bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 12
Jeremiah 12
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 13 →
1
Inu Chauta nditati nditsutsane nanu, wokhoza ndinu ndithu. Komabe ndifuna kudandaulako kwa Inu za mlandu wanga. Chifukwa chiyani anthu oipa zinthu zimaŵayendera bwino? Chifukwa chiyani anthu osakhulupirika amakhala pabwino?
2
Inu mudaŵabzala, ndipo adamera mizu. Amakula, namabala zipatso. Amakonda kulankhula za Inu, koma mitima yao ili kutali ndi Inu.
3
Koma Inu Chauta ine mumandidziŵa. Mumandiyang'ana, ndipo mumayesa mtima wanga, nkuwona kuti ndimakukondani. Muŵakoke anthu oipa ngati nkhosa zokaphedwa. Muŵaike padera mpaka tsiku loti akaphedwe.
4
Kodi dziko lidzakhala likulirabe mpaka liti? Ndipo udzu wake udzakhalabe wouma mpaka liti? Palibe mbalame kapena nyama zimene zatsala chifukwa anthu okhalamo ndi oipa kwambiri. Amati, “Mulungu sadzaona zimene zidzatiwonekere masiku athu otsiriza.”
5
Chauta adayankha kuti, “Ngati kukutopetsa kuthamanga ndi anthu, nanga udzapikisana bwanji ndi akavalo? Ngati mtima wako ulefuka m'dziko lokoma, nanga udzatani m'nkhalango ya ku Yordani?
6
Ngakhale abale ako ndi anansi ako nawonso amakuchita chiwembu, onsewo amvana pa zokuimba mlandu, usaŵakhulupirire, ngakhale alankhule nawe mau okoma.
7
“Banja la Israele ndalisiya, ndaŵataya anthu amene ndidaŵasankha. Okondeka anga ndaŵapereka kwa adani ao.
8
Anthu anga osankhidwa asanduka ngati mikango yakuthengo, amandidzumira mwaukali. Nchifukwa chake ndimadana nawo.
9
Anthu anga osankhidwa ali ngati mbalame yamaŵangamaŵanga imene akabaŵi aizinga kuchokera konsekonse. Kasonkhanitseni nyama zakuthengo, mubwere nazo ku phwando.
10
Abusa ambiri adaononga munda wanga wamphesa, adapondereza munda wanga. Munda wokoma uja adausandutsa chipululu.
11
Ndithu adausandutsa chipululu, ukundilirira Ine uli wokhawokha. Dziko lonse lasanduka chipululu, ndipo palibe amene akusamalako.
12
Anthu oononga abalalikira ku zitunda zonse zam'chipululu. Ndipo Ine Chauta ndatuma ankhondo kuti akanthe dziko lonse, kuyambira ku malire ena mpaka ku malire enanso. Palibe aliyense amene angapeze mtendere.
13
Anthu adafesa tirigu, koma adakolola minga. Adadzitopetsa pogwira ntchito, koma osapindula nkanthu komwe. Zokolola zao nzochititsa manyazi, chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Chauta.”
14
Chauta akuti, “Anthu oipa onse oyandikana ndi Aisraele, akulanda Aisraelowo dziko, choloŵa chimene ndidapatsa anthu angawo. Nchifukwa chake ndidzaŵachotsa m'dziko limenelo, ndipo ndidzachotsa banja la Yuda pakati pao.
15
Komabe nditaŵachotsa, ndidzaŵamveranso chifundo, ndipo ndidzabwezanso mtundu uliwonse ku dziko la choloŵa chake.
16
Tsono iwo akadzaphunzira bwino njira za mayendedwe a anthu anga, ndi kumalumbira m'dzina langa kuti, ‘Pali Chauta Wamoyo,’ monga momwe iwo adaphunzitsira anthu anga kumalumbira m'dzina la Baala, ndiye kuti iwowo ndidzaŵakhazikitsa pakati pa anthu anga.
17
Komatu ngati mtundu wina uliwonse sudzamvera Ine, ndidzauwononga kotheratu.”
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52