bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 20
Jeremiah 20
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 21 →
1
Wansembe Pasuri, mwana wa Imeri, amene anali kapitao wamkulu ku Nyumba ya Chauta, adamva Yeremiya akulosa zinthu zimenezi.
2
Tsono Pasuri adalamula kuti anthu amenye mneneri Yeremiya ndi kumuika m'ndende ku chipata cha Benjamini, ku Nyumba ya Chauta.
3
M'maŵa mwake Pasuri adatulutsa Yeremiya m'ndende, ndipo Yeremiya adauza Pasuri kuti, “Chauta sakutchulanso dzina loti Pasuri, koma loti ‘Zoopsa pa mbali zonse.’
4
Paja Chauta akunena kuti: Ndidzakusandutsa choopsa kwa mwiniwakewe, ndiponso kwa abwenzi ako onse. Abwenzi akowo adani ao adzaŵapha ndi lupanga, iweyo ukupenya. Ndipo Yuda yense ndidzampereka kwa mfumu ya ku Babiloni. Ena adzaŵatenga ukapolo kupita nawo ku Babiloni, ndipo ena adzaŵapha ndi lupanga.
5
Chuma chonse chamumzindamu, phindu lonse la ntchito yake, zinthu zonse za mtengo wapatali ndi chuma cha mafumu a ku Yuda, zonsezo ndidzazipereka kwa adani ao. Iwowo adzafunkha zimenezi ndi kupita nazo ku Babiloni.
6
Ndipo iwe Pasuri ndi onse a pabanja pako, nanunso adzakutengani ukapolo kupita nanu ku Babiloni. Mudzafera komweko ndi kuikidwa komweko, iweyo pamodzi ndi abwenzi ako amene unkaŵalosera zabodza.”
7
Inu Chauta, mwandipusitsa ine, ndipo ndapusadi. Inu ndinu amphamvu kuposa ine, ndipo mwandipambana. Aliyense akundiseka tsiku lonse, aliyense akundinyodola kosalekeza.
8
Ndikamalankhula, ndimakweza mau, ndimafuula kuti, “Ndeu kuno, taonongeka!” Mau anu, Inu Chauta, andisandutsa wonyozeka ndi wonyodoledwa masiku onse.
9
Ndikanena kuti, “Sindidzalalikanso za Chauta, sindidzalankhulanso m'dzina lake,” mau anu, Inu Chauta, amayaka ngati moto mumtima mwanga. Ndimayesa kuŵasunga m'kati, koma pambuyo pake ndimaŵatulutsa popeza kuti sindingathe kupirira.
10
Ndimamva ambiri akunong'ona. Zoopsa zili pa mbali zonse! Amati, “Kamnenezeni! Tiyeni tikamneneze!” Amene adaali abwenzi anga amayembekeza kuti ndigwa pansi, amati, “Mwina mwake adzatha kunyengedwa, tsono ife tidzamgwira ndi kulipsira pa iyeyo.”
11
Koma Chauta ali nane, ndiye wankhondo woopsa. Nchifukwa chake anthu ondizunza adzakhumudwa, ndithu sadzandipambana. Adzachita manyazi kwambiri, chifukwa cha kundilepherako, ndipo manyazi aowo sadzaiŵalika konse.
12
Inu Chauta Wamphamvuzonse, amene mumaweruza anthu molungama, amene mumapenya zamumtima, ndikupereka mlandu wanga kwa Inu. Ndikukupemphani kuti mundilipsirire adani anga.
13
Imbirani Chauta, mtamandeni Chauta! Ndiye amapulumutsa osauka kwa adani ao.
14
Litembereredwe tsiku limene ndidabadwa. Lisatamandidwe tsiku limene mai wanga adandibala.
15
Tsoka kwa iye amene adakasangalatsa bambo wanga ndi uthenga woti, “Kunyumba kwanu kwabadwa mwana wamwamuna.”
16
Munthu ameneyo akhale ngati mizinda imene adaiwononga Chauta mopanda chifundo ija. Amve kulira kwa kupweteka m'maŵa, ndiponso phokoso la nkhondo masana,
17
chifukwa choti sadandiphere m'mimba, kuti mai wanga asanduke manda anga, ndipo kuti mimba yake ikhale chitupire.
18
Kodi chifukwa chiyani ndidabadwa? Kodi ndidabadwira mavuto ndi chisoni, kuti moyo wanga ukhale wa manyazi okhaokha?
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52