bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 23
Jeremiah 23
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 24 →
1
“Tsoka kwa abusa amene amaononga ndi kumwaza nkhosa za pabusa panga,” akutero Chauta.
2
Nchifukwa chake Chauta, Mulungu wa Israele, ponena za abusa oyang'anira anthu ake, akuti, “Mwabalalitsa ndi kumwaza nkhosa zanga, simudazisamale bwino. Choncho ndidzakulangani chifukwa cha machimo anu.
3
Pambuyo pake Mwiniwakene ndidzasonkhanitsa nkhosa zanga zotsala, kuzichotsa ku malo onse amene ndidazimwazira. Ndidzazibwezera ku busa lakwao, ndipo zidzaswana ndi kuchuluka.
4
Ndidzazipatsa abusa oziŵeta bwino. Sizidzaopanso kapena kuchita mantha, kapena kusokera,” akuterotu Chauta.
5
Chauta akunena kuti, “Akubwera masiku pamene ndidzaphukitsira Davide nthambi yoongoka imene idzakhala mfumu yanzeru ndi yoweruza m'dzikomo mwachilungamo ndi mosakondera.
6
Pa masiku akewo Yuda adzapulumuka, ndipo Israele adzakhala pabwino. Adzamutcha dzina ili lakuti, ‘Chauta ndiye chilungamo chathu.’ ”
7
Chauta akunena kuti, “Akubwera masiku pamene anthu polumbira sazidzatinso, ‘Pali Chauta wamoyo, amene adatulutsa Aisraele ku dziko la Ejipito!’
8
Koma azidzati, ‘Pali Chauta wamoyo, amene adatulutsa Aisraeli ku dziko lakumpoto, ndi ku maiko konse kumene adaŵabalalitsira.’ Ndithu ndidzaŵabwezera ku malo amene ndidapatsa makolo awo.”
9
Kunena za aneneri, mtima wanga wasweka, m'nkhongono mwachita kuti zii! Ndakhala ngati munthu woledzera, munthu wosokonezeka ndi vinyo, chifukwa cha Chauta ndi mau ake oyera.
10
Dziko lino ladzaza ndi anthu achigololo. Chifukwa cha temberero la Chauta m'dziko mwagwa chilala, mabusa akuchipululu auma. Amene amangothamangira zoipa, amalimbikira kuchita zosalungama.
11
“Zoonadi, aneneri ndiponso ansembe, onsewo saopa Mulungu. Ndaŵapeza akuchita zoipa ngakhale m'Nyumba mwanga,” akutero Chauta.
12
“Nchifukwa chake njira zao zidzakhala zoterera. Adzaŵapirikitsira kumdima kumene akagwe. Ndidzaŵaonetsa ndoza pa nthaŵi ya chilango chao,” akuterotu Chauta.
13
“Pakati pa Aneneri a ku Samariya ndaonapo choipa ichi: ankalosa m'dzina la Baala, motero adasokeza anthu anga Aisraele.
14
Pakati pa aneneri a ku Yerusalemunso ndaonapo chinthu choopsa kwambiri: amachita zigololo, amanena bodza, ndipo amalimbitsa mtima anthu ochita zoipa, kotero kuti palibe amene amaleka machimo ake. Kwa Ine onsewo ali ngati anthu a ku Sodomu ndi Gomora.”
15
Chifukwa cha zimenezi, ponena za aneneri ameneŵa, Chauta akuti, “Ndidzaŵadyetsa dzoŵaŵa ndi kuŵamwetsa madzi azumu, chifukwa zoipa zimene zaŵanda m'dziko lonse zachokera kwa aneneri omweŵa.”
16
Chauta Wamphamvuzonse akuuza anthu kuti, “Musamvere zimene akunena aneneri, iwowo amakuloserani zonyenga. Zimene amakuuzani kuti akuziwona m'masomphenya ndi maganizo ao chabe, si zolankhula Chauta ai.
17
Saleka kuŵauza amene amandinyoza Ine kuti, ‘Zinthu zidzakuyenderani bwino.’ Ndipo amene amaumirira kutsata zofuna za mtima wao amaŵauza kuti, ‘Simudzaona vuto ai.’ ”
18
Ine ndidati, “Mwa aneneriwo ndani amene adakhala nao m'bungwe la Chauta? Ndani adamuwona ndi kumva mau ake? Ndani mwa iwo adasamalako mau ake ndi kuŵamvera?
