bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 19
Genesis 19
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 20 →
1
Angelo aŵiri aja adaloŵa m'Sodomumo madzulo ndi kachisisira, Loti atakhala pafupi ndi chipata cha mzindawo. Tsono Lotiyo atangoŵaona anthuwo, adaimirira nakaŵalonjera. Adaŵeramitsa mutu, nati,
2
“Chonde ambuye anga, tiyeni mukafike kunyumba, mukatsuke mapazi ndi kugona komweko. M'maŵa kukacha, mungathe kupitirira ndi ulendo wanu.” Koma iwo adayankha kuti, “Iyai, ife tigona panja mumzinda mommuno.”
3
Loti adaumirirabe kuŵapempha, ndipo pambuyo pake iwo adavomera, napita kunyumba kwa Loti. Tsono Loti adaŵachitira phwando. Adaŵaphikira buledi wosafufumitsa naŵakonzera chakudya chokoma kwambiri, anthuwo nkudya.
4
Alendowo asanakagone, anthu onse amumzindamo, achinyamata ndi okalamba omwe, adadzazinga nyumbayo.
5
Adaitana Loti namufunsa kuti, “Kodi anthu abwera kwanu usiku uno aja ali kuti? Atulutse, abwere kuno kuti tigone nawo.”
6
Loti adatuluka panja natseka chitseko.
7
Tsono adaŵapempha kuti, “Inu abwenzi anga, musachite zimenezi chifukwa nkulakwa kwambiri kuchita zotere.
8
Onani, ine ndili ndi ana aakazi aŵiri, anamwali osadziŵa mwamuna. Bwanji ndikupatseni ana ameneŵa kuti muchite nawo zomwe mukufuna. Koma alendoŵa, musaŵachite kanthu kena kalikonse chifukwa ndi alendo anga, ndipo ndiyenera kuŵatchinjiriza.”
9
Koma iwowo adati, “Choka apa, wakudza iwe! Ndiwe yani iwe kuti ungatiwuze zoti tichite? Tachoka apa! Mwina mwake tingathe kukuzunza kwambiri kupambana iwowo.” Motero adamkankha Lotiyo, nasendera kuti akathyole chitseko.
10
Koma anthu aŵiri anali m'kati aja adamkokera Lotiyo m'nyumba, natseka chitseko.
11
Kenaka adaŵachititsa khungu anthu onse amene adaaima pabwalowo, achinyamata ndi okalamba omwe, kotero kuti sadathenso kuwona khomo.
12
Anthu aŵiriwo adafunsa Loti kuti, “Kodi aliponso wina aliyense amene uli naye kuno? Tenga ana ako aamuna, ana ako aakazi, akamwini ako ndi wina aliyense wachibale amene ali mumzinda muno, mutuluke,
13
chifukwa ife tikuti tiwononge malo ano. Chauta waziona zoipa zonse zimene anthu okhala mumzinda muno akuchita, ndipo tatumidwa kuti tiuwononge mzindawu.”
14
Pamenepo Loti adapita kwa anyamata amene ankafuna kukwatira ana akewo naŵauza kuti, “Fulumirani, tiyeni tituluke kuno, chifukwa patsala pang'ono kuti Chauta aononge malo ano.” Koma iwowo ankangoyesa nthabwala chabe.
15
M'mamaŵa, angelo aja adayesa kumufulumizitsa Loti namuuza kuti, “Fulumira! Iweyo ndi mkazi wako ndi ana ako aakazi aŵiri, mutuluke kupita kunja kwa mzinda, kuti mupulumutse moyo wanu pamene mzinda uno ukukaonongedwa.”
16
Koma Loti ankakayikabe, tsono Chauta adamumvera chifundo. Motero anthuwo adatenga Loti, mkazi wake ndi ana ake aŵiri aja moŵagwira pa dzanja, naŵatulutsa mumzindamo, nkuŵasiya panja pomwepo.
17
Ataŵatulutsira kunja kwa mzindawo, mmodzi mwa angelowo adati, “Thamangani, mupulumutse moyo wanu. Musacheukire m'mbuyo, ndipo musaime m'chigwamo. Thaŵirani ku mapiri kuti mungaphedwe.”
