bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 25
Jeremiah 25
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 26 →
1
Naŵa mau amene adadza kwa Yeremiya, onena za anthu onse a ku Yuda. Mauŵa adafika chaka chachinai cha ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya ku Yuda, ndiye kuti chaka choyamba cha ufumu wa Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni.
2
Mneneri Yeremiya adauza anthu onse a ku Yuda ndi onse okhala ku Yerusalemu kuti,
3
“Pa zaka 23, kuyambira chaka cha 13 cha ufumu wa Yosiya mwana wa Amoni mfumu ya ku Yuda, mpaka lero lino, ndakhala ndikulandira mau a Chauta ndi kumavutika nkukuuzani, koma inu simudamvere.
4
Inu simudamvere kapena kutchera khutu, ngakhale kuti Chauta sadaleke kukutumirani aneneri, atumiki ake.
5
Aneneriwo ankati, ‘Aliyense mwa inu akaleka makhalidwe ake oipa ndi ntchito zake zoipa, ndiye kuti mudzakhala m'dziko limene Chauta adakupatsani inu ndi makolo anu mpaka muyaya.
6
Musamatsate milungu ina, kumaitumikira ndi kumaipembedza. Musamapute mkwiyo wanga ndi mafano opanga ndi manja anu. Tsono Ine sindidzakuwonongani.’
7
Komabe simudandimvere. Mudaputa mkwiyo wanga ndi mafano amene mudapanga ndi manja anu, motero mudadziwononga nokha,” akuterotu Chauta.
8
Motero Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Chifukwa choti simudamvere mau anga,
9
ndidzaitana mafuko onse akumpoto, pamodzi ndi mtumiki wanga Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni. Ndidzaŵatuma kuti adzathire nkhondo dzikoli ndi anthu ake, ndiponso anthu a mitundu ina yozungulira dzikoli. Ndidzaŵaononga kwathunthu ndi kuŵasandutsa chinthu chonyansa, chonyozeka ndiponso chochititsa manyazi mpaka muyaya.
10
Ndidzathetsa chimwemwe chonse ndi kusangalala konse pakati pao. Ndidzaletseratu mau achikondwerero a mkwati wamwamuna ndi mkwati wamkazi. Sikudzamvekanso phokoso la mphero, ndipo ndidzazima nyale zonse.
11
Dziko lonseli lidzakhala chipululu ndi bwinja. Pa zaka makumi asanu ndi aŵiri mitundu imeneyi idzatumikira mfumu ya ku Babiloni.
12
Zaka makumi asanu ndi aŵirizo zitatha, ndidzailanga mfumu ya ku Babiloniyo pamodzi ndi anthu ake chifukwa cha zoipa zao, ndipo dziko lao ndidzalisandutsa bwinja mpaka muyaya.
13
Ndidzachita zonse zimene ndidanena zokhudza dziko limenelo, zonse zimene zidalembedwa m'bukumu, ndiponso zonse zimene mneneri Yeremiya adalosa zotsutsa anthu ameneŵa.
14
Iwo adzakhala akapolo a anthu a mitundu yochuluka ndi a mafumu otchuka. Motero ndidzaŵabwezera potsata zochita zao ndi ntchito za manja ao.”
15
Chauta, Mulungu wa Israele, adandiwuza kuti, “Tenga chikho ichi chodzaza ndi mkwiyo wanga, ndipo ukamwetse anthu a mitundu yonse kumene nditi ndikutume.
16
Atamwa, adzayamba kudzandira ndipo adzachita misala chifukwa cha nkhondo imene ndikutumiza pakati pao.”
17
Tsono ndidalandira chikhocho kumanja kwa Chauta ndipo ndidapatsa anthu a mitundu yonse, kuti amwe monga momwe Chauta adaandilamulira.
18
Adandituma ku Yerusalemu, ku mizinda ya ku Yuda, kwa mafumu ake ndi kwa akalonga ake, kuti ndiŵasandutse ngati bwinja, ndi chinthu chonyozeka ndi chomachiseka monga m'mene aliri tsopanomu.
