bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 30
Genesis 30
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 29
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 31 →
1
Rakele ataona kuti sakumubalira ana Yakobe, adayamba kuchita nsanje ndi mkulu wake uja, ndipo adauza Yakobe kuti, “Mundipatse ana, apo ai, ndingofa basi.”
2
Yakobe adapsera mtima Rakele, namuuza kuti, “Sindingathe kuloŵa m'malo mwa Mulungu. Iyeyo ndiye akukuletsa kubala ana.”
3
Apo Rakele adati, “Nayu mdzakazi wanga Biliha, khala nayeni kuti andibalire mwana. Motere podzera mwa iye, inenso ndidzakhala ndi ana.”
4
Choncho Rakele adapereka Biliha kwa mwamuna wake, ndipo adakhala naye.
5
Biliha adatenga pathupi namubalira Yakobe mwana wamwamuna.
6
Tsono Rakele adati, “Mulungu waweruza mondikomera mtima. Wamva pemphero langa, ndipo wandipatsa mwana wamwamuna.” Motero mwanayo adamutcha Dani.
7
Biliha mdzakazi wa Rakele adatenganso pathupi namubaliranso Yakobe mwana wamwamuna.
8
Pamenepo Rakele adati, “Ndalimbana naye kwambiri mkulu wanga, ndipo ndapambana.” Motero mwanayo adamutcha Nafutali.
9
Leya ataona kuti waleka kubala, adapereka mdzakazi wake Zilipa kwa Yakobe.
10
Ndipo Zilipa adabala mwana wamwamuna.
11
Tsono Leya adati, “Ndachita mwai.” Motero mwanayo adamutcha Gadi.
12
Zilipa mdzakazi wa Leyayo adamubaliranso Yakobe mwana wamwamuna wachiŵiri.
13
Apo Leya adati, “Ndakondwa! Ndipo akazi adzanditchula wamwai.” Motero mwanayo adamutcha Asere.
14
Pa nthaŵi yodula tirigu, Rubeni adapita ku minda, nakapezako zipatso za mankhwala a chisulo, ndipo adadzapatsa Leya mai wake. Rakele adauza Leya kuti, “Chonde patseko mankhwala amene mwana wako wakufuniraŵa.”
15
Leya adayankha kuti, “Kodi sunakhutitsidwebe ndi mwamuna wanga udandilandayu? Tsopano ufuna kutenganso mankhwala a chisulo amene mwana wanga wandifunira?” Rakele adati, “Ukandipatsa mankhwala a chisulo ochokera kwa mwana wakoŵa, ŵamunaŵa akhala ndi iwe usiku uno.”
16
Pamenepo Yakobe ankabwera madzulo kuchokera ku munda, Leya adatuluka kukamlonjera, nati “Lero mugone kunyumba kwanga kuno, chifukwa cha mankhwala a chisulo ondifunira mwana wanga.” Motero Yakobe adakhala ndi Leya usiku umenewo.
17
Mulungu adamva pemphero la Leya, choncho adatenga pathupi, namubalira Yakobe mwana wamwamuna wachisanu.
18
Tsono adati, “Mulungu wandipatsa mphotho chifukwa ndidapereka mdzakazi wanga kwa mwamuna wanga.” Motero mwanayo adamutcha Isakara.
19
Leya adatenganso pena pathupi, namubalira Yakobe mwana wamwamuna wachisanu ndi chimodzi.
20
Ndipo adati, “Mulungu wandipatsa mphotho yokoma. Tsopano mwamuna wanga adzakhala nane chifukwa ndamubalira ana aamuna asanu ndi mmodzi.” Motero mwanayo adamutcha Zebuloni.
21
Pambuyo pake adabala mwana wamkazi, namutcha Dina.
22
Tsono Mulungu adakumbukira Rakele, namva pemphero lake, nkulola kuti abale ana.
23
Iyenso adatenga pathupi, nabala mwana wamwamuna. Ndipo adati, “Mulungu wandichotsa manyazi a uchumba wanga.”
24
Motero mwanayo adamutcha Yosefe, nanena kuti, “Mulungu andipatse wina mwana.”
