bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 8
Jeremiah 8
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 9 →
1
Chauta akunena kuti, “Pa nthaŵi imeneyo anthu adzatulutsa m'manda mafupa a akalonga, a ansembe, a aneneri ndiponso a anthu onse amene ankakhala ku Yerusalemu.
2
Adzaŵamwaza pa mtunda kuyang'ana mwezi, ndi nyenyezi zonse zakumwamba zimene ankazikonda, kumazitumikira, kuzitsata, kuzipempha nzeru ndi kumazipembedza. Mafupa amenewo sadzaŵasonkhanitsa kapena kuŵakwirira, koma adzasanduka ndoŵe pamwamba pa nthaka.
3
Anthu onse otsala mwa anthu a mtundu woipawu, kulikonse kumene ndaŵapirikitsira, adzakonda kufa kupambana kuti akhale ndi moyo,” akuterotu Chauta Wamphamvuzonse.
4
Chauta adandiwuza kuti ndifunse anthu ake mau aŵa: “Kodi anthu akagwa, ndiye kuti sangathe kudzukanso? Kodi munthu akasokera, ndiye kuti sangathe kubwereranso?
5
Chifukwa chiyani nanga anthu ameneŵa akupitirirabe kulakwa, osabwereranso? Akangamira ndithu machimo ao, akukana kubwerera.
6
Ndakhala ndikutchereza ndi kuŵamvetsera, koma sadalankhulepo zoona. Palibe wochimwa aliyense amene adandiwonetsa kuti walapa, namanena kuti, ‘Ndachitanji ine?’ Koma aliyense akungotsata njira zake, ngati kavalo wothamangira nkhondo.
7
Mbalame amati kapande ija imadziŵa nthaŵi yake mumlengalenga. Nkhunda, namzeze ndi ngalu zimadziŵa nthaŵi yake yonyamukira ulendo. Koma anthu anga sadziŵa malangizo a Chauta.
8
“Mungathe kunena bwanji kuti, ‘Ndife anzeru, timasunga malamulo a Chauta, pamene alembi akulemba zabodza?’
9
Anthu anzeru adzachita manyazi, adzatha nzeru, ndipo adzagwidwa. Akana mau a Chauta, nanga nzeru zao nzotani?
10
Nchifukwa chake akazi ao ndidzaŵapatsa kwa anthu ena, minda yao ndidzaipereka kwa amene aŵagonjetsa. Ndithudi, kuyambira ana ndi akulu omwe, onsewo ali ndi khwinthi la phindu lopeza monyenga. Aneneri ndi ansembe omwe, onsewo ndi onyenga.
11
Iwo amapoletsa mabala a anthu anga pamwamba pokha. Amangonena kuti, ‘Kuli mtendere, kuli mtendere,’ chonsecho kulibe konse mtendere.
12
Kodi akamachita zonyansa, amachita manyazi ngati? Iyai, sankachita manyazi mpang'ono pomwe. Sadziŵa nkugwetsa nkhope komwe. Nchifukwa chake adzagwera pakati pa anzao amene adagwa kale. Adzagweratu pa tsiku limene ndidzaŵalanga,” akutero Chauta.
13
“Ndidzaŵatheratu. Ndidzachotsa dzinthu dza m'minda mwao. Sipadzakhala mphesa pa mpesa, kapena nkhuyu pa mkuyu, ndi masamba ake omwe adzauma. Zinthu zimene ndidaŵapatsa, ndidzaŵachotsera zonse.”
14
Anthu amati, “Chifukwa chiyani tikungokhala? Tiyeni tonse pamodzi tithaŵire ku mizinda yamalinga, tikafere komweko. Chauta, Mulungu wathu, wagamula kuti tiyenera kufa, watimwetsa madzi aululu pakuti tamchimwira.
15
Tinkafuna mtendere, koma zinthu sizidatiyendere bwino. Tinkafuna kuchira, koma tidangopeza zoopsa zokhazokha.”
16
“Adani athu aloŵa kale mu mzinda wa Dani. Dziko lonse likunjenjemera ndi kulira kwa akavalo ao. Adani akubwera kudzaononga dzikoli pamodzi ndi zinthu zake zonse. Adzaononganso mzinda ndi onse okhalamo.
17
Onani, ndikukutumirani njoka, mphiri zimene munthu sangazilodze, ndipo zidzakulumani,” akuterotu Chauta.
18
Kudandaula kwanga nkosalekeza. Mtima wanga walefukiratu.
19
Imvani kulira kwa anthu anga kuchokera ku dziko lakutali. Akuti, “Kodi Chauta sali ku Ziyoni? Kodi mfumu yake siili kumeneko?” Chauta ayankha kuti, “Chifukwa chiyani akundiputa ndi mafano ao, ndiponso ndi milungu yao yachilendo?”
20
Anthu akuti, “Kholola lapita, chilimwe chapita, koma sitidapulumukebe.”
21
Ndikumva kuŵaŵa chifukwa cha mavuto a anthu anga, ndikungolira, nkhaŵa yandigwira.
22
Kodi ku Giliyadi kulibe mankhwala ochiritsa? Kodi kumeneko kulibe sing'anga? Chifukwa chiyani mabala a anthu anga sadapole?
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52