bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 51
Jeremiah 51
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 50
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 52 →
1
Chauta akunena kuti, “Ndidzautsa mphepo yoti idzaononge Babiloni pamodzi ndi onse okhala m'dziko la Babiloni.
2
Ndidzatuma alendo ku Babiloni, kuti adzampepete ndi kuseseratu zonse zokhala m'dziko lake. Iwowo adzamuukira pa mbali zonse nthaŵi ya zoopsayo.
3
Okoka uta musaŵalekerere, kapena onyadira chovala chao chankhondo. Anyamata ake musasiyeko ndi mmodzi yemwe. Ankhondo ake onse muŵaononge.
4
Adzavulazidwa ndi kufera m'dziko lonse ndi m'miseu ya mzinda wao womwe.
5
Israele ndi Yuda sadasiyidwe ndi Mulungu wao, Chauta Wamphamvuzonse. Koma dziko la Ababiloni nlodzaza ndi machimo, machimo ake onyoza Woyera uja wa Israele.
6
“Aliyense mwa inu athaŵe, achoke ku Babiloni kuti apulumutse moyo wake. Musaphedwe naye pamodzi pamene adzalandira chilango chake. Limeneli ndilodi tsiku limene Chauta adzaŵalanga, ndipo adzaŵalipsira kwathunthu.
7
Pajatu Babiloni anali ngati chikho chagolide m'manja mwa Chauta, kuti aledzeretse dziko lonse lapansi. Mitundu yambiri ya anthu idamwako vinyo wake, nchifukwa chake idapenga.
8
Babiloni wagwa mwadzidzidzi ndipo waonongeka. Mlireni, mfunireni mankhwala, kuti mwina nkuchira.
9
Ena adati, ‘Tidayesa kumpatsa mankhwala koma sadachire. Tiyeni tingomsiya, timchokere ndipo aliyense apite ku dziko lakwao. Paja mlandu wake wafika mpaka kumwamba, wafika mpaka ku mlengalenga.’ ”
10
Tsono Chauta waonetsa poyera kuti ifeyo ndife osalakwa. Tiyeni tilengeze ku Ziyoni zimene Chauta, Mulungu wathu, watichitira.
11
“Songolani mivi, tengani zishango.” Chauta wautsa mitima ya mafumu a Amedi, poti cholinga chake nchoti aononge Babiloni. Afuna kumlipsira chifukwa choononga Nyumba yake.
12
Kwezani mbendera yankhondo ndipo muwononge malinga a Babiloni. Mulimbitse oteteza, muike alonda, mukonzekere kulalira. Pakuti Chauta watsimikiza, ndipo adzachitadi zimene adanena za anthu a ku Babiloni.
13
Inu amene muli ndi mitsinje yambiri, ndinu olemera kwambiri, koma chimalizo chanu chafika, moyo wanu watha.
14
Chauta Wamphamvuzonse adalumbira pali Iye yemwe mwini wake kuti, “Ndidzatuma anthu osaŵerengeka ngati dzombe kuti adzakuthireni nkhondo, ndipo adzafuula, kuwonetsa kuti apambana.”
15
Chauta ndiye amene adalenga dziko lapansi ndi mphamvu zake. Ndiye amene adapanga zonse ndi nzeru zake, ndipo ndi umisiri wake adayala thambo lakumwamba.
16
Iye akalankhula, kumamveka mkokomo wa madzi kumwamba, ndiye amene amadzetsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi. Amang'animitsa mphezi za mvula, amakunthitsa mphepo kuchokera kumene amaisunga.
17
Anthu onse ndi opusa, alibe nzeru. Mmisiri aliyense wosula amachita manyazi ndi mafano ake. Mafano amene amapangawo ngabodza, mwa iwo mulibe konse moyo.
18
Mafanowo ngachabechabe, oyenera kuŵaseka, ndipo pamene anthuwo adzalangidwe, mafanowo adzaonongedwa.
19
Koma Mulungu wa Yakobe sali ngati mafanowo, Iye ndiyedi Mlengi wa zonse. Aisraele ndi anthu ake amene Iye adaŵasankha, dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse.
20
Iwe Babiloni ndiwe nyundo yanga, chida changa chankhondo: ndi iwe ndimaphwanyaphwanya mitundu ya anthu, ndimaononga maufumu.
21
Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya akavalo ndi okwerapo ao. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya magaleta ndi oyendetsa ake.
22
Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya amuna ndi akazi ao. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya nkhalamba ndi achinyamata. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya anyamata ndi anamwali.
