bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 44
Jeremiah 44
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 43
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 45 →
1
Nawu uthenga umene Yeremiya adalandira wonena za Ayuda amene ankakhala ku dziko la Ejipito ku Migidoli, ku Tapanesi, ku Memfisi ndi ku dziko la Patirosi:
2
“Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, Mwaziwona zoopsa zimene ndidagwetsa pa Yerusalemu ndi mizinda yonse ya ku Yuda. Tsopano yonseyo yasanduka mabwinja, yopanda anthu okhalamo.
3
Zonsezi zidachitika chifukwa cha machimo a anthu amene adaputa mkwiyo wanga, pofukizira lubani milungu ina ndi kumaitumikira, milungu imene sadaidziŵe iwowo kapena inu kapenanso makolo anu.
4
Komabe ine ndidakhala ndikutuma atumiki anga aneneri kuti adzakuuzeni kuti, ‘Musamachita zoipa zimene Ine ndimadana nazo.’
5
Koma makolo anuwo sadamvere, sadasamaleko nkomwe. Sadaleke kuchita zoipa zao, sadasiye kuifukizira lubani milungu ina.
6
Motero ukali wa mkwiyo wanga udayaka ngati moto m'mizinda ya ku Yuda ndi ku miseu ya mu Yerusalemu. Mizindayo idasanduka mabwinja osiyidwa, monga m'mene iliri leromu.
7
“Ndiye tsopano Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuti, Chifukwa chiyani mukuti mudziwononge chotero? Chifukwa chiyani mukufuna kuphetsa Ayuda amuna ndi akazi, ana ndi makanda, osakutsalirani ndi mmodzi yemwe pa mtundu wanu?
8
Chifukwa chiyani mukuputa mkwiyo wanga pochita zoipa ndi manja anu ndiponso pomafukizira lubani milungu ina m'dziko la Ejipito m'mene mukukhala? Mudziwononga nokha, ndipo musanduka chinthu chomachiseka ndi chonyozeka m'maso mwa anthu a mitundu yonse ya pa dziko lapansi.
9
Kodi mwaiŵala zoipa zonse zimene adachita makolo anu, mafumu a ku Yuda ndi akazi ao, ndiponso inuyo ndi akazi anu, ku dziko la Yuda ndiponso pa miseu ya mu Yerusalemu?
10
Mpaka lero lino simudalape, simudachite mantha, simudatsate malamulo anga amene ndidakuikirani inuyo ndi makolo anu.
11
“Nchifukwa chake Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, Ndatsimikiza zoti ndiŵakhaulitse ndi kuŵatheratu anthu a ku Yuda.
12
Ndidzatenga anthu otsala a ku Yuda amene adatsimikiza zopita ku Ejipito kukakhala kumeneko, onsewo adzatheratu. Adzaphedwa m'dziko la Ejipito, ena adzafa pa nkhondo, ena adzafa ndi njala. Ang'onoang'ono ndi akuluakulu omwe adzafadi pa nkhondo kapena kufa ndi njala. Ndipo adzasanduka chinthu chonyansa ndi chochititsa mantha, chinthu chomachiseka ndi chonyozeka.
13
Ndidzalanga Ayuda okhala ku Ejipito monga momwe ndidalangira a ku Yerusalemu. Ndidzaŵalanga ndi nkhondo, njala ndi mliri.
14
Motero mwa anthu otsala ku Yuda, amene adapita nakakhala ku Ejipito, palibe amene adzapulumuke, kapena kukhala moyo, kapena kubwerera ndi kukakhalanso ku Yuda komwe ankalakalaka. Palibe amene adzabwerere, kungopatula ena othaŵa nkhondo.”
15
Tsono amuna onse amene adadziŵa kuti akazi ao ankafukizira lubani milungu ina, ndiponso akazi onse amene anali pamenepo, anthu ochuluka ndithu, kudzanso anthu onse amene ankakhala ku Patirosi m'dziko la Ejipito, adayankha Yeremiya kuti,
16
“Ife sitidzamvera zimene watiwuza m'dzina la Chauta.