19
Adanditumanso kwa Farao, mfumu ya ku Ejipito, kwa nduna zake, kwa akalonga ake, kwa anthu ake onse,
20
ndi kwa anthu a mitundu ina yachilendo yokhala pakati pao. Adanditumanso kwa mafumu onse a ku dziko la Uzi, kwa mafumu onse a Afilisti, ndiye kuti ku Asikeloni, ku Gaza, ku Ekeroni ndi ku chigawo chotsala cha ku Asidodi.
21
Adanditumanso ku Edomu, ku Mowabu ndiponso kwa Aamoni.
22
Adandituma kwa mafumu onse a ku Tiro ndi Sidoni, ndiponso kwa mafumu a maiko a m'mbali mwa nyanja, ndiye kuti
23
ku Dedani, ku Tema, ku Buzi ndi kwa onse ometa cham'mbali.
24
Adanditumanso kwa mafumu onse a ku Arabiya ndi kwa ena aja okhala m'chipululu.
25
Adandituma kwa mafumu onse a ku Zimiri, kwa mafumu onse a ku Elamu, kwa mafumu onse a ku Mediya,
26
kwa mafumu onse akumpoto, akufupi ndi akutali omwe, ndi kwa maufumu onse a dziko lonse lapansi. Potsiriza, atamwa onsewo, idzamwe ndi mfumu ya ku Babiloni.
27
“Kenaka udzaŵauze kuti, Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, ‘Imwani, muledzere, musanze, mugwe osadzukanso, chifukwa cha nkhondo imene ndikutumiza pakati panu.’ ”
28
“Akakana kulandira chikho kumanja kwako kuti amwe, uŵauze kuti, Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, Muyenera kumwa!
29
Tsopanotu ndiyamba ndalanga mzinda umene umadziŵika ndi dzina langa. Kodi mukuganiza kuti inuyo simudzalangidwa? Iyai, simungathe kupulumuka. Ndithu, nditumiza nkhondo kwa anthu onse okhala pa dziko lapansi,” akutero Chauta Wamphamvuzonse.
30
“Tsono iwe, ulengeze mau oŵatsutsa, uŵauze kuti, ‘Chauta adzakhuluma kumwamba, mau ake adzamveka ngati bingu kuchokera ku malo ake opatulika. Zoonadi, adzakhuluma, kukalipira anthu ake, adzafuula kwambiri ngati anthu oponda mphesa, polimbana ndi anthu onse a pa dziko lapansi.
31
Phokoso lalikululo lidzamveka pa dziko lonse lapansi, chifukwa Chauta akuŵazenga mlandu anthu a mitundu yonse. Akuti aweruza anthu onse, ndipo oipa adzaphedwa ndi lupanga, akuterotu Chauta.’ ”
32
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Onani, tsoka likuti likachoka pa mtundu wina likukagwa pa mtundu winanso. Ndipo ku malekezero a dziko lapansi kukuyambika mphepo yamkuntho.”
33
Pa tsiku limenelo, onse ophedwa ndi Chauta adzangoti vuu pa dziko lonse lapansi. Palibe amene adzaŵalire, kapena kukaŵaika m'manda. Adzangosiyidwa ngati ndoŵe ponseponse.
34
Inu abusa lirani kwambiri, fuulani kwamphamvu. Inu atsogoleri a anthu anga, dzolani phulusa. Nthaŵi yanu yokaphedwa yafika, ndipo mudzachita kuphedwa ngati nkhosa zamphongo.
35
Abusawo adzasoŵa kothaŵira, eniake a nkhosa adzasoŵa njira yopulumukira.
36
Mverani, abusa akulira, eniake a nkhosa akulira kwambiri, pakuti Chauta akuwononga busa lao.
37
Makola ao a nkhosa, amene adaali pa mtendere, akusanduka mabwinja chifukwa cha ukali woopsa wa Chauta.
38
Chauta waŵasiya anthu ake ngati mkango wosiya phanga lake, ndipo dziko lao lasanduka chipululu, chifukwa cha mazunzo a nkhondo ndi mkwiyo woopsa wa Chauta.
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 26 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52