bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jeremiah 5
Jeremiah 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 6 →
1
“Thamangani uku ndi uku m'miseu ya Yerusalemu, mudziwonere nokha. Funafunani ku mabwalo ake ngati mungapezeke munthu, munthu wake wochita zolungama, wofunitsitsa zoona, kuti choncho Yerusalemu ndidzamkhululukire.
2
Ngakhale anthu akulumbira m'dzina la Chauta wamoyo, komabe akungolumbira monama.
3
Kodi Inu Chauta, suja mumafuna anthu onena zoona? Inu mudaŵakantha anthuwo, koma iwo sadamve kuŵaŵa. Mudaŵatswanya, koma sadafune kutembenuka mtima. Adaumitsa mitima yao ngati mwala, adakana kwamtuwagalu kulapa.”
4
Apo ndidati, “Ndi amphaŵi chabe aŵa, alibe ndi nzeru zomwe. Iwo sadziŵa njira ya Chauta, sazindikira zimene Mulungu wao akufuna.
5
Tsono ndidzapita kwa akuluakulu, ndidzalankhula ndi amenewo. Pakuti ndiwo angadziŵe njira ya Chauta, ndi zimene Mulungu wao akufuna.” Koma ndidaona kuti iwowonso adathyola goli la Chauta, adadula nsinga zao.
6
Nchifukwa chake mkango wam'malunje udzaŵapha, mmbulu wochoka ku thengo udzaŵaononga. Kambuku adzaŵalalira pafupi ndi mizinda yao. Ndipo adzakadzula aliyense wotuluka, poti zolakwa zao nzambiri, abwereratu m'mbuyo kwambiri.
7
Chauta akuti, “Kodi ndingakukhululukireni bwanji pa zonsezi? Ana anu adandisiya Ine, ndipo adapembedza milungu imene siili milungu konse. Ine ndidaŵapatsa zonse zimene ankasoŵa, komabe adakonda kumachita chigololo, namapita ku nyumba za akazi adama.
8
Aliyense ankathamangira mkazi wa mnzake, monga amachitira akavalo onenepa akamamemesa.
9
Ndiye ndingapande kuŵalanga chifukwa cha zimenezi? Monga ndisaulipsire mtundu wochita zotere?
10
Tsono ndidzatuma adani kuti akaononge mizere ya mipesa yao, komabe osati kotheratu. Akasadze nthambi zake, poti anthu ameneŵa si ake a Chauta.
11
Anthu a ku Israele ndi a ku Yuda onse akhala osakhulupirika kwa Ine,” akuterotu Chauta.
12
Anthuwo ankanama ponena za Chauta, ankati, “Mulungu sangatichite kanthu. Choipa sichidzatigwera, sitidzaona nkhondo kapena njala.
13
Mau a aneneri azikangopita ngati mphepo, ndipo uthenga wao si wa kwa Mulungu. Zimene amanena zidzaŵagwera iwo omwewo.”
14
Nchifukwa chake tsono Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, akuti, “Poti iwowo atero, mau anga ndidzaŵasandutsa moto m'kamwa mwako, anthuwo ndidzaŵasandutsa nkhuni, ndipo motowo udzaŵapserezeratu.”
15
“Iwe Israele, ndikukudzetsera mtundu wa anthu odzakuthira nkhondo, mtundu wake ndi wochokera kutali. Mtundu umenewu ndi wosagonjerapo, mtundu wakalekale, mtundu umene chilankhulo chake iwe suchidziŵa, ndipo zimene akunena, iwe sungazimvetse.
16
Ankhondowo mipaliro yao imapha anthu ambirimbiri, onsewo ndi ngwazi zokhazokha pa nkhondo.
17
Adzakutherani zokolola zanu ndi chakudya chanu. Adzapha ana anu aamuna ndi aakazi, adzakupheraninso nkhosa zanu ndi ng'ombe zanu. Adzaononga mipesa yanu ndi mikuyu yanu. Adzagwetsa mwankhondo mizinda yanu yamalinga imene mumaidalira.
18
“Koma ngakhale pa masiku amenewo sindidzakuwonongani kotheratu.
19
Ndipo mukamafunsana kuti, ‘Chifukwa chiyani Chauta Mulungu wathu watichita zimenezi?’ Iwe Yeremiya uzidzayankha kuti, ‘Monga momwe mudasiyira Chauta, ndi kumatumikira milungu yachilendo m'dziko lanu, momwemonso ndimo m'mene inuyo muzidzatumikira anthu a m'dziko lachilendo.’ ”
20
Mulalike kwa ana a Yakobe, mulengeze kwa anthu a ku Yuda kuti,
21
“Imvani izi, inu anthu opusa, opanda ndi nzeru zomwe, inu amene maso muli nawo, koma simupenya, amene makutu muli nawo, koma simumva.
22
Ine Chauta ndikuti, Kodi simukuchita nane mantha? Kodi simukunjenjemera pamaso panga? Ndine amene ndidaika mchenga kuti ukhale malire a nyanja, malire amene nyanjayo singaŵabzole. Mafunde ake, ngakhale aŵinduke bwanji, sangathe kupitirirapo. Ngakhale akokome chotani, sangathe kubzola.
23
Koma anthu ameneŵa ndi okanika ndiponso a mtima waupandu. Adapatuka ndipo adapitiratu.
24
Sadanenepo m'mitima mwao kuti, ‘Tiyeni tizimvera Chauta Mulungu wathu, amene amatipatsa mvula pa nthaŵi yake, mvula yachizimalupsa ndi yam'masika. Ndipo salephera kutipatsa nthaŵi ya kholola.’ ”
25
Koma zolakwa zanu zaletsetsa zonsezi, ndipo machimo anu akumanitsani zokoma.
26
Paja mwa anthu anga muli ena achifwamba, amene amalalira anzao monga m'mene amachitira otchera mbalame. Amatcha misampha nakola anthu.
27
Nyumba zao nzodzaza ndi chuma chochipeza mwachinyengo, ngati chitatanga chodzaza ndi mbalame. Nchifukwa chake adasanduka otchuka ndi olemera.
28
Adanenepa nkukhala a matupi osalala. Ntchito zao zoipa nzopanda malire, saweruza mwachilungamo nkhani ya ana amasiye, kuti iyende bwino, ndipo sateteza amphaŵi.
29
Chauta akuti, “Ndiye ndingapande kuŵalanga chifukwa cha zimenezi? Monga ndisaulipsire mtundu wochita zotere?”
30
M'dziko muno mwachitika chinthu chododometsa ndi choopsa.
31
Aneneri akulosa zabodza, ndipo ansembe akuvomerezana nawo. Komabe anthu anga akukondanso zomwezo. Kodi mudzatani potsiriza?
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52