bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 22
Genesis 22
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 23 →
1
Pambuyo pake Mulungu adamuyesa Abrahamu. Adamuitana, adati, “Abrahamu!” Ndipo Abrahamu adayankha kuti, “Ee Ambuye.”
2
Mulungu adati, “Tenga Isaki, mwana wako mmodzi yekha uja amene umamkonda kwambiri, upite ku dziko la Moriya. Kumeneko ukampereke ngati nsembe yopsereza pa phiri limene ndidzakuuza.”
3
M'maŵa mwake Abrahamu adakonza chishalo pa bulu wake nadulanso nkhuni zokaotchera nsembe, ndipo adatenga Isaki pamodzi ndi antchito ake aŵiri, nanyamuka ulendo wopita ku malo amene Mulungu adaamuuza.
4
Pa tsiku lachitatu lake Abrahamu adaona malowo chapatali.
5
Ndipo adauza antchito ake aja kuti, “Inu bakhalani pano ndi buluyu. Ine ndi mnyamatayu tipita uko kukapemphera, pambuyo pake tidzakupezani.”
6
Abrahamu adasenzetsa Isaki nkhuni zokaotchera nsembe yopsereza ija, iyeyo adaatenga moto m'manja mwake, pamodzi ndi mpeni, onse nkumayendera limodzi.
7
Tsono Isaki adaitana bambo wake kuti, “Atate.” Abrahamu adavomera kuti, “Ee, mwana wanga.” Isaki adafunsa kuti, “Moto ndi nkhuni ndikuziwona, zilipo, koma nanga mwanawankhosa wokaotchera nsembe ali kuti?”
8
Abrahamu adamuyankha kuti, “Mwana wanga, Mulungu akatipatsa mwanawankhosayo.” Choncho onse aŵiri adapitiriza ulendo wao limodzi.
9
Atafika ku malo amene adaamuuza Mulungu aja, Abrahamu adamanga guwa, naika nkhuni pamwamba pa guwalo. Kenaka adamanga mwana wake uja, namgoneka pamwamba pa nkhunizo.
10
Tsono adasolola mpeni kuti amuphe mwana wakeyo.
11
Koma mngelo wa Chauta adamuitana kuchokera kumwamba, adati, “Abrahamu, Abrahamu!” Iye adayankha kuti, “Ee, Ambuye!” Mngeloyo adati,
12
“Usamuphe mnyamatayo, kapena kumchita kanthu kena kalikonse. Ndikudziŵa kuti ndiwe womveradi Mulungu, chifukwa sudandimane mwana wako mmodzi yekhayo.”
13
Abrahamu atayang'ana, adaona kuti pali nkhosa yamphongo yogwidwa nyanga zake m'ziyangoyango. Adapita kukaigwira, naipha ngati nsembe yopsereza m'malo mwa mwana wake uja.
14
Abrahamu adaŵatcha malowo kuti Chauta adapatsa. Ndipo mpaka lero lino anthu amati, “Paphiri la Chauta adzapatsa.”
15
Mngelo wa Chauta uja adamuitana Abrahamu kachiŵiri kuchokera kumwamba, adati,
16
“Chauta akunena kuti, ‘Ndikulumbira kuti ndidzakudalitsa kwambiri iwe chifukwa wachita zimenezi, osandimana mwana wako mmodzi yekha uja.
17
Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka ngati nyenyezi zakumwamba, kapenanso ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja. Zidzukulu zakozo zidzagonjetsa adani ao onse.
18
Ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzalandira madalitso kudzera mwa zidzukulu zako, chifukwa iwe wandimvera.’ ”
19
Abrahamu adabwerera kumene adaasiya antchito ake kuja, ndipo onsewo adapita ku Beereseba. Tsono Abrahamu adakhazikika komweko.
20
Pambuyo pake Abrahamu adamva kuti Milika adabalira Nahori mbale wake ana asanu ndi atatu.
21
Mwana wake wachisamba anali Uzi, mng'ono wa Uziyo anali Buzi. Panalinso Kemuwele, bambo wake wa Aramu,
22
Kesedi, Hazo, Pilidasi, Idilafe ndi Betuele.
23
Betuele adabereka Rebeka. Milika adabalira Nahori mbale wa Abrahamu ana asanu ndi atatu ameneŵa.
24
Ndipo Reuma, mzikazi wa Nahori, adabala Teba, Gahamu, Tahasi ndi Maaka.
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 23 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50