19
Onani mphepo yamkuntho yochokera kwa Chauta! Onani ukali wake woomba ngati namondwe, udzaomba pa mitu ya anthu oipa.
20
Mkwiyo wa Chauta sudzaleka, mpaka atachita zonse zimene adatsimikiza mumtima mwake. Zimenezi mudzazidziŵa masiku akubweraŵa.”
21
Chauta adati, “Aneneri ameneŵa sindidaŵatume ndine, komabe ankathamanga uku ndi uku ndi mithenga yao. Sindidalankhule nawo, komabe ankalosa.
22
Akadakhala nane pa bungwe langa, bwenzi atalalikadi mau anga kwa anthu anga. Bwenzi ataŵachotsa m'njira zao zoipa, kuti aleke machimo ao.”
23
Chauta akuti, “Kodi ndimakhala Mulungu pokhapokha ndikakhala pafupi, koma ndikakhala patali ndiye kuti sindinenso Mulungu?
24
Kodi munthu nkubisala pobisika potani, pamene Ine sindingathe kumuwona? Kodi Ine sindili ponseponse, kumwamba ndi pa dziko lapansi pano?” Akuterotu Chauta.
25
“Ndamva zimene aneneri akulankhula, aneneri amene akulosa zabodza m'dzina langa, nkumafuula kuti, ‘Ndalota, ndalota.’
26
Kodi zabodzazi adzazisunga mumtima mwao mpaka liti aneneri onamaŵa, amene amalosa zonyenga za mumtima mwao?
27
Aneneri ameneŵa amakhulupirira kuti anthu anga adzandiiŵala akamamva zamalotozo, monga momwe makolo ao adaiŵalira dzina langa pomapembedza Baala.
28
Ngati mneneri walota maloto, afotokoze maloto akewo. Koma amene ali ndi mau anga, alalike mau angawo moona. Kodi mungu ungafanane ndi tirigu?” Akuterotu Chauta.
29
“Kodi suja mau anga amatentha ngati moto? Kodi suja mau anga ali ngati nyundo imene imaphwanya thanthwe?
30
“Nchifukwa chake ndikuŵakana aneneri amene amaberana mau iwo okhaokha nkumati mauwo ndi a Ineyo.
31
Ndikuŵatsutsa aneneri amene amakonda kulankhula zamabodza, namanena kuti, ‘Ameneŵa ndiwo mau a Chauta.’
32
Ndikuŵakana aneneri amene amalota zabodza, namasimbira anthu anga ndi kumaŵasokeza ndi mabodza aowo. Sindidaŵatume ndine kapena kuŵalamula, ndipo sathandiza anthu mpang'ono pomwe,” akuterotu Chauta.
33
Chauta adauza Yeremiya kuti, “Anthu ameneŵa, kaya ndi mneneri, kaya ndi wansembe, akakufunsa kuti, ‘Kodi uthenga wolemetsa wa Chauta ukuti chiyani?’ Udzayankhe kuti, ‘Inuyo ndiye katundu wolemetsa Chauta, ndipo adzakutayani,’ akuterotu Chauta.
34
Ndipo mneneri, wansembe, kapena munthu wina aliyense, wonena kuti, ‘Nawu uthenga wolemetsa wa Chauta,’ ameneyo ndidzamulanga pamodzi ndi banja lake.
35
Koma mau amene aliyense azifunsa mnzake kapena mbale wake akhale akuti, ‘Kodi Chauta wanena zotani?’
36
Koma musanenanso kuti ‘Nawu uthenga wolemetsa wa Chauta.’ Uthenga wa aliyense ndi mau a iye mwini, motero inuyo mudapotoza mau a Mulungu wamoyo, Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wathu.
37
Tsono iwe Yeremiya udzamufunse mneneri kuti, ‘Kodi Chauta wayankha zotani?’ Kapena kuti, ‘Kodi Chauta wanena zotani?’
38
Koma ngati munena kuti, ‘Nawu uthenga wolemetsa wa Chauta,’ Chautayo akuti, ‘Popeza kuti mwanena mau akuti nawu uthenga wolemetsa wa Chauta, pamene ndidakuuzani kuti musanene mau ameneŵa,
39
pamenepo Ine mwini ndidzakunyamulani ngati katundu wolemetsa nkukutayani kutali. Ndidzakuchotsani pamaso panga inuyo pamodzi ndi mzinda umene ndidakupatsani inu ndi makolo anu.
40
Ndidzakunyozani mpaka muyaya, ndikakuchititsani manyazi osaiŵalika.’ ”
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 24 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52