bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 34
Jeremiah 34
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 35 →
1
Inalipo nthaŵi pamene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ndi gulu lake lankhondo, pamodzi ndi maufumu onse a pa dziko lapansi amene ankaŵalamulira, ndiponso anthu a mitundu yonse, ankathira nkhondo Yerusalemu ndi mizinda yake yozungulira. Nthaŵi imeneyo Chauta adauza Yeremiya kuti,
2
“Pita ukauze Zedekiya mfumu ya ku Yuda kuti Chauta akunena kuti Mzinda uwu ndidzaupereka kwa mfumu ya ku Babiloni, ndipo iyeyo adzautentha.
3
Iweyo sudzapulumuka m'manja mwake. Udzagwidwa ndithu ndipo adzakupereka m'manja mwake. Udzamuwona maso ndi maso, ndipo udzalankhula naye pakamwa ndi pakamwa. Tsono adzakutenga kupita nawe ku Babiloni.
4
Komabe imva mau a Chauta, iwe Zedekiya mfumu ya ku Yuda. Akuti, Sudzafera pa nkhondo.
5
Koma udzafera pa mtendere. Ndipo paja anthu ankafukiza lubani poika maliro a makolo ako akale, amene anali mafumu iweyo usanaloŵe ufumu, tsono nawenso podzaika maliro ako adzafukiza lubani. Pokuimbira nyimbo yamaliro azidzati, ‘Ogo nanu! Mbuyathu uja!’ Ndalankhula zimenezi ndine Mwiniwakene,” akuterotu Chauta.
6
Tsono zonsezi mneneri Yeremiya adakakambira Zedekiya, mfumu ya ku Yuda ku Yerusalemu.
7
Nthaŵi imeneyo nkuti gulu lankhondo la mfumu ya ku Babiloni likuthira nkhondo Yerusalemu ndi mizinda yotsala ya ku Yuda, Lakisi ndi Azeka. Imeneyi yokha ndiyo inali mizinda yamalinga yotsala ya ku Yuda.
8
Mau a Chauta adamvekanso kwa Yeremiya. Nthaŵiyo nkuti mfumu Zedekiya atapangana nawo anthu onse a ku Yerusalemu kuti alengeze zakuti akapolo ao adzaŵamasule.
9
Onse amene anali ndi akapolo Achihebri, aamuna kapena aakazi, aŵamasuledi. Sankayenera kumsunga mu ukapolo Myuda mnzao.
10
Akulu onse pamodzi ndi anthu wamba, atachita chipangano kuti akapolo aŵamasule, kuti asaŵasungenso mu ukapolo, zimenezi zidachitikadi ndipo adaŵamasula.
11
Komabe pambuyo pake adasintha maganizo ao. Amuna ndi akazi amene adaaŵamasula aja, adaŵagwiranso ukapolo.
12
Tsono Chauta adauza Yeremiya kuti
13
akalengeze kwa anthu mau a Chauta akuti, “Ndidachita chipangano ndi makolo anu pa tsiku limene ndidaŵatulutsa ku dziko la Ejipito ku nyumba ya ukapolo ija. Chipanganocho chidati:
14
Zaka zisanu ndi ziŵiri zitatha, aliyense mwa inu ammasule mu ukapolo Muhebri aliyense amene adadzigulitsa kwa inu nagwira ntchito zaka zisanu ndi chimodzi. Koma makolo anu sadandimve ndipo sadasamaleko konse.
15
Komabe masiku omwe apitaŵa mudatembenuka mtima ndipo nkuyamba kuchita zomwe ndimafuna Ine. Nonse mudamvana zoŵapatsa ufulu Aisraele anzanu. M'Nyumba imene imadziŵika ndi dzina langa mudalonjeza kuti mudzachitadi zimenezi.
16
Koma tsono mudasinthanso maganizo, ndipo mwaipitsa dzina langa. Nonsenu mudaŵagwiranso anthu amene mudaaŵamasula aja, nkuŵasandutsanso akapolo anu.”
17
Nchifukwa chake Chauta akunena kuti, “Simudandimvere, simudalengeze ufulu kuti mumasule abale ndi anansi anu. Chabwino! Ineyo tsono ndidzalengeza ufulu wina kwa inu, ufulu wake wa kufa ndi lupanga, mliri kapena njala. Ndidzakusandutsani chinthu chochititsa mantha pakati pa maufumu a pa dziko lapansi.
18
Simudasamale chipangano chimene mudachita ndi Ine, ndipo simudasunge lonjezo limene mudachita pamaso panga. Tsono Ine ndidzakusandutsani ngati mwanawang'ombe uja amene ankamdula paŵiri napita pakati pa zigawozo.
19
Amene ankadutsa pakati pa zigawo ziŵiriwo anali akulu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu, atsogoleri a boma, ansembe, ndiponso anthu a m'dzikomo.
20
Onsewo ndidzaŵapereka kwa adani ao ndi kwa amene amafuna kuŵapha. Ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame ndi nyama zakuthengo.
21
Ndidzapereka Zedekiya, mfumu ya ku Yuda, pamodzi ndi nduna zake, kwa adani ao amene amafuna kuŵapha, ndiye kuti kwa gulu lankhondo la mfumu ya ku Babiloni limene nthaŵi ino layamba kubwerera m'mbuyo.
22
Koma ndidzaŵalamula, ndidzaŵabwezeranso ku mzinda uno. Adzauthira nkhondo ndi kuulanda, ndipo adzautentha. Motero mizinda ya Yuda ndidzaisandutsa chipululu, mopanda anthu.”
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 35 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52