bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 1
Genesis 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 2 →
1
Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
2
Dziko lapansilo linali lopanda maonekedwe enieni ndiponso losakonzeka. Mdima unali utaphimba nyanja yaikulu ponseponse, ndipo Mzimu wa Mulungu unkayendayenda pamwamba pa madziwo.
3
Tsono Mulungu adati, “Kuyere,” ndipo kudayeradi.
4
Mulungu adaona kuti kuyerako kunali kwabwino. Pomwepo adalekanitsa kuyerako ndi mdima.
5
Kuyerako adakutcha Usana, mdima uja adautcha Usiku. Ndipo kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku loyamba.
6
Kenaka Mulungu adati, “Pakhale cholekanitsa madzi, kuti madziwo akhale pa malo aŵiri olekana,” ndipo zidachitikadi.
7
Motero Mulungu adalenga cholekanitsa madzi chija, naŵagaŵa madziwo, ena pansi pa cholekanitsacho ena pamwamba pake.
8
Cholekanitsacho adachitcha dzina loti Thambo. Ndipo kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku lachiŵiri.
9
Mulungu adatinso, “Madzi apansiŵa akhale pa malo amodzi, kuti paoneke mtunda,” ndipo zidachitikadi.
10
Mulungu adautcha mtundawo Dziko, madzi adaŵasonkhanitsa aja adaŵatcha Nyanja. Mulungu adaona kuti zinali zabwino.
11
Tsono adati, “Panthaka pamere zomera zobala njere, ndiponso mitengo yobala zipatso zanjere malinga ndi mtundu wake,” ndipo zidachitikadi.
12
Motero panthaka padamera zomera za mitundu yonse, zipatso zokhala ndi njere ndi mitengo yobeleka zipatso za njere, malingana ndi mitundu yao. Mulungu adaona kuti zinali zabwino.
13
Ndipo kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku lachitatu.
14
Pambuyo pake Mulungu adati, “Kuthambo kukhale miyuni kuti izilekanitsa usana ndi usiku, ndiponso kuti ikhale zizindikiro za nyengo, masiku ndi zaka.
15
Miyuni imeneyi ikhale ku thambo ndi kumaunikira dziko lapansi,” ndipo zidachitikadi.
16
Motero Mulungu adalenga miyuni iŵiri yaikulu: dzuŵa loŵala masana, ndi mwezi woŵala usiku. Adalenganso nyenyezi.
17
Mulungu adaika miyuniyo ku thambo, kuti iziwunikira dziko lapansi,
18
kuti iziŵala usana ndi usiku, kulekanitsa kuyera ndi mdima. Mulungu adaona kuti zinali zabwino.
19
Ndipo kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku lachinai.
20
Zitatero Mulungu adati, “M'nyanja mukhale zamoyo zambirimbiri, ndipo pakhale mbalame zouluka mu mlengalenga.”
21
Motero Mulungu adalenga nsomba zazikulu zam'nyanja, pamodzi ndi zolengedwa zina zonse zokhala m'madzi, ndiponso mbalame ndi zouluka zina zamitundumitundu. Mulungu adaona kuti zonse zimene adalengazo zinali zabwino.
22
Adazidalitsa ponena kuti, “Swanani ndipo mudzaze nyanja, mbalamenso ziswane pa dziko.”
23
Tsono kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku lachisanu.
24
Ndipo Mulungu adati, “Padziko pakhale mitundu yonse ya zamoyo potsata mitundu yake: zoŵeta, zokwaŵa, ndi nyama zakuthengo, potsata mitundu yake.” Ndipo zidachitikadi.
25
Pomwepo Mulungu adalenga nyama zakuthengo potsata mitundu yake, ndi nyama zoŵeta potsata mitundu yake, ndiponso zokwaŵa zonse potsata mitundu yake. Mulungu adaona kuti zonse zimene adalengazo zinali zabwino.
26
Zitatha izo Mulungu adati, “Tiyeni tipange munthu m'chifanizo chathu, adzakhale wonga Ifeyo. Adzalamulire nsomba zam'nyanja, mbalame zamumlengalenga, nyama zoŵeta, ndi zokwaŵa zonse za pa dziko lapansi.”
27
Motero Mulungu adalenga munthu, m'chifanizo chake, adaŵalengadi m'chifanizo cha Mulungu. Adaŵalenga wina wamwamuna wina wamkazi.
28
Adaŵadalitsa poŵauza kuti, “Mubereke ndi kuchulukana, mudzaze dziko lonse lapansi ndi kumalilamulira. Ndakupatsani ulamuliro pa nsomba, mbalame ndi nyama zonse zimene zikukhala pa dziko lapansi.”
29
Ndipo Mulungu adati, “Ndikukupatsani zomera zonse za mtundu wokhala njere, ndi mitundu yonse ya zomera zobala zipatso zanjere, kuti muzidya.
30
Koma nyama zonse zakuthengo, mbalame, ndi zokwaŵa zonse, ndazipatsa msipu kuti zizidya,” ndipo zidachitikadi momwemo.
31
Mulungu adaona kuti zonse zimene adalengazo zinali zabwino kwambiri. Tsono kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50