25
Atabadwa Yosefe, Yakobe adauza Labani kuti, “Mundilole ndizibwerera kwathu.
26
Patseni akazi anga ndakugwirirani ntchitoŵa, pamodzi ndi ana anga, ndipo ndichoke. Mukudziŵa kuti ndakugwirirani bwino ntchito.”
27
Labani adamuuza kuti, “Undilole kuti ndinenepo mau aŵa, ‘Ine ndi nzeru zamtundu ndadziŵadi kuti Chauta wandidalitsa chifukwa cha iwe.
28
Tandiwuza malipiro ako, ndikupatsa.’ ”
29
Yakobe adayankha kuti, “Mukudziŵa m'mene ndakugwirirani ntchito, ndi m'mene zoŵeta zanu zaswanirana kwambiri pozisamala ine.
30
Kale munali ndi zoŵeta pang'ono koma tsopano zachuluka, ndipo Chauta wakudalitsani chifukwa cha ine. Tsopano ndiyenera kusamala banja langa.”
31
Apo Labani adamufunsa kuti, “Kodi ndikulipire chiyani?” Yakobe adayankha kuti, “Sindifuna malipiro ena aliwonse. Komabe ndidzapitirira kukuŵeterani zoŵeta zanu, mukavomera kuchita zimene ndinene.
32
Lero ndipita pakati pa zoŵeta zanu zonse. Ndipatula nkhosa zonse zakuda, ndiponso mbuzi zonse zamaŵangamaŵanga ndi zamathothomathotho. Malipiro amene ndifuna ine ndi ameneŵa.
33
Patsogolo pake mudzazindikira ngati ndachita zimenezi mokhulupirika pamene mubwere kudzaona malipiro anga. Mukadzaona kuti ndili ndi mbuzi yopanda mathotho kapena maŵanga kapena mwanawankhosa amene sali wakuda, mudzadziŵe kuti imeneyo ndi yakuba.”
34
Labani adavomera, adati, “Chabwino. Tichite monga waneneramo.”
35
Koma tsiku limenelo, Labani adachotsa atonde onse amathothomathotho ndi amaŵangamaŵanga, kudzanso mbuzi zazikazi zamathothomathotho ndi zamaŵangamaŵanga, zonse za maŵanga oyera. Adachotsanso nkhosa zonse zakuda, nauza ana ake kuti aziyang'anire zoŵeta zonsezo.
36
Atatero adasiyana naye Yakobe uja nayenda mtunda wa masiku atatu. M'menemo nkuti Yakobeyo akuŵeta zoŵeta zina za Labani.
37
Tsono Yakobe adatenga nthambi zaziŵisi za mitengo ya mitundu itatu yakudzikolo, nazikungunula makungwa, kotero kuti nthambizo zinkaoneka za mipyololo yoyera.
38
Nthambizo adaziika patsogolo pa zoŵeta kumene zinkamwera madzi, kuti zoŵetazo ziziyang'ana nthambizo pomwa madzi, chifukwa zoŵetazo zinkakwerewa podzamwa madzi.
39
Motero zoŵetazo zikatenga maŵere zitayang'ana nthambizo, ana ake ankakhala ndi maonekedwe amathothomathotho ndiponso amaŵangamaŵanga.
40
Yakobe adaika anaankhosa padera, naika nkhosa zina kuti ziyang'anane ndi zoŵeta za Labani zamathothomathotho ndi zakuda. Mwa njira imeneyi adapeza zoŵeta zakezake, ndipo sadazisokoneze ndi zoŵeta za Labani.
41
Zoŵeta zamphamvu zikamakwerewa, Yakobe ankazikhazikira nthambi zija kumaso kwake pa malo omwera, kuti pakutero zitenge maŵere pafupi ndi nthambizo.
42
Choncho zoŵeta zikakhala zofooka zinali za Labani, koma zamphamvu zinali za Yakobe.
43
Mwa njira imeneyi Yakobe adalemera kwambiri. Adakhala ndi zoŵeta zambiri, akapolo aamuna ndi aakazi, ngamira ndi abulu.
← Chapter 29
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 31 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50