17
Koma tidzachitadi zonse zimene tidalumbira. Tidzaifukizira ndithu lubani mfumukazi yakumwamba ndi kuiperekera nsembe zazakumwa, monga tinkachitira ifeyo ndi makolo athu, mafumu athu ndi akalonga athu, m'mizinda ya ku Yuda ndi m'miseu ya mu Yerusalemu. Nthaŵi imeneyo tinali ndi chakudya chambiri, ndipo tinkakhuta, osapeza zovuta.
18
Koma kuchokera nthaŵi imene tidaleka kuifukizira lubani mfumukazi yakumwamba, ndi kumaiperekera nsembe zazakumwa, takhala tikusoŵa zonse, ndipo taonongeka ndi nkhondo ndi njala.”
19
Akaziwo adapitirira ponena kuti, “Pamene tinkaifukizira lubani mfumukazi yakumwamba ndi kumaiperekera nsembe zazakumwa, kodi suja amuna athu ankavomereza m'mene tinkapangira mfumukaziyo makeke abwino olembapo chithunzi chake, ndiponso m'mene tinkaiperekera nsembe zazakumwa?”
20
Atalimva yankho la anthu onsewo, amuna ndi akazi omwe, Yeremiya adati,
21
“Za lubani amene munkafukiza inuyo, makolo anu, mafumu anu, akalonga anu ndi anthu am'dzikomo, m'mizinda ya ku Yuda ndi m'miseu ya mu Yerusalemu, kodi muyesa kuti Chauta adaziiŵala? Kodi nkupanda kuzikumbukira mumtima mwake?
22
Nchifukwa chake Chauta sadathenso kupirira ntchito zanu zoipa ndi zonyansa zimene munkachita. Choncho dziko lanu lidasanduka chipululu, chinthu choopsa ndi chotembereredwa, dziko lopanda anthu, monga liliri leromu.
23
Tsoka limeneli lakugwerani chifukwa choti munkafukiza lubani, ndipo munkachimwira Chauta pokana kumvera mau ake ndi posatsata malamulo ndi malangizo ake.”
24
Yeremiya adauzanso anthu onse, makamaka akazi, kuti, “Mverani mau a Chauta inu nonse ochokera ku Yuda amene mukukhala ku Ejipito.
25
Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuti, Inu ndi akazi anu mudalonjeza ndi pakamwa panupa ndipo mudazichitadi ndi manja anu. Inu mudanena kuti, ‘Tidzachita zimene talumbira. Tidzaifukizira lubani mfumukazi yakumwamba ndi kuiperekera nsembe zazakumwa.’ Chabwino, tsimikizani lonjezo lanuli, ndi kuchitadi zimene mudalumbirazo.
26
Koma tsono imvani mau a Chauta, inu nonse ochokera ku Yuda amene mumakhala ku Ejipito. Chauta akuti, Ndalumbira m'dzina langa lopambana kuti mwa anthu a ku Yuda palibe ndi mmodzi yemwe wodzatchulanso dzina limeneli m'dziko lino la Ejipito kuti, ‘Pali Chauta wamoyo.’
27
Panopo ndikuŵazonda kuti ndiŵachite zoipa osati zabwino. Anthu onse a ku Yuda amene ali ku Ejipito adzaphedwa pa nkhondo, ena adzafa ndi njala, mpaka nditaŵatheratu.
28
Opulumuka ku nkhondo, amene adzabwerera ku Yuda kuchokera ku Ejipito, ndi oŵerengeka okha. Choncho otsala onse a ku Yuda amene adapita kukakhala ku Ejipito adzadziŵa kuti zoona nziti, zaozo kapena zangazi.
29
Ndikukupatsani chizindikiro chakuti ndidzakulangani ku malo ano, kuti choncho mudziŵe kuti mau anga oti ndidzakulangani ndi oonadi.
30
Chizindikirocho ndi ichi: Farao Hofira, mfumu ya ku Ejipito, ndidzampereka kwa adani ake, ndi kwa anthu ofuna kumupha, monga ndidamchitira Zedekiya mfumu ya ku Yuda: iyenso ndidampereka kwa mdani wake Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, amene ankafuna kumupha.”
← Chapter 43
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 45 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52