bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 3
Genesis 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 4 →
1
Njoka inali yochenjera kupambana zamoyo zonse zimene Chauta adazilenga. Njokayo idafunsa mkazi uja kuti, “Kodi nzoona kuti Mulungu adakuletsani kuti musadye zipatso za mtengo uliwonse m'munda muno?”
2
Mkazi uja adayankha kuti, “Tingathe kudya zipatso za mtengo uliwonse m'munda muno,
3
kupatula wokhawo umene uli pakati pake. Mulungu adanena kuti tisadye zipatso za mtengo umenewo, ngakhale kuzikhudza, chifukwa choti tikadzangotero, tidzafa.”
4
Koma njokayo idayankha mkaziyo kuti, “Iyai, kufa simudzafa konse.
5
Mulungu amadziŵa kuti inu mukadzadya zipatso zimenezi, maso anu adzatsekuka, ndipo mudzakhala monga momwe aliri Mulunguyo. Mudzadziŵa zabwino ndi zoipa.”
6
Tsono mkaziyo adaona kuti mtengowo ndi wokongola, ndiponso kuti zipatso zake zingakhale zokoma kudya. Pompo adayamba kukhumbira kuti adyeko zipatsozo, adzakhale wanzeru. Motero adathyolako zipatso zina za mtengowo, naadya. Tsono zina adapatsako mwamuna wake, ndipo iyenso adadya.
7
Atangodya choncho, adazindikira kuti ali maliseche. Choncho adasoka masamba a mkuyu navala.
8
Madzulo dzuŵa litapepa, aŵiriwo adamva mtswatswa, Chauta akuyenda m'mundamo, ndipo iwo adabisala m'katikati mwa mitengo, kuti Iye angaŵaone.
9
Koma Chauta adamuitana Adamu uja kuti, “Kodi uli kuti?”
10
Adamu adayankha kuti, “Ndinakumvani m'mundamu ndipo ndinaopa, ndiye ndinabisala ntaona kuti ndili maliseche.”
11
Mulungu adamufunsa kuti, “Kodi adakuuza ndani kuti uli maliseche? Kapena wadyatu zipatso za mtengo uja ndidakuuza kuti usadyewu eti?”
12
Pamenepo Adamu adayankha kuti, “Mkazi mudandipatsayu ndiye amene anandipatsa zipatsozo kuti ndidye, ndipo ndadyadi.”
13
Apo Chauta adafunsa mkazi kuti, “Kodi iwe, zimene wachitazi wachitiranji?” Mkazi uja adayankha kuti, “Njoka ndiyo imene inandinyenga kuti ndidye.”
14
Pamenepo Chauta adauza njokayo kuti, “Chifukwa chakuti wachita zimenezi, ndiwe wotembereredwa pakati pa nyama zonse za pansi pano, zoŵeta ndi zakuthengo zomwe. Kuyambira tsopano mpaka muyaya udzakwaŵa ndi kumimba kwako, ndipo chakudya chako chidzakhala fumbi.
15
Ndidzaika chidani pakati pa iwe ndi mkazi, padzakhala chidani pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake. Idzaphwanya mutu wako, ndipo iwe udzaluma chidendene chake.”
16
Pambuyo pake Mulungu adauza mkaziyo kuti, “Ndidzaonjeza zovuta zako pamene udzakhala ndi pathupi, udzamva zoŵaŵa pa nthaŵi yako ya kubala mwana. Udzakhumba mwamuna wako, ndipo mwamuna wakoyo adzakulamulira iwe.”
17
Kenaka Mulungu adauza Adamu kuti, “Iwe unamvera mkazi wako, wadya zipatso zija zimene ndidaakuuza kuti usadye. Nthaka idzatembereredwa chifukwa cha zimene wachitazi. Udzayenera kugwira ntchito yathukuta nthaŵi ya moyo wako wonse, kuti upeze chakudya chokwanira.
18
M'nthakamo mudzamera zitsamba za minga ndi za nthula, ndipo iwe udzadya zomera zakuthengo.
19
Udzayenera kukhetsa thukuta kuti upeze chakudya, mpaka udzabwerera kunthaka komwe udachokera. Udachokera ku dothi, udzabwereranso kudothi komweko.”
20
Adamu adatcha mkazi wake Heva, chifukwa choti iyeyu anali mai wa anthu onse.
21
Ndipo Chauta adasokera Adamu ndi mkazi wake zovala zachikopa naŵaveka onse aŵiriwo.
22
Chauta adati, “Tsopano munthuyu wakhala monga tiliri ife, popeza kuti akudziŵa zabwino ndi zoipa. Asaloledwe kudya zipatso za mtengo wopatsa moyowo ndi kukhala moyo mpaka muyaya.”
23
Motero Chauta adamtulutsamo m'munda mwa Edeni muja, kuti azilima m'nthaka momwe adachokera.
24
Atampirikitsira kunja Adamuyo, Mulungu adaika akerubi kuvuma kwa munda wa Edeni. Adaikanso lupanga lamoto limene linkazungulira mbali zonse, kutchinjiriza mtengo wopatsa moyo uja, kuti wina asaufike pafupi.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50