bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 28
Jeremiah 28
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 29 →
1
Chaka chomwecho mwezi wachisanu wa chaka chachinai, Zedekiya ataloŵa ufumu wa ku Yuda, Hananiya mwana wa Azuri mneneri wa ku Gibiyoni, adalankhula nane ku Nyumba ya Chauta. Ansembe ndi anthu onse alikumva, iye adati,
2
Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, “Ndathyola goli laukapolo la mfumu ya ku Babiloni.
3
Zisanathe zaka ziŵiri, ndidzabwezera ziŵiya zonse za ku Nyumba yanga ku malo ano, zimene Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adazichotsa kuno kupita nazo ku Babiloni.
4
Ndidzambwezanso ku malo ano Yehoyakini, mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda. Ndidzabweza akapolo onse ochokera ku Yuda amene adatengedwa kupita ku Babiloni. Motero ndidzathyola goli laukapolo la mfumu ya ku Babiloni.”
5
Apo mneneri Yeremiya adayankha mneneri Hananiya pamaso pa ansembe ndi anthu onse amene anali m'Nyumba ya Chauta. Adati,
6
“Inde momwemo! Chauta achitedi choncho. Chauta achitedi zimene walosazi, pakubwezera ziŵiya za ku Nyumba yake ndi akapolo onse ku malo ano kuchokera ku Babiloni.
7
Komabe ungomva zimene nditi ndikuuze iweyo ndi anthu onse.
8
Aneneri amene adatsogola kale ankalosa za nkhondo, za njala ndi za mliri, zodzagwera maiko ambiri ndi maufumu otchuka.
9
Koma ngati mneneri alosa za mtendere, zimene walosazo zikachitikadi, pamenepo zidzadziŵika kuti Chauta adamtumadi.”
10
Pamenepo mneneri Hananiya adachotsa goli m'khosi mwa mneneri Yeremiya nalithyola.
11
Adauza anthu onse kuti, “Chauta akuti, ‘Umu ndimo m'mene ndidzathyolera goli laukapolo la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni. Ndidzalichotsa m'khosi mwa anthu a mitundu yonse zisanathe zaka ziŵiri.’ ” Zitatero mneneri Yeremiya adachokapo.
12
Patapita nthaŵi pang'ono Hananiya atathyola goli m'khosi mwa Yeremiya, Chauta adauza Yeremiya kuti,
13
“Pita ukamuuze Hananiya mau a Chauta akuti, ‘Iweyo wathyola goli lamtengo, m'malo mwake Ine ndidzaika goli lachitsulo.
14
Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, Ndaika goli lachitsulo m'khosi mwa anthu a mitundu yonseyi, kuti azitumikira Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni. Adzamutumikiradi, ndipo ndampatsanso ulamuliro ngakhale pa nyama zakuthengo.’ ”
15
Tsono Yeremiya adauza Hananiya kuti, “Mvera, iwe Hananiya, Chautatu sadakutume, ndipo iweyo wanyenga anthuŵa kuti azimvera ulosi wabodza.
16
Nchifukwa chake Chauta akunena kuti, ‘Chenjera, ndidzakuchotsa pa dziko lapansi. Ufa chaka chino chisanathe, chifukwa chakuti wakhala ukulalikira zopandukira Chauta.’ ”
17
Zidachitikadi kuti mneneri Hananiya adafa chaka chomwecho, mwezi wachisanu ndi chiŵiri.
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 29 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52