bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 30
Jeremiah 30
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 29
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 31 →
1
Chauta adauza Yeremiya kuti,
2
“Ine Chauta, Mulungu wa Israele, ndikunena kuti, Lemba m'buku zonse zimene ndakuuza.
3
Nthaŵi ikubwera yoti ndidzaŵabwezere anthu anga, Israele ndi Yuda, ku dziko limene ndidapatsa makolo ao, ndipo lidzakhaladi lao.”
4
Mau amene akunena za Israele ndi Yuda ndi aŵa:
5
“Tamva kulira kwankhaŵa, kufuula kwamantha, ndipo palibe mtendere paliponse.
6
Funsani kuti muzindikire, Kodi munthu wamwamuna angathe kubala mwana? Nanga nchifukwa chiyani ndikuwona munthu wamwamuna aliyense atagwira manja pa mimba ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira? Chifukwa chiyani nkhope zonse zagwa?
7
Kalanga ine! Tsiku limenelo nlalikulu kwambiri, sipadzakhala lina lofanana nalo. Idzakhala nthaŵi yamavuto kwa Yakobe, komabe adzapulumuka ku mavutowo.”
8
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Tsiku limenelo ndidzathyola goli laukapolo m'khosi mwao, ndidzadula zingwe zoŵamanga. Aisraele sadzakhalanso akapolo a alendo.
9
Azidzangotumikira Chauta, Mulungu wao, ndi Davide, mfumu yao, amene ndidzaŵasankhulira.
10
“Nchifukwa chake musachite mantha inu a m'banja la Yakobe, mtumiki wanga, musataye mtima inu Aisraele,” akuterotu Chauta. “Ndithu ndidzakupulumutsani kuchokera ku dziko lakutali. Ndidzapulumutsanso zidzukulu zanu kuchokera kudziko kumene ali mu ukapolo. Nonsenu mudzabwereranso, ndipo mudzakhala ndi mtendere popanda okuwopsani.
11
Ine ndili nanu, ndipo ndidzakupulumutsani,” akuterotu Chauta. “Ndidzaononga mitundu yonse ya anthu kumene ndidakubalalitsani, koma inu sindidzakuwonongani kotheratu. Ndidzakulangani potsata chilungamo, sindingakulekerereni osakulangani konse.”
12
Chauta akunena kuti, “Chilonda chanu nchosachizika, bala lanu nlonyeka.
13
Palibe amene angathe kukutetezani pa mlandu wanu. Palibe mankhwala opoletsa chilonda chanu. Palibe mankhwala ochiza nthenda yanu.
14
Abwenzi anu onse akuiŵalani, sakulabadiraninso. Ndakulangani mwankhanza, poti mlandu wanu ndi waukulu, machimo anu ndi ambiri.
15
Chifukwa chiyani mukudandaula nacho chilonda chanu? Bala lanu silingapole ai. Mlandu wanu ndi waukulu, machimo anu ngambiri, nchifukwa chake ndakuchitani zimenezi.
16
Tsono onse amene adakuwonongani inu, ndidzaŵaononga iwonso. Onse okuzunzani adzatengedwa ukapolo. Onse ofunkha zinthu zanu, nawonso zao zidzafunkhidwa. Ndipo onse okusakazani, ndidzachita zoti nawonso aŵasakaze.
17
Koma inuyo, ndidzachiza matenda anu, ndidzapoletsa mabala anu, chifukwa anthu ena amati ndinu otayika, amati, ‘Ndi anthu a ku Ziyoni aŵa, opanda oŵasamala,’ ” akuterotu Chauta.
18
Chauta akunena kuti, “Ndidzabwezeranso a banja la Yakobe ku dziko lao. Ndidzaonetsanso chikondi changa ku malo ake onse. Mzinda wa Yerusalemu uja udzamangidwanso pabwinja pake pompaja. Nyumba yaufumu idzamangidwanso pamalo pake.
19
Anthuwo adzaimba nyimbo zoyamika Chauta, ndipo padzamveka phokoso la chisangalalo. Ndidzaŵachulukitsa, sadzakhalanso oŵerengeka ai. Ndidzaŵapatsa ulemerero, ena sadzaŵanyozanso.
20
Ana ao adzakhalanso monga m'mene adaaliri kale. Mpingo wao wonse ndidzaukhazikitsanso Mwiniwakene. Ndidzalanga onse oŵazunza.
21
Wodzaŵalamulira adzakhala mmodzi mwa iwo. Mtsogoleri wao adzachokera pakati pao. Ineyo ndidzamkokera pafupi nane, ndipo iye adzayandikana nane. Ndanitu angalimbe mtima payekha kuti ayandikane ndi Ine?” Akutero Chauta.
22
“Motero inu mudzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu.
23
“Onani, mphepo yamkuntho ya Chauta! Mkuntho wamphamvu wa kamvulumvulu, ukuwomba pa mitu ya anthu olakwa.
24
Mkwiyo wa Chauta sudzachoka mpaka utatsiriza kuchita zonse zimene mtima wa Chautayo ukufuna. Mudzamvetsa zimenezi masiku akubwerawo.”
← Chapter 29
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 31 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52