bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 34
Genesis 34
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 35 →
1
Tsiku lina Dina mwana wa Yakobe wobadwa kwa Leya, adapita kukacheza ndi akazi ena am'dzikomo.
2
Sekemu, mwana wa Hamori Muhivi, amene anali mfumu ya chigawo cha dzikolo, atamuwona namwaliyo, adamgwira nagona naye.
3
Sekemu ankamukondadi Dina, mwana wa Yakobe, ndipo ankamulankhula mau achikondi.
4
Choncho adakauza bambo wake kuti, “Nditengereni namwaliyu kuti akhale mkazi wanga.”
5
Yakobe adaamva kuti Dina mwana wake adamgwiririra, koma popeza kuti ana ake aamuna anali ku busa kuŵeta ng'ombe, sadachitepo kanthu mpaka iwowo atabwera.
6
Hamori, bambo wa Sekemu, adapita kukacheza ndi Yakobe.
7
Pa nthaŵi imeneyo ana ake a Yakobewo anali atangobwerako kubusa kuja. Anawo atamva zimenezo, adapsa mtima kwambiri. Adakwiya koopsa poona kuti Sekemu wachita chinthu choipa kwambiri ndi kuchita chipongwe Aisraele, pogwira Dina, mwana wa Yakobe, nkuchita naye zoipa.
8
Tsono Hamori adaŵauza kuti, “Mwana wanga Sekemu wamkonda mwana wanu. Chonde muloleni kuti amukwatire.
9
Tiyeni tikhale ogwirizana chifukwa cha ukwati umenewu. Ife tidzakwatira ana anu, inunso mudzakwatira ana athu.
10
Mukhale nafe pamodzi m'dziko mwathu mommuno. Mukhazikike kulikonse kumene mungakonde, muzichita malonda mwaufulu, ndipo muzigula malo omangira nyumba monga mufunira.”
11
Pambuyo pake Sekemu adauza atate ake a Dina ndi alongo ake aja kuti, “Mundikomere mtima, ndipo ndidzakupatsani zonse zimene mungafune.
12
Tandiwuzani mphatso imene mufuna, ndipo mutchule mtengo uliwonse wolowolera. Ine ndidzakupatsani zonse zimene mungatchule, malinga mukandilola kumkwatira mkaziyu.”
13
Koma ana a Yakobe adayankha Sekemu ndi bambo wake Hamori moŵanyenga, popeza kuti Sekemu adaamchititsa manyazi Dina mlongo wao.
14
Iwowo adati, “Sikungatheke kuti tilole mlongo wathu kukwatiwa ndi munthu wosaumbalidwa. Chimenechi ndi chinthu chamanyazi kwa ife.
15
Tingathe kuvomera pokhapokha inu mutakhala monga momwe tiliri ifemu, ndiye kuti mutaumbala ana anu onse aamuna.
16
Pamenepo tidzakulolani kuti mukwatire ana athu, ndipo ifenso tidzakwatira ana anu. Tsono tidzakhazikika pakati panu ndi kusanduka fuko limodzi.
17
Koma ngati simuvomereza zimene tikunenazi, zoti muumbalidwe, ife tidzangomtenga mwana wathu wamkaziyu.”
18
Mau ameneŵa adakondweretsa kwambiri Hamori ndi mwana wake Sekemu.
19
Ndipo mnyamatayo adafulumira kuchita zimene zinkafunikazo, chifukwa choti adaamkonda kwambiri mwana wa Yakobeyo. Sekemu anali wotchuka kwambiri m'banja lakwaolo.
20
Tsono Hamori pamodzi ndi mwana wake Sekemu adakachita msonkhano ku chipata cha mzinda wao, nalankhula ndi anthu a m'mudzi mwao kuti,
21
“Anthu aŵa ndi abwenzi athu. Motero tiŵalole kuti akhale m'dziko mwathu muno, kuti azichita malonda mwaufulu. Dzikoli ndi lalikulu ndipo lingathenso kuŵakwanira iwowo. Tiyeni tizikwatirana nawo.
22
Komatu anthu ameneŵa adzavomera kukhala pakati pathu ndi kusakanizana nafe, kuti tikhale mtundu umodzi, pokhapokha ifeyo tikaumbala amuna onse monga amachitira iwowo.
23
Nanga sindiye kuti zoŵeta zao, katundu wao ndi ng'ombe zao zidzakhala zathu? Motero tiyeni tivomere kuti azikhala pakati pathu.”
24
Anthu amumzindamo adavomereza zimene Hamori ndi Sekemu adanena, ndipo amuna onse amumzindamo adaumbalidwa.
25
Patangopita masiku atatu, zilonda za kuumbala kuja zisanapole pa anthu aja, ana aŵiri a Yakobe, Simeoni ndi Levi, alongo ake a Dina, adatenga mikondo yao, nakaloŵa mosadziŵika mumzinda muja, nkukapha amuna onse.
26
Adapha Hamori ndi mwana wake Sekemu. Adamtenga Dina kumchotsa m'nyumba mwa Sekemu, nachokapo.
27
Ana ena a Yakobe adafika pa ophedwa aja nafunkha zonse zamumzindamo, chifukwa choti anali atamgwiririra mlongo wao.
28
Adalanda nkhosa, zoŵeta, pamodzi ndi abulu ao ndi zonse zimene zinali mumzindamo ndiponso za ku minda yao.
29
Adatenga chuma chonse, nagwira akazi onse ndi ana, nkutenganso zonse za m'nyumba mwao.
30
Yakobe adauza Simeoni ndi Levi kuti, “Hi, mwandiputira nkhondo. Dzina langa laipa pakati pa anthu a dziko lino, Akanani ndi Aperizi. Ine ndilibe anthu ambiri, tsono iwoŵa akaitanizana kuti adzandithire nkhondo, ine ndi banja langa lonse, tonse pamodzi tidzaonongeka.”
31
Koma iwowo adati, “Pepani, mlongo wathu sangamusandutse mkazi wachiwerewere ai!”
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 35 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50