23
Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya abusa ndi ziŵeto zao. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya alimi ndi ng'ombe zao. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya abwanamkubwa ndi atsogoleri ankhondo.
24
“Inu mukupenya, ndidzalipsira Babiloni ndi onse okhalamo chifukwa cha zolakwa zonse zimene adachita ku Ziyoni,” akutero Chauta.
25
“Ndikukuimba mlandu, iwe phiri loononga, iwe amene umasakaza dziko lonse lapansi. Ndidzasamula dzanja langa pofuna kukulanga, ndi kukugubuduzira kunsi kuchokera pa mathanthwe ako. Ndidzakusandutsa phiri lopserera.
26
Palibe mwala wako ndi umodzi womwe umene adzabwere nawo kuti augwiritse ntchito ngati mwala wapangodya. Iwe udzakhala chipululu mpaka muyaya,” akutero Chauta.
27
“Kwezani mbendera yankhondo pa dziko, lizani lipenga kuti mitundu ya anthu imve. Itanani mitundu yonse kuti imuthire nkhondo Babiloni. Itanani maufumu a ku Ararati, a ku Mini ndi a ku Asikenazi. Ikani mtsogoleri wankhondo kuti amenyane ndi Babiloniyo. Mubweretse akavalo ochuluka ngati dzombe.
28
Sonkhanitsani mitundu ya anthu kuti imuthire nkhondo. Muitane mafumu a ku Medi, pamodzi ndi abwanamkubwa ndi nduna zao, ndiponso ankhondo a m'maiko onse amene amaŵalamulira.
29
Dziko likunjenjemera, likuphiriphitha chifukwa cha kupweteka, chifukwa zimene Chauta adakonzera Babiloni zidzachitikadi, zakuti adzamsandutsa dziko lachipululu lopanda anthu.
30
Ankhondo a ku Babiloni aleka kuponya nkhondo, angokhala khale m'malinga ao. Mphamvu zao zatha, asanduka ngati akazi. Nyumba zake zatenthedwa, mipiringidzo ya zipata zake yathyoka.
31
Othamanga akungopezanapezana, amithenganso akungotsatanatsatana. Onsewo akukauza mfumu ya ku Babiloni kuti mbali zonse za mzinda wake zalandidwa.
32
Madooko onse alandidwa, malo obisalako alonda atenthedwa, ndipo ankhondo ake onse asokonezeka.
33
Babiloni wokongola uja wangokhala ngati popunthira tirigu pa nthaŵi yopuntha kumene. Ndipotu posachedwa nthaŵi yake yokolola ifika,” akutero Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele.
34
A ku Yerusalemu akuti, “Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, watiwononga, Watitswanya ndi kutitaya ngati mbiya yopanda kanthu. Watimeza ngati ng'ona. Wakhuta ndi zakudya zathu zotsekemera, kenaka nkutilavula.”
35
Anthu okhala m'Ziyoni anene kuti, “Zankhanza zimene Ababiloni adatichita ife ndi ana athu ziŵabwerere.” Anthu okhala mu Yerusalemu anene kuti, “Magazi athu amene adamwazika aŵagwere Ababiloniwo ngati chilango chao.”
36
Nchifukwa chake Chauta akunena kuti, “Ndidzakumenyera nkhondo yako, ndipo ndidzakulipsirira. Ndidzaumitsa nyanja ya ku Babiloni, akasupe ake onse adzaphwa.
37
Motero Babiloni adzasanduka mulu wa nyumba zopasuka, malo a nkhandwe, malo oopsa ndi onyozeka, opanda wina wokhalamo.
38
“Ababiloni adzakhuluma ngati mikango. Adzadzuma ngati ana a mikango.
39
Akachita dyera, ndidzaŵakonzera madyerero. Tsono ndidzaŵaledzeretsa, ndipo adzasangalala nkugona tulo tampakampaka, osadzukanso ai.
40
Ndidzapita nawo kuti akaphedwe ngati anaankhosa, ngati nkhosa zamphongo kapena atonde,” akutero Chauta.
41
“Ndithu Babiloni wagonjetsedwa, mzinda umene dziko lonse lapansi linkaunyadira walandidwa. Ogo! Babiloni uja wasanduka chinthu chonyansa pakati pa mitundu ya anthu!
42
Nyanja yakwera mpaka kumiza Babiloni, waphimbidwa ndi mafunde ake.
43
Mizinda yake yasanduka malo onyansa, dziko louma ndi lachipululu, dziko lopanda anthu losayendako mwanawamunthu.
44
Ndidzalanga Beli, mulungu wa Ababiloni, ndidzamsanzitsa zimene adameza. Mitundu ya anthu sidzapitanso kwa iye. Malinga a Babiloni agwa!
