bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 22
Jeremiah 22
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 23 →
1
Chauta adandiwuza kuti, “Pita ku nyumba ya mfumu ya ku Yuda, ukaiwuze kuti,
2
‘Iwe mfumu ya ku Yuda, imva mau a Chauta. Imva iwe amene umakhala pa mpando waufumu wa Davide, iweyo pamodzi ndi atumiki ako ndiponso anthu ako amene amaloŵera pa zipata izi.
3
Chautatu akuti uziweruza molungama ndi mosakondera. Munthu amene adambera zake uzimpulumutsa kwa womsautsa. Usavutitse mlendo, mwana wamasiye kapena mkazi wamasiye. Usakhetse magazi a anthu osachimwa pa malo ano.
4
Ndithu, ukamadzamvera mau aŵa, ndiye kuti mafumu okhala pa mpando waufumu wa Davide adzapitirirabe kumalamulira. Azidzaloŵera pa zipata izi za ku nyumba ya mfumu, atakwera pa magaleta ndi pa akavalo, iwowo pamodzi ndi atumiki ao ndi anthu ao.
5
Koma ngati sudzamvera mau anga, ndikulumbira pali Ine ndemwe, kuti nyumba imeneyi idzasanduka bwinja!’ ” Akuterotu Chauta.
6
Naŵa mau a Chauta onena za nyumba ya mfumu ya ku Yuda: “Ngakhale iwe ndimakukonda ngati Giliyadi, kapena ngati nsonga ya phiri la Lebanoni, komabe ndidzakusandutsa chipululu, mzinda wopanda anthu.
7
Ndidzatuma anthu oti adzakuwononge, aliyense ali ndi zida zake. Adzadula mikungudza yako yokoma, nadzaiponya pa moto.
8
“Pamene anthu a mitundu ina adzadutse pa mzinda umenewu, azidzafunsana kuti, ‘Kodi chifukwa chiyani Chauta adaononga chotere mzinda waukuluwu?’
9
Yankho lake lidzakhala lakuti, ‘Nchifukwa chakuti anthu akewo adasiya chipangano chimene adapangana ndi Chauta, Mulungu wao. Adayamba kupembedza milungu ina ndi kumaitumikira.’ ”
10
Musailire mfumu, musaŵaimbire nyimbo malemuwo. Koma mulire amene wachotsedwa m'dziko lake chifukwa sadzabwereranso, sadzaliwonanso dziko lake.
11
Paja Salumu, mwana wa Yosiya, mfumu ya ku Yuda, adaloŵa m'malo mwa atate ake pa mpando waufumu umene adausiya. Tsono ponena za amene uja Chauta akuti, “Iyeyo sadzabwereranso.
12
Adzafera ku dziko laukapolo, ndipo sadzaliwonanso dziko lino.”
13
“Tsoka kwa munthu womanga nyumba yake mopanda chilungamo, womanga zipinda zake monyenga, pogwiritsa ntchito anthu, koma osaŵapatsa malipiro a ntchito yao.
14
Munthuyo amanena kuti, ‘Ndidzadzimangira nyumba yaikulu, ya zipinda zam'mwamba zikuluzikulu, ndidzaikamo mawindo, ndi kukhomamo matabwa a mkungudza, ndipo ndidzaipaka utoto wofiira.’
15
Kodi uganiza kuti ndiwe mfumu poti nyumba zako ndi zamkungudza? Ganiza za bambo wako: suja anali nazo zosoŵeka zonse? Suja ankaweruza molungama ndi mosakondera? Ndipo paja zonse zidamuyendera bwino.
16
Ankateteza anthu otsika ndi osauka, ndipo zonse zinkamuyendera bwino. Kodi zimenezi sizidaonetse kuti ankandidziŵa?” Akuterotu Chauta.
17
“Koma iwe maganizo ako ndi mtima wako sizili penanso, zili pa phindu lonyenga, pa zopha anthu osalakwa, ndi pa zankhanza ndi zozunza ena.”
18
Nchifukwa chake Chauta ponena za Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya ku Yuda, akuti, “Sipadzakhala womulira munthu ameneyo kuti, ‘Kalanga ine, mbale wanga!’ Kapena kuti, ‘Kalanga ine, mlongo wanga!’ Sipadzakhala womulira kuti, ‘Kalanga ine, mbuye wanga!’ Kapena kuti, ‘Kalanga ine, mfumu yanga.’
19
Adzamuika ngati bulu basi, kuchita kumguguza nkukamtaya kuseri kwa zipata za Yerusalemu.”
20
“Tsono inu anthu a ku Yerusalemu, kwerani ku mapiri ku Lebanoni, mukalire mofuula kumeneko, mau anu amveke mpaka ku Basani. Mulire mofuula muli ku Abarimu, chifukwa onse amene munkaŵadalira aonongeka.
21
Ndidaakuchenjezani pamene zinthu zinkakuyenderani bwino. Koma inu mudati, ‘Sitidzamvera.’ Ndi m'mene mwakhala mukuchitira kuyambira muli ana aang'ono, simudamvere mau anga.
22
Mphepo idzakuchotserani abusa anu onse, ndipo amene munkaŵadalira adzatengedwa ukapolo. Tsono mudzanyozedwa, mudzachita manyazi, chifukwa cha zolakwa zanu zochuluka.
23
Inu amene mumakhala ku nyumba ya ku Lebanoni ija, amene mudamanga nyumba zanu pakati pa mikungudza, mudzalira kwambiri pamene zoŵaŵa zidzakugwerani, zonga za mkazi pa nthaŵi yake yochira.”
24
Chauta akuti, “Pali Ine ndemwe, iwe Yehoyakini, mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda, ngakhale ukadakhala ngati mphete ya ku dzanja langa lamanja, ndikadakuvula nkukutaya.
25
Ndidzakupereka kwa anthu ofuna kukupha, amene umaŵaopa, ndiye kuti kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ndi anthu ake.
26
Ndidzakupititsa ku dziko lina pamodzi ndi mai wako amene adakubala. Simudabadwire kumeneko, komabe nonsenu mudzafera kumeneko.
27
Simudzabwereranso kudziko kumene mudzafuna kubwerera.”
28
Ine ndidati, “Kodi ndiye kuti Yehoyakiniyu wakhala ngati mbiya yonyozeka, yosweka, chinthu chimene anthu sakuchisamala? Nanga chifukwa chiyani iyeyu ndi ana ake akuŵachotsa ndi kuŵaponya ku dziko losadziŵika konse?”
29
Iwe dziko, iwe dziko, iwe dziko, imva mau a Chauta.
30
Chauta akuti, “Munthu ameneyu mumtenge ngati wopanda ana, munthu amene sadzakhoza pa moyo wake. Ndithu, palibe ndi mmodzi yemwe mwa zidzukulu zake amene adzakhale pa mpando waufumu wa Davide ndi kudzalamuliranso Yuda.”
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 23 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52