bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 14
Jeremiah 14
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 15 →
1
Ine Yeremiya Chauta adandiwuza mau onena za chilala, mau ake adati,
2
“Yuda akulira, mizinda yake ikuvutika, anthu ake adzigwetsa pansi mwachisoni. Kulira kwa anthu a mu Yerusalemu kwakula.
3
Atsogoleri ao otchuka akutuma antchito ao kuti akatunge madzi. Apita ku zitsime, koma osapezako madzi, ndiye akubwerera ndi mitsuko yopanda kanthu. Achita manyazi ndipo atha nzeru, adziphimba kumaso.
4
Pansi mpouma kotheratu, poti kulibe mvula. Alimi akuchita manyazi, ndipo adziphimba kumaso.
5
Mbaŵala yomwe ikusiya mwana wake wakhanda ku thengo chifukwa choti kulibe msipu.
6
Mbidzi zikuima pa zitunda zopanda kanthu, zikupuma moti ŵefuŵefu ngati nkhandwe. M'maso mwachita chidima, chifukwa chosoŵa msipu.”
7
Anthu akuti, “Inu Chauta, ngakhale machimo athu akutipalamulitsa, komabe muchitepo kanthu kuti dzina lanu lisanyozeke. Kusakhulupirika kwathu nkwakukuludi. Takuchimwirani zedi.
8
Inu Chauta, amene muli chikhulupiriro cha Aisraele, ndiponso Mpulumutsi wao pa nthaŵi ya mavuto, mukukhaliranji ngati mlendo m'dziko lino, ngati wapaulendo wogona usiku umodzi?
9
Chifukwa chiyani mukukhala ngati munthu wothedwa nzeru? Mukukhaliranji ngati wankhondo amene sangathenso kupulumutsa anthu? Komabe Inu Chauta, muli pakati pathu, ife amene timadziŵika ndi dzina lanu, choncho musatisiye tokha.”
10
Chauta akunena za anthu ameneŵa kuti, “Amakonda kuyendayenda kumene afuna, ndipo sangathe kudziletsa. Nchifukwa chake Ine Chauta sindingakondwere nawo, ndipo tsopano ndidzakumbukira kuipa kwao, ndidzaŵalanga chifukwa cha machimo ao.”
11
Pambuyo pake Chauta adandiwuza kuti, “Usaŵapempherere anthu ameneŵa, kuŵafunira zabwino.
12
Ngakhale asale zakudya, Ine sindidzamva kulira kwao. Ndipo ngakhale apereke nsembe zopsereza ndi chopereka cha chakudya, sindidzazilandira. Koma ndidzaŵaononga ndi nkhondo, njala ndi mliri.”
13
Koma ine ndidati, “Ha, Inu Chauta, aneneri ao amauza anthu kuti sadzafa ndi nkhondo, ndipo simudzagwa njala m'dziko mwathu, koma mudzakhala mtendere wokhawokha.”
14
Koma Chauta adandiyankha kuti, “Zakuti aneneriwo amalosa m'dzina langa, ili ndi bodza. Ine sindidaŵasankhe, sindidaŵatume kapena kulankhula nawo. Iwo amakuloserani zinthu zonama zimene akuti adaziwona m'masomphenya. Amaombeza zabodza, zimene amalankhula ndi zonyenga zopeka iwo eni ake.
15
Nchifukwa chake Ine Chauta ndikunena kuti aneneri ameneŵa akulosa m'dzina langa pamene sindidaŵatume. Amakuuzani kuti simudzafa pa nkhondo kapena ndi njala m'dziko lino. Koma aneneriwo ndiwo amene adzaphedwe pa nkhondo kapena kufa ndi njala.
16
Anthu amene adaŵalosera adzaponyedwa m'miseu ya mu Yerusalemu, atafa pa nkhondo kapena ndi njala. Iwowo, akazi ao, ana ao aamuna ndi ana ao aakazi, onse adzafa, ndipo sipadzaoneka oika maliro ao. Ndithu ndidzaŵalanga poŵagwetsa m'mavuto oŵayenerera.”
17
“Ukaŵauze kuti, ‘Maso anga adze misozi kosalekeza usiku ndi usana. Pakuti anthu anga osankhidwa ali ndi bala lalikulu, akanthidwa kwamphamvu.
18
Ndikamayenda ku thengo, ndikuwona anthu ophedwa pa nkhondo. Ndikaloŵa mu mzinda, ndikuwona anthu ofa ndi njala. Aneneri ndi ansembe akupitirizabe ntchito zao m'dzikomo, koma osadziŵa zimene akuchita.’ ”
19
Kodi anthu a ku Yuda mwaŵatayiratu? Kodi anthu a mu Ziyoni akuipirani m'maso? Chifukwa chiyani mwatikantha kotero kuti sitingathenso kukhala bwino? Tinkayembekeza mtendere, koma sitidaupeze. Tinkayembekeza kuchira, koma tidangoopsedwa kwambiri.
20
Inu Chauta, tikuvomera kuipa kwathu ndiponso kupalamula kwa makolo athu. Ifeyo tidakuchimwiranidi.
21
Musatikane, kuti dzina lanu linganyozeke. Musanyoze mpando wanu wachifumu ndi waulemerero. Mukumbukire chipangano chanu ndi ife, ndipo musachiphwanye.
22
Pakati pa milungu yonama ya anthu a mitundu ina, kodi alipo mulungu wina amene angathe kupereka mvula? Kodi mlengalenga umapereka mvula pawokha? Kodi Inu Chauta, suja ndinu nokha amene mumachita zimenezi? Nchifukwa chake timakhulupirira Inu, popeza kuti ndinu amene mumachita zinthu zonsezi.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52