bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 26
Jeremiah 26
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 27 →
1
Pamene Yehoyakimu, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, adayamba kulamulira, Chauta adauza Yeremiya kuti,
2
“Kaime m'bwalo la Nyumba ya Chauta. Ndipo ukalankhule kwa anthu onse okhala m'mizinda ya ku Yuda, amene amakapembedza ku Nyumba imeneyo. Ukaŵauze zonse zimene ndakulamula kuti ukanene, osasiyapo kanthu.
3
Mwina mwake nkutheka kuti adzamvera, ndipo aliyense adzaleka machimo ake. Tsono ndidzaleka osaŵapatsa chilango chimene ndidaati ndiŵalange nacho, chifukwa cha ntchito zao zoipa.
4
Ukaŵauze kuti, Chauta akuti: Ngati simundimvera Ine, ngati simutsata malamulo amene ndidakupatsani,
5
ngati simumvera mau a aneneri, atumiki anga, amene ndakhala ndikuŵatuma kwa inu, ngakhale kuti inu simunkaŵamvera,
6
ndiye kuti Nyumba ino ndidzaiwononga monga m'mene ndidaonongera Silo. Ndipo mzinda uno ndidzausandutsa chinthu chonyozeka kwa mitundu yonse ya pa dziko lapansi!”
7
Tsono ansembe, aneneri, pamodzi ndi anthu ena ambiri, adamva Yeremiya akulankhula mau ameneŵa m'Nyumba ya Chauta.
8
Yeremiya atatsiriza kulankhula zimene Chauta adamlamula kuti auze anthu onse, ansembe, aneneri ndi anthu onsewo adamgwira, namuuza kuti, “Ukuyenera kuphedwa.
9
Chifukwa chiyani walosa m'dzina la Chauta kuti Nyumba ino idzaonongedwa ngati Silo, ndipo kuti mzinda uno udzasanduka wopanda anthu, ngati chipululu?” Motero anthu onse adasonkhana nazinga Yeremiya m'Nyumba ya Chauta.
10
Akuluakulu a ku Yuda atamva zimene zinkachitikazo, adanyamuka kuchokera ku nyumba ya mfumu kupita ku Nyumba ya Chauta, nakakhala pa bwalo lao ku chipata chatsopano cha Nyumba ya Chauta.
11
Pamenepo ansembe ndi aneneri adauza akuluakuluwo ndi anthu ena onse kuti, “Munthu ameneyu ndi woyenera kumupha, chifukwa choti amalosa zoipa za mzinda uno, monga inu nomwe mwadzimvera.”
12
Tsono Yeremiya adauza akuluakulu aja ndi anthu onse kuti, “Chauta adachita kundituma kuti ndilengeze mau onse mwamvaŵa oinena Nyumba ya Mulungu ino pamodzi ndi mzindawu.
13
Ngati tsopano mukonza makhalidwe anu ndi ntchito zanu zomwe, ndi kuyamba kumvera mau a Chauta Mulungu wanu, ndiye kuti Iye adzakhululuka osakulangani monga m'mene adaaganizira.
14
Ineyo ndili m'manja mwanu. Mundichite chilichonse chimene chikukomereni.
15
Koma tsono mudziŵe kuti mukangondipha, ndiye kuti inuyo pamodzi ndi mzinda uno ndi anthu onse okhalamo, mudzapalamula mlandu wokhetsa magazi a munthu wosalakwa. Ndithudi, nzoona kuti Chauta ndiye adandituma kwa inu, kuti mumve zonse ndikunenazi.”
16
Pamenepo akuluakuluwo ndi anthu ena adauza ansembe ndi aneneri kuti, “Munthuyu sayenera kufa, popeza kuti walankhula nafe m'dzina la Chauta, Mulungu wathu.”
17
Akuluakulu ena am'dzikomo adaimiriranso nauza anthu onse amene adasonkhanawo kuti,
18
“Nthaŵi imene Hezekiya anali mfumu ya ku Yuda, Mika wa ku Moreseti ankalosa, ndipo adauza anthu onse a ku Yuda kuti Chauta Wamphamvuzonse akuti, “ ‘Ziyoni adzalimidwa ngati munda. Yerusalemu adzasanduka bwinja, phiri la Nyumba ya Mulungu lidzasanduka nkhalango.’
19
Nanga kodi mfumu Hezekiya ndi anthu onse a ku Yuda adamupha amene uja? Kodi suja mfumu idaopa Chauta nipempha kuti aikomere mtima? Ndipo suja Chauta adaleka osaŵapatsa chilango chimene adaati aŵalange nacho? Koma ife tili pafupi kudziitanira tsoka lalikulu.”
20
Padaalinso munthu wina amene ankalosa m'dzina la Chauta, dzina lake Uriya mwana wa Semaya wa ku Kiriyati-Yearimu. Iyeyo adaalosanso zodzagwera mzinda uno ndi dziko lino monga momwe adachitira Yeremiya.
21
Mfumu Yehoyakimu ndi akuluakulu ake onse ndiponso ankhondo ake, atamva zimene adaanena, adaafuna kumupha. Uriya atamva choncho, adachita mantha, nathaŵira ku Ejipito.
22
Komabe mfumu Yehoyakimu adatuma Elinatani mwana wa Akibori, pamodzi ndi anthu ena, ku Ejipito.
23
Iwowo adakagwira Uriya ku Ejipito komweko, nkubwera naye kwa mfumu Yehoyakimu. Mfumuyo idalamula kuti Uriyayo aphedwe, ndipo mtembo wake adakauika ku manda a anthu wamba.
24
Koma Ahikamu mwana wa Safani ndiye adatchinjiriza Yeremiya, motero sadaperekedwe kwa anthu kuti amuphe.
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 27 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52