bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 27
Genesis 27
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 28 →
1
Isaki atakalamba, adachita khungu, mwakuti sankatha kupenya. Tsono adatumiza mau kuti Esau mwana wake wamkulu abwere. Atabwera, Isaki adamuitana kuti, “Mwana wanga!” Iye adavomera kuti, “Ŵaŵa.”
2
Tsono Isakiyo adati, “Ona, ine nkukalamba kuno, ndipo sindidziŵa tsiku loti ndidzafe.
3
Tenga zida zako, uta ndi mivi yomwe, upite ku thengo ukandiphere nyama.
4
Undiphikire chakudya chokoma chija ndimakondachi, ubwere nacho kuno. Nditadya, ndidzakudalitsa ndisanafe.”
5
Rebeka ankangomvetsera pamene Isaki ankalankhula ndi mwana wake Esau. Tsono Esauyo atapita ku thengo kukasaka nyama yoti akapatse bambo wake,
6
Rebeka adauza Yakobe kuti, “Ine ndamva bambo wako akuuza Esau kuti,
7
‘Ubwere ndi nyama kuno, undiphikire. Nditadya, ndidzakudalitsa pamaso pa Chauta ndisanafe.’
8
Ndiye iwe mwana wanga, undimvere ndipo uchite zonse zimene ndikuuze.
9
Pita ku khola, ukanditengere timbuzi tiŵiri tonenepa bwino, kuti ndiphike, ndi kukonza chakudya chimene bambo wako amachikonda.
10
Ukapereke chakudyacho kwa bambo wako kuti akadye, ndipo akudalitse asanafe.”
11
Koma Yakobe adauza mai wake kuti, “Mukudziŵa kuti Esau ndi wacheya, koma ine khungu langa ndi losalala.
12
Mwina mwake bambo wanga adzandikhudza, ndipo adzadziŵa kuti ndikumunyenga. Motero m'malo mondidalitsa, adzanditemberera.”
13
Mai wake adayankha kuti, “Mwana wanga, temberero lakelo lidzagwere ine, osati iwe. Iweyo ungochita zimene ndakuuza, kanditengere timbuzito.”
14
Choncho Yakobe adapita kukatenga timbuzito nakapatsa mai wake, ndipo Rebeka adaphika chakudya chimene bamboyo ankachikonda.
15
Pambuyo pake Rebeka adatenga zovala zabwino za Esau zimene ankazisunga m'nyumba, naveka mng'ono wake Yakobe.
16
Adamuvekanso zikopa za tianatambuzi pamikono pake ndiponso pakhosi pake posalala popanda cheya.
17
Ndipo adatenga buledi ndi chakudya chokonza bwino chija, napatsira Yakobe.
18
Yakobe adapita kwa bambo wake, namuitana kuti, “Bambo!” Isaki adafunsa kuti, “Kodi ndiwe mwana wanga uti?”
19
Yakobe adayankha kuti, “Ndine Esau mwana wanu wamkulu, ndipo zija mudaandiwuzazi ndachita. Chonde dzukani, khalani tsonga, mudye nyama ndakutengeraniyi, ndipo mundidalitse.”
20
Apo Isaki adafunsa kuti, “Kodi nyama imeneyi waipeza bwanji msanga chotere, mwana wanga?” Yakobe adayankha kuti, “Chauta, Mulungu wanu, adandithandiza kuti ndiipeze.”
21
Isaki adauza Yakobe kuti, “Tasendera pafupi kuti ndikukhudze, kuti ndidziŵe ngati ndiwedi mwana wanga Esau, kapena ai.”
22
Yakobe adasendera pafupi ndi bambo wake, ndipo bambo wakeyo adamukhudza nati, “Liwuli ndi la Yakobe, koma mikonoyi ndi ya Esau.”
23
Sadamzindikire Yakobe popeza kuti mikono yake inali yacheya ngati ya Esau. Motero adayambapo kumdalitsa.
24
Koma adafunsanso kuti, “Kodi ndiwedi mwana wanga Esau?” Yakobe adayankhanso kuti, “Ndine amene.”
25
Apo Isaki adati, “Bwera nayo kuno nyama yako, kuti ndidye ndipo ndikudalitse.” Yakobe adabwera ndi nyamayo, Isaki nkudya. Yakobe adampatsanso vinyo woti amwe.
26
Tsono bambo wakeyo adati, “Bwera pafupi, udzandimpsompsone, mwana wanga.”
