bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 32
Jeremiah 32
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 31
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 33 →
1
Chauta adalankhula ndi Yeremiya pa chaka cha khumi cha ufumu wa Zedekiya ku Yuda, chimene chinali chaka cha 18 cha ufumu wa Nebukadinezara.
2
Pa nthaŵi imeneyo ankhondo a mfumu ya ku Babiloni ankazinga Yerusalemu ndi zithando zankhondo. Mneneri Yeremiya anali atamtsekera m'bwalo la alonda, m'kati mwa nyumba yaufumu ya ku Yuda.
3
Zedekiya mfumu ya ku Yuda ndiye amene adaamtsekera m'menemo. Mfumuyo idaamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani iwe ukulosa zakuti, Chauta akunena kuti, ‘Mzindawu ndidzaupereka kwa mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzaulanda.
4
Zedekiya mfumu ya ku Yuda sadzapulumuka kwa Ababiloni, koma adzaperekedwa ndithu kwa mfumu ya ku Babiloni. Adzaonana naye maso ndi maso nadzalankhula naye.
5
Zedekiya adzatengedwa kupita ku Babiloni, ndipo adzakhala kumeneko mpaka nditamkhaulitsa, akutero Chauta. Ngakhale iye adzamenyane nawo chotani Ababiloniwo, sadzatha kuŵapambana.’ ”
6
Yeremiya adanena kuti, “Chauta adandiwuza kuti
7
Hanamele, mwana wa Asalumu, amalume anga, akudzandiwona, ndipo adzandiwuza kuti, ‘Gula munda wanga wa ku Anatoti, poti iweyo ndiye woyenera kuuwombola.’
8
Monga momwe Chauta adanenera, Hanamele msuweni wanga adadzandiwonadi ku bwalo la alonda. Iyeyo adati, ‘Gula munda wanga ku Anatoti m'dziko la Benjamini, poti iwe ndiye woyenera kuuwombola kuti ukhale choloŵa chako.’ Tsono ndidadziŵa kuti umenewu unali uthenga wa Chauta uja.
9
Motero ndidagula mundawo ku Anatoti kwa Hanamele msuweni wanga, ndipo mtengo wake unali masekeli asiliva 17.
10
Ndidasaina chipanganocho ndi kuchimata pamaso pa mboni, kenaka nkuyesa ndalamazo pa sikelo.
11
Pambuyo pake ndidatenga makalata anga a chipangano, ina yomata, m'mene munali mau onse a chipangano, ndi ina yosamata.
12
Makalatawo ndidaŵapereka kwa Baruki mwana wa Neriya, mdzukulu wa Maseiya, pamaso pa Hanamele msuweni wanga, pamaso pa mboni zimene zidaasaina chipanganocho, ndiponso pamaso pa Ayuda onse okhala m'bwalo la alonda.
13
Ndidamlangiza Baruki pamaso pa onsewo kuti,
14
Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, walamula kuti iweyo utenge makalata a umboni wa chipanganoŵa, inai yomata inai yosamata, uŵasunge m'mbiya kuti akhale nthaŵi yaitali.
15
Ndithudi Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akutitu idzafika nthaŵi pamene anthu azidzagulanso nyumba, minda ndi mitengo ya mphesa m'dziko lino.”
16
Nditampatsa Baruki, mwana wa Neriya, makalata a chipangano aja, ndidayamba kupemphera kwa Chauta, ndidati,
17
“Ha! Inu Chauta! Mudalenga ndinu dziko lakumwamba ndi dziko lapansi. Mudazilenga ndi dzanja lanu lamphamvu kwambiri. Palibe chokukanikani.
18
Mumaonetsa chikondi chanu chosasinthika kwa anthu osaŵerengeka. Ndipo mumalanga ana chifukwa cha machimo a makolo ao. Inu Mulungu wamkulu ndi wamphamvu, dzina lanu ndinu Chauta Wamphamvuzonse.
19
Zolinga zanu nzazikulu, ndipo ntchito zanu nzamphamvu. Maso anu amaona makhalidwe onse a anthu. Ndipo aliyense mumampatsa mphotho malinga ndi makhalidwe ake ndi ntchito zake.
20
Inu mudachita zizindikiro zozizwitsa ndi ntchito zododometsa ku Ejipito, ndipo mwakhala mukuzichitabe mpaka pano, pakati pa Israele ndiponso pakati pa anthu onse. Motero mwatchukitsa dzina lanu mpaka lero lino.
21
Inu ndi dzanja lanu lamphamvu kwambiri mudatulutsadi anthu anu Aisraele ku Ejipito pochita zizindikiro zozizwitsa ndi ntchito zododometsa zimene zidaopsa adani athu.
22
Mudaŵapatsa dziko lino, limene mudalonjeza makolo ao molumbira, dziko lamwanaalirenji.