18
Koma Loti adamuyankha kuti, “Iyai mbuyanga musatero.
19
Mwandikomera mtima kwambiri pakupulumutsa moyo wanga. Komatu mapiriwo ali patali kwambiri. Kuwonongeka kwa malo ano mwanenaku kuchitika ine ndisanafike kumapiriko, ndipo ndifa.
20
Apo patsidyapo pali kamzinda kakang'ono. Pamenepo mpafupi, ndingathe kukafika. Bwanji ndipite kumeneko. Nkochepa kwambiri, koma ndikhoza kupulumukirako.”
21
Munthuyo adayankha kuti, “Zimenezo ndavomereza. Kamzinda kameneko sindikaononga.
22
Fulumira! Thamanga! Sindichita kena kalikonse mpaka iwe utafika kumeneko.” Choncho Loti adathamanga nakafika ku kamzinda kaja. Nchifukwa chake kamzindako adakatcha Zowari.
23
Pamene dzuŵa linkatuluka, Loti nkuti atafika kale ku Zowari.
24
Tsono Chauta adagwetsa moto wa sulufule pa Sodomu ndi Gomora kuchokera kumwamba.
25
Motero adaonongeratu mizinda imeneyi, pamodzi ndi chigwa chonse ndi anthu onse am'mizindamo, kuphatikizapo zomera zonse za m'dziko limenelo.
26
Koma mkazi wa Loti adaacheukira m'mbuyo, ndiye pomwepo adasanduka mwala wamchere.
27
M'maŵa mwake, m'mamaŵa, Abrahamu adathamangira ku malo omwe aja, kumene adaaimirira pamaso pa Chauta.
28
Adayang'ana ku mizinda ya Sodomu ndi Gomora ndi ku chigwa chija. Ndipo adangoona utsi uli tolotolo kutuluka m'chigwamo ngati utsi wotuluka m'ng'anjo ya moto.
29
Motero pamene Chauta ankaononga mizinda yam'chigwayo, adakumbukira pemphero la Abrahamu, ndipo adapulumutsa Loti ku chiwonongeko chimene chidasakaza mizinda ija m'mene Loti ankakhala.
30
Popeza kuti Loti ankaopa kukhala ku Zowari, iyeyo pamodzi ndi ana ake aakazi aŵiri aja, adapita ku dziko lamapiri, onsewo nkumakakhala m'mapanga.
31
Mwana wamkulu adauza mng'ono wake kuti, “Bambo athuŵa akukalamba tsopano, ndipo palibe munthu ndi mmodzi yemwe pa dziko lapansi woti angatikwatire, kuti tibale ana monga momwe zimachitikira zinthu pa dziko lapansi.
32
Tiye tiŵaledzeretse abamboŵa kuti agone nafe, kuti mtundu usathe.
33
Choncho usiku womwewo anawo adampatsa vinyo bambo waoyo. Zitatero, mwana wamkuluyo adagona ndi bambo wake. Pamenepo nkuti bamboyo ataledzera kwambiri, kotero kuti sankadziŵa zimene zinkachitika.”
34
M'maŵa mwake mwana wamkuluyo adauza mng'ono wake uja kuti, “Ine dzulo ndidagona ndi atate. Tiye tsono tiŵaledzeretsenso kuti iwenso ugone nawo, kuti choncho mtundu wathu usathe.”
35
Motero usiku umenewo adamledzeretsanso, ndipo mwana wamng'onoyo adagona ndi bambo wake. Nthaŵi imeneyinso nkuti bamboyo ataledzera, kotero kuti sadadziŵe zochitikazo.
36
Mwa njira imeneyi, ana onse aŵiriwo a Loti adatenga pathupi pa bambo wao.
37
Mwana wamkuluyo adabala mwana wamwamuna, namutcha Mowabu. Iyeyo ndiye kholo la Amowabu onse.
38
Mwana wamng'onoyo nayenso adabala mwana wamwamuna, namutcha Benami. Iyeyo ndiye kholo la Aamoni.
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 20 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50