27
Atabwera pafupi kudzampsompsona Isaki adanunkhiza zovala zimene Yakobe adaavala, ndipo pompo adamdalitsa, adati, “Fungo lokoma la mwana wanga lili ngati fungo la zokolola za m'munda umene Chauta adaudalitsa.
28
Mulungu akugwetsere mvula, ndipo minda yako ikhale yobala bwino. Akupatse zakudya ndi zakumwa zambiri.
29
Anthu azikutumikira, mitundu ya anthu izikugwadira. Ukhale wolamulira pakati pa abale ako, zidzukulu za mai wako zizikugwadira. Atembereredwe onse okutemberera, ndipo adalitsidwe onse okudalitsa.”
30
Isaki atamaliza kudalitsako, Yakobe adachokapo. Nthaŵi yomweyo wafika Esau kuchokera kuuzimba kuja.
31
Iyenso adaphika chakudya chabwino kwambiri, nakapereka kwa bambo wake. Esauyo adati, “Chonde bambo dzukani, khalani tsonga, mudye nyama imene ine mwana wanu ndakutengerani, ndipo mundidalitse.”
32
Isaki adamufunsa kuti, “Kodi iwenso ndiwe yani?” Iye adayankha kuti, “Ndine mwana wanu wamkulu Esau.”
33
Pompo Isaki adayamba kunjenjemera thupi lonse, nafunsa kuti, “Nanga uja adapha nyama nkubwera nayo kwa ineyu ndani? Ndadya kale imeneyo, iwe usanabwere. Ndamudalitsa kale, ndipo madalitso amenewo ndi ake mpaka muyaya.”
34
Esau atamva zimenezi, adalira kwambiri ndi mtima woŵaŵa, ndipo adati, “Bambo, pepani inenso mundidalitseko.”
35
Koma Isaki adayankha kuti, “Mng'ono wako anabwera, ndipo wandinyenga. Iyeyo ndiye amene watenga madalitso ako onse.”
36
Pamenepo Esau adati, “Kameneka nkachiŵiri kundichenjeretsa iye uja. Nchosadodometsa kuti dzina lake ndi Yakobe. Ukulu wanga wauchisamba adandilanda, ndipo tsopano wandilandanso madalitso anga. Kodi monga madalitsowo simudandisungireko ndi pang'ono pomwe?”
37
Isaki adayankha Esauyo kuti, “Ndamudalitsa kale iyeyo kuti akhale mbuyako, ndipo abale ake onse ndaŵasandutsa atumiki ake. Ndampatsa chakudya ndi chomwera chake. Nanga tsopano chatsalanso nchiyani choti ndikuchitire iwe mwana wanga?”
38
Esau adapitirirabe kumpempha bambo wakeyo kuti, “Kodi bambo, dalitso muli nalo limodzi lokhali? Tandidalitsaniko nanenso bambo.” Ndipo atatero adayambanso kulira.
39
Tsono Isaki, bambo wakeyo, adamuuza kuti, “Pa malo ako okhalapo sipadzakhala konse chonde, mvula siidzagwa pa minda yako.
40
Ntchito yako idzakhala yomenya nkhondo, ndipo udzakhala wotumikira mbale wako. Koma ukadzatha kudzimasula, udzachokeratu m'goli la ulamuliro wake.”
41
Motero Esau adadana naye Yakobe chifukwa choti m'malo modalitsa iyeyo, bambo wake adadalitsa Yakobe. Ndipo adati, “Nthaŵi yakuti ndilire maliro a bambo wanga ili pafupi, pamenepo ndidzamupha Yakobeyu.”
42
Koma Rebeka atamva za maganizo onse a Esau, adaitana Yakobe namuuza kuti, “Taona, mbale wako Esau akuganiza zoti akuphe kuti akulipsire.
43
Tsopano mwana wanga, uchite zimene ndikuuze. Konzeka, thaŵira kwa mlongo wanga Labani ku Harani.
44
Bakakhala kwa iyeyo kanthaŵi ndithu,
45
mpaka mtima wa mbale wako utatsika ndi kuiŵala zonse zimene wamchitazi. Pa nthaŵiyo, ine ndidzatuma munthu kudzakutenga. Nanga nditayirenji inu ana anga aŵiri pa tsiku limodzi?”
46
Rebeka adauza Isaki kuti, “Akazi Achihitiŵa, ine ndatopa nawo! Yakobenso akakwatira wina mwa a Ahiti akunoŵa, ine kodi moyo wanga nkukomanso?”
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 28 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50