bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 20
Genesis 20
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 21 →
1
Abrahamu adachokako ku Mamure kuja napita ku Negebu, chigawo chakumwera. Adakakhala pakati pa mzinda wa Kadesi ndi dziko la Suri, nakhazikika ku dziko la Gerari.
2
Kumeneko adauza anthu kuti, “Sarayu ndi mlongo wanga.” Motero Abimeleki, mfumu ya ku Gerari, adamtenga Sarayo.
3
Tsono Mulungu adamuwonekera usiku m'maloto nati, “Ufatu iwe chifukwa mkazi watengayu ndi wokwatiwa.”
4
Koma Abimeleki anali asanamkhudze mkaziyo, choncho adati, “Ambuye, kodi Inu mungaphedi munthu wosalakwa?
5
Abrahamu pondiwuza adati, ‘Ndi mlongo wanga,’ ndipo iyenso mwini wake ankanena kuti, ‘Ndi mlongo wanga.’ Ine pochita zimenezi, mtima wanga sudanditsutse konse, ndipo sindidalakwe.”
6
Mulungu adamuyankha m'maloto momwemo kuti, “Inde ndikudziŵa kuti iwe udachita zimenezi popanda mtima wako kukutsutsa. Choncho ndidakuletsa ndine kuti usandichimwire pakumkhudza mkaziyo.
7
Koma tsopano, umpereke mkazi ameneyu kwa mwamuna wake. Mwamunayo ndi mneneri, ndipo adzakupempherera kuti usafe. Koma ukapanda kumpereka, ndikukuchenjezeratu kuti udzafa ndithu, iweyo ndi banja lako lonse.”
8
M'maŵa mwake, m'mamaŵa, Abimeleki adaitana antchito ake onse naŵauza zonsezi, ndipo anthuwo adachita mantha kwambiri.
9
Tsono Abimeleki adaitana Abrahamu namufunsa kuti, “Kodi iwe watichita zotani? Kodi ine ndakulakwira chiyani, kuti iweyo undiputire chilango chotere ine ndi onse a mu ufumu wanga? Zimene wandichitazi nzosayenera konse kuzichita.
10
Chifukwa chiyani wachita zimenezi?”
11
Abrahamu adayankha kuti, “Ndinkaganiza kuti kuno kulibe ndi mmodzi yemwe woopa Mulungu, ndipo kuti akadandipha nkutenga mkazi wangayu.
12
Komabetu, kunena zoona, ndi mlongo wangadi ameneyu, chifukwa ndi mwana wa bambo wanga, koma osati womubala mai wanga, ineyo nkumukwatira.
13
Motero pamene Mulungu adandituma kuchokera kunyumba kwa bambo wanga, kuti ndipite ku maiko achilendo, ndidaamuuza mkazi wangayu kuti, ‘Undiwonetse kuti ndiwedi wokhulupirika kwa ine, pouza aliyense kuti ndine mlongo wako, kulikonse kumene tizipita.’ ”
14
Tsono Abimeleki adabwezera Sara kwa Abrahamu, ndipo nthaŵi yomweyo adampatsa nkhosa, ng'ombe ndi akapolo aamuna ndi aakazi.
15
Adauza Abrahamu kuti, “Dziko lonseli ndi langa, ungathe kukhala kulikonse komwe ukufuna.”
16
Ndipo adauza Sara kuti, “Mlongo wakoyu ndikumpatsa ndalama zasiliva chikwi chimodzi, kuti zikhale ngati mboni kwa onse amene ali nawoŵa kuti iwe ndiwe wosalakwa.”
17
Motero Abrahamu adapempherera Abimeleki, ndipo Mulungu adamchiza. Adachizanso mkazi wake pamodzi ndi antchito ake aakazi, kuti onsewo azitha kubala.
18
Ndiye kuti Chauta anali ataŵatseka akazi onse a m'banja la Abimeleki kuti akhale osabala, chifukwa cha Sara mdzakazi wa Abrahamu.
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50