bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 17
Genesis 17
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 18 →
1
Abramu ali wa zaka 99, Chauta adamuwonekera namuuza kuti, “Ine ndine Mulungu Mphambe. Tsono uzindimvera nthaŵi zonse, ndipo uzichita zolungama.
2
Ndidzachita nawe chipangano, ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zambiri.”
3
Pomwepo Abramu adagwada pansi ndipo Mulungu adati,
4
“Nachi chipangano chimene ndidzachite nawe. Ndikulonjeza kuti udzakhala kholo la anthu a mitundu yambiri.
5
Dzina lako silidzakhalanso Abramu, koma Abrahamu. Limeneli ndilo dzina lako, chifukwa ndikukusandutsa kholo la anthu a mitundu yambiri.
6
Ndidzakupatsa zidzukulu zambiri, ndipo zina mwa izo zidzakhala mafumu. Udzakhala ndi zidzukulu zambiri kotero kuti zidzakhala mitundu yaikulu.
7
Chipangano changachi ndidzachikhazikitsa pakati pa Ine ndi iwe ndi zidzukulu zako zam'tsogolo, ndipo chidzakhala chipangano chosatha. Ine ndidzakhala Mulungu wako ndi Mulungu wa zidzukulu zako.
8
Dziko lino limene ukukhalamo ngati mlendoli, ndidzakupatsa iwe ndi zidzukulu zako. Dziko lonse la Kanani lidzakhala la zidzukulu zako mpaka muyaya, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao.”
9
Mulungu adauzanso Abrahamu kuti, “Iwenso tsono uyenera kuvomera kusunga chipangano changa, pamodzi ndi zidzukulu zako zam'tsogolo.
10
Iwe pamodzi ndi zidzukulu zako, muyenera kusunga chipangano ichi chakuti mwamuna aliyense pakati panupa aziwumbalidwa.
11
Kuyambira tsopano muziwumbalidwa. Chimenechi chidzakhala chizindikiro cha chipangano pakati pa Ine ndi inu.
12
Muziwumbala mwana wamwamuna aliyense akakwanitsa masiku asanu ndi atatu. Muziwumbala mwamuna aliyense pa mibadwo yanu yonse, mbadwa kapena kapolo amene mudamgula kwa mlendo wosakhala wa mbumba yanu.
13
Inde aliyense aumbalidwe, ndipo chimenechi chidzakhala chizindikiro pa matupi anu, choonetsa kuti chipangano changa ndi inu nchamuyaya.
14
Munthu wamwamuna wosaumbalidwa adzachotsedwa pakati pa anthu a mtundu wake, chifukwa sadasunge chipangano changa.”
15
Pambuyo pake Mulungu adauza Abrahamu kuti, “Mkazi wakoyu usamutchulenso kuti Sarai. Tsopano dzina lake ndi Sara.
16
Iyeyu ndidzamdalitsa ndipo adzakubalira mwana wamwamuna. Ndidzamdalitsa, ndipo adzakhala mai wa mitundu ya anthu. Pakati pa zidzukulu zakezo padzatuluka mafumu.”
17
Apo Abrahamu adagwada pansi. Adayamba kuseka, nati, “Kodi mwamuna woti ali ndi zaka 100, angathe kuberekanso? Kodi Sara, amene ali ndi zaka 90, angathe kubalanso?”
18
Ndipo adauza Mulungu kuti, “Ndikukupemphani kuti mungodalitsa Ismaele yemweyu.”
19
Koma Mulungu adati, “Iyai, ndi mkazi wako Sara amene adzakubalira mwana wamwamuna ndipo udzamutcha Isaki. Ndidzasunga chipangano changa ndi iyeyo ndiponso ndi zidzukulu zake, ndipo chipanganocho chidzakhala chamuyaya.
20
Koma kunena za Ismaeleyu, ndidzamdalitsa, ndipo ndidzampatsa ana ambiri pamodzi ndi zidzukulu. Adzakhala bambo wa mafumu khumi ndi aŵiri, ndipo zidzukulu zake ndidzakhala mtundu waukulu.
21
Koma ndidzasunga chipangano changa ndi mwana wako Isaki amene adzabadwa mwa Sara pa nyengo yonga yomwe ino chaka chamaŵachi.”
22
Mulungu atatha kulankhula ndi Abrahamu, adamsiya pomwepo.
23
Tsiku lomwelo Abrahamu adakumbukira zimene Mulungu adamuuza, ndipo adatenga mwana wake Ismaele ndi akapolo onse obadwira m'nyumba mwake, kapena amene Abrahamu adaŵagula, kungoti amuna onse a m'nyumba mwake, naŵaumbala monga momwe Mulungu adaamuuzira.
24
Abrahamu anali wa zaka 99 pa nthaŵi imene adaumbalidwa.
25
Mwana wake Ismaele anali wa zaka 13 pamene adaumbalidwa.
26
Pa tsiku limeneli Abrahamu ndi mwana wake Ismaele adaumbalidwa,
27
pamodzi ndi anthu aamuna onse, amuna obadwira m'banja mwake ndiponso ena amene adaŵagula ndi ndalama kwa alendo, onsewo adaumbalidwa pamodzi ndi iyeyo.
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50