45
Tulukani m'Babiloni, inu anthu anga! Fulumirani, pulumutsani moyo wanu! Thaŵani mkwiyo woopsa wa Chauta!
46
Musataye mtima. Musaope maphephe amene awanda m'dziko monse. Chaka ndi chaka pamabuka ndithu maphephe onena za nkhondo pa dziko lapansi, ndiponso zakuti mfumu yakutiyakuti ikumenyana ndi inzake.
47
“Tsono ikudza nthaŵi pamene ndidzalange mafano a Babiloni. Dziko lonselo lidzachita manyazi. Anthu ake onse ophedwa adzakhala ali ngundangunda pakati pake.
48
Pambuyo pake dziko lakumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zokhala m'menemo zidzaimba mokondwera chifukwa cha kugwa kwa Babiloni. Anthu oononga ochokera kumpoto adzamgonjetsa,” akutero Chauta.
49
Babiloni ayeneradi kugwa chifukwa cha amene adaphedwa ku Israele, monga adagwera anthu a pa dziko lonse lapansi amene adaphedwa ndi iyeyo.
50
“Inu amene mwapulumuka ku nkhondo ya Babiloni, chokanipo apa, musazengereze. Kumbukirani Chauta ngakhale muli kutali ndi kwanu, muzimkumbukira Yerusalemu.
51
Inu mukuti ‘Tikuchita manyazi chifukwa cha manyozo amene talandira. Nkhope zathu zagwa chifukwa anthu achilendo aloŵa ku mabwalo opatulika a ku Nyumba ya Chauta.’ ”
52
Koma Chauta akunena kuti, “Ikubwera nthaŵi pamene ndidzalange mafano a ku Babiloni, ndipo kubuula kwa anthu olasidwa kudzamveka m'dziko lake lonse.
53
Ngakhale Babiloni adzikweze mpaka ku mlengalenga, nkulimbitsa nsanja zake, ndidzatuma oononga kuti amgonjetse,” akutero Chauta.
54
“Imvani mau olira m'Babiloni. Imvani phokoso la kuwonongeka kwakukulu m'dziko la Ababiloni.
55
Ndithu, Chauta akuwononga Babiloni, ndipo akuthetsa phokoso lake lalikulu. Mfuu wa anthu ake ukumveka ngati mafunde amkokomo, phokoso lake likukwererakwerera.
56
Woononga amufikira Babiloni, ndipo ankhondo ake onse agwidwa, mauta ao athyoka. Pajatu Chauta ndi Mulungu wolanga, adzabwezeradi kwathunthu zoipa zao.
57
Ndidzaledzeretsa akuluakulu ake pamodzi ndi anzeru ake. Ndidzaledzeretsa abwanamkubwa ake, atsogoleri ankhondo, ndi ankhondo ake amene. Adzagona tulo tampakampaka, tosadzuka nato,” ikutero mfumu imene dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse.
58
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Malinga aakulu a Babiloni adzasalazidwa. Zipata zake zazitali zidzatenthedwa. Mitundu ya anthu idagwira ntchito pachabe, anthu adangotopa nkumanga zimene tsopano zikupsa ndi moto.”
59
Mfumu Zedekiya anali ndi phungu wake wamkulu, dzina lake Seraya, mwana wa Neriya, mdzukulu wa Maseiya. Pa chaka chachinai cha ufumu wa Zedekiya ku Yuda, Seraya adatsagana ndi mfumuyo kupita ku Babiloni. Tsono mneneri Yeremiya adampatsirako uthenga Serayayo.
60
Yeremiya anali atalemba m'buku za chiwonongeko chonse cha Babiloni, ndiponso za zina zonse zokhudza Babiloni.
61
Yeremiyayo adauza Seraya kuti, “Pamene ukafike ku Babiloni, usakalephere kuŵaŵerengera anthu mau onseŵa.
62
Ukanene kuti, ‘Inu Chauta, mwalengeza cholinga chanu chofuna kuwononga malo ano, osasiyapo kanthu, munthu kapena nyama. Ndipo adzakhala chipululu mpaka muyaya.’
63
Ukakatha kuŵerenga bukulo, ukalimangire ku mwala, nkuliponya mu mtsinje wa Yufurate.
64
Ndipo ukanene kuti, ‘Umu ndimo m'mene Babiloni adzamirire. Sadzadzukanso chifukwa cha zoopsa zonse zimene ndidzamgwetsere.’ ” Mau a Yeremiya athera pamenepa.
← Chapter 50
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 52 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52