23
Adaloŵa nkulilanda kuti likhale lao. Koma iwo sadakumvereni, sadatsate malamulo anu. Sankachita zimene mudaaŵalamula. Nchifukwa chake mwaŵagwetsera mavuto onseŵa.
24
Onani, adani akuzinga ndi nthumbira zankhondo mzindawu kuti aulande. Mzinda umenewu udzaperekedwa kwa Ababiloni utafooka ndi nkhondo, njala ndi mliri. Zimene munkanena zija zachitikadi, monga mwadziwonera nokha.
25
Komabe ngakhale mzindawu udzaperekedwa kwa Ababiloni, Inu Chauta mudandilamula kuti ndigule mundawo pali mboni ziŵiri.”
26
Chauta adauza Yeremiya kuti,
27
“Ine ndine Chauta, Mulungu wa anthu onse. Kodi chilipo choti Ine nkundikanika?
28
Nchifukwa chake Ineyo ndikunena kuti ndidzapereka mzindawu kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni. Iyeyo adzaulanda,
29
ndipo Ababiloni amene akuuthira nkhondo, adzaloŵamo. Adzautentha ndi kugwetsa makamaka nyumba zimene padenga pake anthu ankandipsetsa mtima pofukizapo lubani kwa Baala ndi poperekapo chopereka cha chakumwa kwa milungu ina.
30
Chiyambire pa ubwana wao, Aisraele ndi Ayuda akhala akungochita zoipa pamaso panga, nkumandikwiyitsa ndi ntchito zao zoipa,” akutero Chauta.
31
“Mzinda umenewu wakhala ukuutsa mkwiyo wanga ndi ukali wanga kuyambira nthaŵi imene adaumanga mpaka lero lino. Nchifukwa chake ndiyenera kuuchotsa pamaso panga.
32
Aisraele ndi Ayuda, mafumu ao, akalonga, ansembe, aneneri, pamodzi ndi onse okhala ku Yerusalemu ndi ku Yuda, adandikwiyitsa ndi ntchito zao zoipa.
33
Andifulatira kotheratu. Ngakhale ndidavutikira kumaŵaphunzitsa, sadamve kapena kutolapo nzeru iliyonse.
34
Adaika mafano ao onyansa m'Nyumba imene imadziŵika ndi dzina langa, ndipo adaiipitsa.
35
Adamanga nsanja yopembedzerapo Baala m'chigwa cha Benihinomu, kuti apereke ana ao aamuna ndi aakazi ngati nsembe kwa Moleki. Sindidalamule zimenezo ndine, ndipo sindidaganizeko kuti iwo nkuchita zonyansa zoterezi, ndi kuchimwitsa anthu a ku Yuda pakutero.”
36
Anthu ponena za mzinda umenewu akuti udzaperekedwa kwa mfumu ya ku Babiloni utafooka ndi nkhondo, njala ndi mliri. Komatu zimene Chauta, Mulungu wa Israele akunena ndi izi:
37
Akuti, “Ine ndidzaŵasonkhanitsa anthuŵa kuchokera ku maiko onse kumene ndidaŵapirikitsira ndili wokwiya, waukali ndi wopsa mtima kwambiri. Ndidzaŵabwezanso ku malo ano, ndipo adzakhala kuno ndi mtendere wonse.
38
Adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao.
39
Ndidzaŵapatsa mtima umodzi ndi mkhalidwe umodzi, kotero kuti azidzandiwopa nthaŵi zonse. Motero iwowo ndi ana ao omwe, zinthu zidzaŵayendera bwino.
40
Ndidzachita nawo chipangano chosatha. Sindidzaleka kuŵachitira zabwino. Ndidzaŵapatsa mtima wondiwopa, motero sadzandisiyanso.
41
Ndidzakondwera kuŵachitira zabwino. Ndipo ndidzaŵakhazikitsa m'dziko lino mokhulupirika ndi mtima wanga wonse ndi kufuna kwanga konse.”
42
Chauta akunena kuti, “Monga momwe ndidaŵaonongera anthuŵa, momwemonso ndidzaŵapatsa mtendere umene ndidzaŵalonjeza.
43
Anthu adzagulanso minda m'dziko lino limene inu mumati nlosiyidwa, lopanda munthu ndi nyama yomwe, chifukwa adalipereka kwa Ababiloni.
44
Anthu adzaguladi minda ndi ndalama. Mapangano ake adzalembedwa, adzamatidwa ndipo padzakhala umboni wake ku dera la Benjamini, ku malo oyandikana ndi Yerusalemu, m'mizinda ya ku Yuda, m'mizinda yakumapiri, m'mizinda yakuchigwa ndi yakumwera ku Negebu. Zoona, ndidzaŵabwezera ufulu wao,” akuterotu Chauta.
← Chapter 31
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 33 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52