bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 39
Genesis 39
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 38
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 40 →
1
Aismaele aja adapita naye Yosefe ku Ejipito kumene Potifara Mwejipito, nduna ya Farao ndiponso mkulu wa asilikali olonda kunyumba ya mfumu, adamgula.
2
Chauta anali naye Yosefe, ndipo adamthandiza kuti zonse zimuyendere bwino. Adakhala m'nyumba ya bwana wake, Mwejipito uja.
3
Bwana wakeyo adaona kuti Chauta anali naye Yosefe, ndi kuti ankamukhozetsa pa zonse zimene ankachita.
4
Potifara adakondwa naye Yosefe poona m'mene ankamutumikira. Choncho adamsandutsa kapitao wa nyumba yake, ndiponso woyang'anira zonse zam'nyumbamo.
5
Kuyambira nthaŵi imene Yosefe adayamba kusamalira zonse za m'nyumba ya Potifarayo, Chauta adadalitsa zonse za kunyumba kwa Mwejipitoyo, ngakhale za kuminda kwake, chifukwa cha Yosefeyo.
6
Choncho Potifara adaika m'manja mwa Yosefe zake zonse, kotero kuti sankalabadiranso kanthu kalikonse, koma chakudya chokha chimene ankadya. Yosefe anali wa maonekedwe abwino ndi wokongola.
7
Patapita kanthaŵi, mkazi wa bwana wake adayamba kusirira Yosefe. Tsono mkaziyo adauza Yosefeyo kuti, “Bwanji ugone nane.”
8
Yosefe adakana, adati, “Chifukwa choti ine ndikugwira ntchito muno, bwana wanga salabadiranso kanthu kalikonse ka m'nyumba muno. Adandipatsa ukapitao woyang'anira zake zonse,
9
ndipo ulamuliro wa zonse za m'nyumba muno uli m'manja mwanga, osati m'manja mwake. Sadandimane kanthu kalikonse kupatula inu nokha, pakuti ndinu mkazi wake. Tsono kungatheke bwanji kuti ine ndichite chinthu choipitsitsa choterechi, ndi kuchimwira Mulungu?”
10
Ngakhale mkazi uja ankalankhula mau ameneŵa kwa Yosefe tsiku ndi tsiku, Yosefeyo sankamvako mpang'ono pomwe, ndipo sankalola kuchita naye zoipa.
11
Koma tsiku lina Yosefe adaloŵa m'nyumba kuti agwire ntchito, ndipo panalibe antchito ena m'nyumbamo.
12
Mkazi uja adamgwira mwinjiro Yosefeyo, namuuza kuti, “Ugone nane basi!” Koma iye adathaŵira pabwalo, kusiya mwinjiro uja uli m'manja mwa mkaziyo.
13
Tsono mkazi uja ataona kuti Yosefe wasiya mwinjiro ndipo wathaŵira pabwalo,
14
adaitana antchito am'nyumbamo, naŵauza kuti, “Mwaziwona izi? Mwamuna wanga adabwera ndi Muhebri uyu m'nyumba muno kudzatipunza ife. Iye anakaloŵa kuchipinda kwanga nandinyenga kuti ndigone naye. Koma ine ndinakuŵa kwambiri.
15
Tsono atamva kukuwa kwangako, wasiya mwinjiro wake m'manja mwangamu nkuthaŵira pabwalo.”
16
Mwinjirowo adangousunga m'manja kudikira mpaka bwana wa Yosefe atabwera.
17
Tsono atabwera, adamsimbira nkhani yonseyo, adati, “Kapolo uja Wachihebri mudabwera naye m'nyumba munoyu, analoŵa kuchipinda kwanga kukandipunza ine.
18
Koma ine nditakuwa, iyeyo anasiya mwinjiro wake pafupi ndi ine, nkuthaŵira pabwalo.”
19
Mbuyake wa Yosefe adapsa mtima koopsa atamva mau a mkazi wake onena kuti, “Inde, izi ndi zimene wandichita kapolo wanu.”
20
Pompo adammangitsa Yosefe nakamtsekera m'ndende m'mene ankasungamo akaidi a mfumu, ndipo adakhala m'menemo.
21
Koma Chauta anali naye Yosefe, namkomera mtima kwambiri, kotero kuti wosunga ndende adakondwera naye Yosefe.
22
Adamsandutsa kapitao woyang'anira akaidi anzake onse, pamodzi ndi zonse zochitika m'ndendemo.
23
Zonse zinali m'manja mwa Yosefe, ndipo wosunga ndendeyo sankayang'aniranso kanthu kena kalikonse, chifukwa Chauta anali naye Yosefe ndipo ankamukhozetsa pa zonse zimene ankachita.
← Chapter 38
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 40 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50