedwa adzachitanji m'Nyumba mwanga? Suja iwowo achita zoipa kwambiri? Kodi malumbiro anu ndi nyama zopereka ku nsembe zingathe kukutetezani ku tsoka lanu?
16
Kale Chauta ankakuyerekezani ndi mtengo wa olivi wa masamba obiriŵira ndi wa zipatso zokongola. Koma tsopano adzautentha ndi mkuntho wamkokomo, ndipo nthambi zake zidzapserera.
17
Chauta Wamphamvuzonse, yemwe adakubzalani, ndiye wagamula kuti adzakulangani koopsa, chifukwa cha zoipa zimene mudachita, inu a m'banja la Israele ndi la Yuda. Mwamukwiyitsa pakupereka nsembe zopsereza kwa Baala.”
18
Chauta adandiwululira, ndipo ndidadziŵa za chiwembu cha anthu. Iye adatsekula maso anga nandiwonetsa ntchito zao zoipa.
19
Ndidakhala ngati mwanawankhosa amene akupita naye kokamupha. Sindidadziŵe kuti chidaloza pa ine chiwembu chimene ankakonzekera nkumanena kuti, “Tiyeni tiwudule mtengowu ukali moyo. Tiyeni timuphe munthu ameneyu, kuti asadzakumbukikenso.”
20
Inu Chauta Wamphamvuzonse amene mumaweruza molungama, amene mumayesa mtima ndi maganizo, onetseni kuti mwaŵalipsira, pajatu ndidadzipereka m'manja mwanu!
21
Nchifukwa chake Chauta akunena za anthu a ku Anatoti amene afuna kuwononga moyo wanga namanena kuti, “Usalosenso m'dzina la Chauta kuti tingakuphe.”
22
Nchifukwa chake Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ndidzaŵalanga. Anyamata ao adzaphedwa ku nkhondo. Ana ao aamuna ndi aakazi adzafa ndi njala.
23
Sadzapulumuka ndi mmodzi yemwe, chifukwa ndidzaononga anthu a ku Anatoti, chikadzafika chaka chao cha chilango.”
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52