bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 16
Jeremiah 16
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 17 →
1
Chauta adandiwuza kuti,
2
“Usadzakwatire, usadzabale ana aamuna kapena aakazi ku malo ano.
3
Ndithu kunena za ana aamuna kapena ana aakazi obadwira kuno, kapenanso za amai ao ndi atate ao amene adabereka anawo m'dziko muno,
4
onsewo adzafa ndi nthenda zoopsa. Sadzaŵalira maliro kapena kuŵaika m'manda. Adzakhala ngati ndoŵe yotayikira pansi. Ena adzafera pa nkhondo, ena adzafa ndi njala. Ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame ndi zilombo zakuthengo.”
5
Chauta akunena kuti, “Usaloŵe m'nyumba ya maliro. Usaloŵemo kuti ukalire kapena kutonthoza anthu, pakuti ndaŵachotsera mtendere wanga. Ndachotsanso chikondi changa chosasinthika ndiponso chifundo changa.
6
Akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe, onsewo adzafa m'dziko lino. Koma maliro ao sadzaikidwa, iwowo sadzaŵalira. Palibe amene adzaonetse chisoni podzichekacheka kapena kumeta tsitsi chifukwa cha malirowo.
7
Palibe amene adzapatse chakudya munthu wolira kuti amtonthoze chifukwa cha akufawo. Sadzamupatsa chakumwa kuti amtonthoze, ngakhale amwalire atate ake kapena amai ake.
8
“Usadzaloŵe m'nyumba m'mene muli phwando, kuti udye nao ndi kumwa nao,”
9
Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, “Pa nthaŵi yanu yomwe, ndiponso pa malo omwe ano ndidzathetsa mau achisangalalo ndi achimwemwe, ndipo ndidzachotsa liwu la mkwati wamwamuna ndi la mkwati wamkazi inuyo mukuwona.
10
“Tsono ukadzaŵauza anthuwo mau ameneŵa, makamaka adzakufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani Chauta wanena kuti tsoka lotere lidzatigwera ifeyo? Kodi tidalakwanji? Kodi Inu Chauta, Mulungu wathu, takuchimwirani chiyani?’
11
Tsono iwe udzayankhe kuti, ‘Nchifukwa chakuti makolo anu adandisiya Ine,’ akuterotu Chauta. ‘Adatsata milungu ina, namaitumikira ndi kumaipembedza. Adandisiya Ine, ndipo sadamvere malamulo anga.
12
Komanso inu mudachimwa koposa kupambana makolo anu: aliyense mwa inu akutsata zoipa ndi mtima wake wokanika, m'malo momandimvera Ine.
13
Motero Ine ndidzakupirikitsani m'dziko lino ndi kukuloŵetsani m'dziko limene inu ndi makolo anu simulidziŵa. Kumeneko mudzatumikira milungu ina usana ndi usiku, chifukwa Ine sindidzakuchitiraninso chifundo.’ ”
14
Nchifukwa chake Chauta akunena kuti, “Masiku akubwera pamene anthu polumbira sazidzatinso, ‘Pali Chauta wamoyo, amene adatulutsa Aisraele ku dziko la Ejipito!’
15
Koma azidzati, ‘Pali Chauta wamoyo, amene adatulutsa Aisraele ku dziko lakumpoto, ndi ku maiko konse kumene adaŵabalalitsira!’ Ndithu ndidzaŵabwezera ku malo amene ndidapatsa makolo ao.”
16
Chauta akuti, “Ndidzaitana adani ambiri okhala ngati asodzi a nsomba, ndipo adzaŵagwira anthuŵa ngati nsomba. Pambuyo pake ndidzaitana adani enanso ambiri okhala ngati alenje, kuti akaŵasake anthuŵa ku mapiri, ku zitunda, ndiponso m'mapanga am'matanthwe.
17
Maso anga amaona makhalidwe ao onse oipa, ndi osabisika pamaso panga. Palibenso tchimo lililonse limene sindikulidziŵa.
18
Ndidzaŵalanga moŵirikiza, chifukwa cha kuipa kwao ndi machimo ao. Ndidzatero chifukwa chakuti aipitsa dziko langa ndi mafano ao amene ali ngati mitembo, ndipo dziko limene lili choloŵa changa adalidzaza ndi mafano ao onyansa.”
19
Inu Chauta, ndinu mphamvu zanga ndi linga langa, ndinu pothaŵira panga pa nthaŵi ya mavuto. Anthu a mitundu yonse adzabwera kwa Inu kuchokera ku malire onse a dziko lapansi. Adzati, “Makolo athu anali ndi milungu yonama, anali ndi mafano achabechabe opanda phindu.
20
Kodi munthu nkudzipangira milungu yeniyeni? Atati apange, singakhale milungu konse.”
21
Chauta akuti, “Nchifukwa chake ndidzaŵaphunzitsa, ndidzaŵaphunzitsa kokha kano kuti adziŵe mphamvu zanga zopambana. Ndithudi adzadziŵa kuti Ine dzina langa ndine Chauta.”
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 17 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52