bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 27
Jeremiah 27
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 28 →
1
Pamene Zedekiya, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda adayamba kulamulira, Chauta adalankhula ndi Yeremiya namuuza kuti,
2
“Tenga nsinga zachikopa ndi mitengo ya goli, uzimange m'khosi mwako.
3
Tsono utumize uthenga kwa mafumu a ku Edomu, Mowabu, Amoni, Tiro ndi Sidoni, kudzera mwa amithenga amene abwera ku Yerusalemu kwa Zedekiya, mfumu ya ku Yuda.
4
Uŵauze kuti akadziŵitse atsogoleri ao kuti Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuuza atsogoleriwo kuti:
5
Ndidalenga dziko lapansi ndi mphamvu zanga ndi nyonga zanga. Ndidalenga anthu ndi nyama pa dziko lapansi, ndipo ndimalipereka kwa amene ndimamuwona kuti ndi woyenera.
6
Tsopano ndapereka maiko onseŵa kwa Nebukadinezara mtumiki wanga, mfumu ya ku Babiloni. Ndampatsanso nyama zonse zakuthengo kuti zizimtumikira.
7
Anthu a mitundu yonse adzamtumikira iyeyo, mwana wake ndi mdzukulu wake, mpaka itakwana nthaŵi yoti dziko lake liwonongedwe. Pamenepo anthu a mitundu yambiri ndi mafumu amphamvu adzagonjetsa ufumu wakewo.
8
“Koma ngati anthu a mtundu wina uliwonse kapena a dziko lina lililonse adzakana kutumikira Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, kapena kugonjera ulamuliro wake, Ineyo ndidzaŵalanga ndi nkhondo, njala ndi mliri, mpaka nditaŵapereka m'manja mwake kotheratu,” akuterotu Chauta.
9
“Nchifukwa chake musaŵamvere aneneri anu, oombeza anu, otanthauza maloto, amaula ndi amatsenga anu, akamakuuzani kuti musadzatumikire mfumu ya ku Babiloni.
10
Ndithudi, amakuloserani zabodza, kotero kuti adani adzakuchotsani m'dziko lanu, kupita nanu kutali. Ndidzakupirikitsani ndipo mudzaonongeka.
11
Koma mtundu wina uliwonse umene udzagonjera mfumu ya ku Babiloni ndi kumaitumikira, ndidzausiya kuti ukhale m'dziko lake, kuti uzilima ndi kumakhala kumeneko,” akuterotu Chauta.
12
“Mau okhaokhawo ndidauzanso Zedekiya mfumu ya ku Yuda, ndidati: Mugonjere ulamuliro wa mfumu ya ku Babiloni ndi kumaitumikira iyoyo pamodzi ndi anthu ake. Mukatero mudzapulumutsa moyo wanu.
13
Nanga iweyo ndi anthu ako, muferenji ndi nkhondo, njala ndi mliri, zimene Chauta waopsera mtundu wina uliwonse wosatumikira mfumu ya ku Babiloni?
14
Musaŵamvere aneneri okuuzani kuti musadzatumikire mfumu ya ku Babiloni. Akukuloserani zabodza.
15
Sindidaŵatume ndine, ngakhale iwowo akuti amalosa m'dzina langa. Motero ndidzakupirikitsani, ndipo mudzaonongeka inuyo pamodzi ndi aneneri amene amakuloseraniwo.
16
“Pambuyo pake ndidauza ansembe pamodzi ndi anthu ena onse kuti Chauta akunena kuti: Musaŵamvere aneneri anu amene amakuuzani kuti, ‘Ziŵiya za ku Nyumba ya Chauta adzazibwezanso mwamsanga kuchokera ku Babiloni.’ Iwowo akungokuloserani zabodza.
17
Musaŵamvere, muzitumikira mfumu ya ku Babiloni ndipo mupulumutse moyo wanu. Chifukwa chiyani mzindawu usanduke bwinja?
18
Ngati iwo ndi aneneridi ndipo ngati ali ndi mau a Chauta, apemphere kwa Chauta Wamphamvuzonse kuti ziŵiya zimene zidatsala m'Nyumba ya Chauta ndiponso m'nyumba ya mfumu ku Yerusalemu zisatengedwe kupita ku Babiloni.
19
Chauta Wamphamvuzonse ndiye akunena za mizati, chimbiya, maphaka ndi ziŵiya zonse zimene zidatsala mumzindamu.
20
Zimenezi Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni sadazitenge pa nthaŵi imene ankatenga ukapolo Yehoyakini mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda, kuchoka naye ku Yerusalemu kupita naye ku Babiloni pamodzi ndi atsogoleri a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu.
21
Zoonadi, ameneŵa ndiwo mau a Chauta Wamphamvuzonse onena za ziŵiya zimene zidatsala m'Nyumba ya Chauta, m'nyumba ya mfumu ya ku Yuda ndiponso mu Yerusalemu, akuti,
22
‘Zidzatengedwa kupita ku Babiloni. Ndipo zidzakhala kumeneko mpaka tsiku limene ndidzazikumbukenso. Apo ndidzazitenganso ndi kudzazibwezanso ku malo ano,’ ” akuterotu Chauta.
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 28 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52