bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 44
Genesis 44
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 43
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 45 →
1
Pambuyo pake Yosefe adalamula wantchito wamkulu woyang'anira nyumba yake kuti, “Dzaza matumba a anthuŵa ndi chakudya chambiri momwe angathe kusenzera. Ndipo ndalama za aliyense uziike pakamwa pa thumba.
2
Tsono pakamwa pa thumba la wamng'onoyo uikepo chikho changa chasiliva chija, pamodzi ndi ndalama zake zimene amati agulire tirigu.” Wantchitoyo adachita monga momwe adaamuuzira.
3
M'maŵa kutacha, anthu aja adaloledwa kupita pamodzi ndi abulu ao.
4
Atangoyenda pang'ono kuchoka mumzindamo, Yosefe adauza wantchito wake wamkulu uja kuti, “Nyamuka, uthamangire anthu aja. Ukaŵapeza, uŵafunse kuti, ‘Bwanji mwabwezera zoipa kwa zabwino?
5
Mwaberanji chikho chimene mbuyanga amamwera? Amati akafuna kudziŵa zam'tsogolo, amagwiritsa ntchito chikho chimenechi. Ndithu zimene mwachitazi nzoipa kwambiri.’ ”
6
Wantchito uja ataŵapeza, adanena mau omwe adaamuuza aja.
7
Iwo aja adamuyankha kuti, “Kodi mukulankhulazi nzotani bwana? Ife sitikadatha mpang'ono pomwe kuganiza kuti tichite zimene mukunenazi.
8
Inu nomwe mudaona kuti ife pochoka ku Kanani, tidabwera ndi ndalama zimene tidaazipeza m'matumba mwathu. Nanga tingaberenji siliva kapena golide m'nyumba mwa bwana wanu?
9
Tsono bwana, wina mwa ife akapezeka ndi chikho chimenechi, ndithu aphedwe, ndipo tonsefe tidzakhala akapolo anu, bwana!”
10
Apo wantchitoyo adati, “Chabwino. Komatu wina pakati panupa akapezeka ndi chikhocho, ameneyo akhala kapolo wanga, ena nonsenu muzipita mwaufulu.”
11
Motero onsewo adatsitsa msanga matumba ao, aliyense nkumasula thumba lake.
12
Wantchito wa Yosefe uja adafunafuna mosamala kwambiri kuyambira pa wamkulu mpaka pa wamng'ono, ndipo chikhocho adachipeza m'thumba la Benjamini.
13
Apo onsewo adang'amba zovala zao ndi chisoni. Adasenzetsanso abulu katundu wao uja, nabwerera kumzinda konkuja.
14
Yuda ndi abale ake atafika kunyumba kwa Yosefe, adampeza akadali momwemo ndipo onsewo adaŵerama pamaso pake.
15
Yosefe adati, “Mwachita chiyani? Kodi simukudziŵa kuti munthu monga ine ndingathe kudziŵa zakutsogolo?”
16
Apo Yuda adati, “Kodi ife tinganene chiyani kwa inu, bwana? Tilinso ndi mau ngati? Tingathe kudziyeretsa bwanji? Mulungu waulula cholakwa chathu, bwana. Tonsefe bwana, ndife akapolo anu, osati mmodzi yekha amene wapezeka ndi chikhoyu ai.”
17
Koma Yosefe adati, “Iyai! Ine sindingathe kuchita zotero. Yekhayo amene wapezeka ndi chikho, ndiye adzakhala kapolo wanga. Enanu mungathe kumabwerera kwanu kwa bambo wanu.”
18
Pamenepo Yuda adasendera kwa Yosefe, nati “Pepani bwana, loleni ine mtumiki wanu kuti ndilankhule nanu. Musati mukwiye nane bwana, inu muli ngati Farao yemwe.
19
Bwana, paja mudaatifunsa kuti, ‘Kodi muli naye bambo wanu kapena mbale wanu?’
20
Ndipo ife tidaakuyankhani kuti, ‘Tili naye bambo wathu wokalamba ndi mbale wathu wina wamng'ono amene adabadwa bambo wathuyo atakalamba kale. Mkulu wake wa mnyamata ameneyo adamwalira kale. Choncho m'mimba mwa mai wake, yekhayu ndiye amene ali moyo, ndipo bambo wake amamkonda kwabasi.’
21
Bwana, paja inu mudaatiwuza kuti, ‘Mudzabwere naye, kuti ndidzamuwone.’
22
Ife tidaakuyankhani kuti, ‘Mnyamatayo sangachoke kwa bambo wake, popeza kuti akatero, bambo wakeyo kufa kudzakhala komweko.’
23
Tsono paja mudaanena kuti simudzatilola kufikanso pamaso panu tikadzapanda kubwera naye mng'ono wathuyo.
24
Titabwerera kwathu kwa bambo wathu mtumiki wanu, tidamuuza mau anu onse aja.
25
Iye atatiwuza kuti, ‘Bwererani mukatigulireko chakudya pang'ono,’
26
ife tidamuuza bambo wathu kuti, ‘Sitingathe kupita popeza kuti munthu uja sakatilola kufika pamaso pake, tikapanda kupita ndi mng'ono wathuyu.’
27
Koma bambo wathu adati, ‘Mukudziŵa kuti mkazi wanga adandibalira ana aŵiri.
28
Wina mwa iwowo adandisiya kale. Ndiye kuti adajiwa ndi zilombo chifukwa sindidamuwonenso.
29
Tsopano mukanditengeranso uyu, nakaphedwa, ndiye kuti ine ndidzafa ndi chisoni.’ ”
30
Yuda adapitiriza kulankhula nati, “Nchifukwa chake tsopano ndikabwerera kwathu kwa bambo wanga, mtumiki wanu, opanda mnyamata ameneyu, amene moyo wa bambo wanga uli pa iye,
31
akakangoona kuti iyeyu palibe, basitu akafa. Ndiye kuti ifeyo ndi amene tidzachititse bambo wathu chisoni chofa nacho mu ukalamba wake.
32
Ndiponsotu bwana, ine ndidapereka moyo wanga kwa bambo wanga chifukwa cha mnyamata ameneyu. Ndidamuuza kuti ngati mnyamatayu sindidzabwerera naye, ndidzakhala wolakwa pamaso pa bambo wanga moyo wanga onse.
33
Ndiye tsopano bwana, ineyo nditsalira kuno kuti ndikhale kapolo wanu m'malo mwa mnyamatayu. Muloleni iyeyu apite ndi abale akeŵa.
34
Ine ndingathe bwanji kupita kwa bambo wanga popanda mnyamatayu kupita nane? Ine ndekha sindingathe kupirira kuti ndiwone tsoka lotere likugwera bambo wanga.”
← Chapter 43
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 45 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50