bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 16
Genesis 16
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 17 →
1
Sarai mkazi wa Abramu, sadam'balire ana Abramuyo. Koma Sarai anali ndi mdzakazi wake wa ku Ejipito dzina lake Hagara.
2
Tsono Sarai adauza Abramu kuti, “Chauta sadandipatse ana. Bwanji osati muloŵane ndi mdzakazi wangayu kuti kapena nkundibalira mwana?” Abramu adavomereza zimenezo.
3
Motero Sarai adapereka Hagara uja kwa Abramu, kuti akhale mkazi wake wamng'ono. (Zimenezi zidachitika Abramu atakhala ku Kanani zaka khumi).
4
Abramu ataloŵana ndi Hagara, Hagarayo adatenga pathupi ndipo pompo Hagara adayamba kudzitama, namanyoza Sarai.
5
Tsiku lina Sarai adauza Abramu kuti, “Cholakwa chimenechi chakuti Hagara akundinyoza, chili pa inu. Ine ndidakupatsani mdzakazi ameneyu, ndipo kuyambira paja adatenga pathupipa, wakhala akundinyoza. Chauta ndiye aweruze kuti tiwone wolakwa ndani pakati pathu.”
6
Abramu adayankha kuti, “Iyeyu ndi mdzakazi wako, ndipo ali mu ulamuliro wako. Chita naye chilichonse chomwe ufuna.” Choncho Sarai adayamba kuzunza Hagara, mpaka Hagarayo adathaŵa.
7
Mngelo wa Chauta adakumana naye pa chitsime m'chipululu, pa mseu wopita ku Suri.
8
Ndipo adati, “Iwe Hagara, mdzakazi wa Sarai, kodi ukuchokera kuti, nanga ukupita kuti?” Iye adayankha kuti “Ndikuthaŵa mbuyanga Sarai.”
9
Mngelo wa Chautayo adati, “Iyai, bwerera kwa Sarai, ukamgonjere.
10
Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka, zosaŵerengeka.”
11
Popitiriza mau mngeloyo adati, “Tsopano uli pafupi kukhala ndi mwana wamwamuna, udzamutche Ismaele, ndiye kuti Chauta wamva kulira kwako pa zovuta zako.
12
Koma mwana wako adzakhala ndi mtima wa chilombo, adzadana ndi aliyense, ndipo anthu onse adzadana naye. Adzakhala akudana ndi abale ake onse.”
13
Tsono Hagara adatcha Chauta amene adalankhula naye kuti, “Inu ndinu Mulungu wondipenya,” poti adati, “Pano ndamuwona Iye amene amandipenya.”
14
Nchifukwa chake anthu amachitchula chitsime cha pakati pa Kadesi ndi Beredi kuti Chitsime cha Wamoyo-Wondipenya.
15
Tsono Hagara adamubalira Abramu mwana wamwamuna, namutcha dzina loti Ismaele.
16
Abramu anali wa zake 86 pa nthaŵi imeneyo.
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 17 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50