bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 14
Genesis 14
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 15 →
1
Masiku amenewo, Amurafere mfumu ya ku Sinara, Ariyoki mfumu ya ku Elasara, Kedorilaomere mfumu ya ku Elamu, ndi Tidala mfumu ya ku Goimu,
2
onseŵa adasonkhana kuti athire nkhondo mafumu asanu aŵa: Mfumu Bera wa ku Sodomu, mfumu Birisa wa ku Gomora, mfumu Sinabe wa ku Adima, mfumu Semebera wa ku Zeboimu ndi mfumu ya ku Bela (ndiye kuti Zowari).
3
Mafumu asanu ameneŵa adasonkhana pamodzi ndi ankhondo ao onse m'chigwa cha Sidimu, (ku Nyanja Yakufa).
4
Kedorilaomere ndiye ankalamulira onseŵa pa zaka khumi ndi ziŵiri, koma chaka chakhumi ndi chitatu onseŵa adamuukira.
5
Pa chaka chakhumi ndi chinai Kedorilaomere pamodzi ndi anzake ogwirizana nawo, adadza ndi nkhondo nagonjetsa Arefaimu amene ankakhala ku Asiteroti-karanaimu, Azuzimu amene ankakhala ku Hamu, ndi Aemimu amene ankakhala ku chigwa cha Kiriyataimu.
6
Adagonjetsanso Ahori amene ankakhala m'mapiri a Seiri mpaka ku Eliparani ku malire a chipululu.
7
Ndipo adapotoloka, nakafika ku Enimisipati (ndiye kuti Kadesi), ndipo adagonjetsa dziko lonse la Aamaleke pamodzi ndi la Aamori amene ankakhala ku Hazazoni-Tamara.
8
Tsono mafumu a ku Sodomu, Gomora, Adima, Zeboimu ndi Bela adasonkhanitsa ankhondo ao m'chigwa cha Sidimu, nalimbana
9
ndi Kedorilaomere wa ku Elamu, Tidala wa ku Goimu, Amurafere wa ku Sinara ndi Ariyoki wa ku Elasara, mafumu asanu kulimbana ndi mafumu anai.
10
Chigwa cha Sidimu chinali chodzaza ndi maenje a phula. Tsono anthu a ku Sodomu ndi Gomora adagonja nathaŵa nkhondo, ndipo adagwa m'maenjemo, koma ena adathaŵira ku mapiri.
11
Mafumu anai aja adatenga zonse za ku Sodomu ndi za ku Gomora, pamodzi ndi chakudya, nachokapo.
12
Adamtenganso Loti, mphwake wa Abramu uja, pamodzi ndi zake zonse, chifukwa ankakhala ku Sodomu komweko.
13
Koma munthu wina atapulumuka, adabwera kwa Abramu Muhebri uja, namuuza zonsezi. Abramuyo ankakhala pafupi ndi mitengo ija ya thundu ya ku Mamure, wa fuko la Amoni, mbale wa Esikolo ndi Anere, amene ankagwirizana ndi Abramu pa nkhondo.
14
Abramu atamva kuti mbale wake wagwidwa, adasonkhanitsa anthu ake odziŵa kumenya nkhondo. Onse pamodzi analipo 318, ndipo adalondola mafumu aja njira yonse mpaka ku Dani.
15
Atafika kumeneko, adagaŵa anthu ake m'magulu, ndipo iye ndi anthu ake adakamenyana nawo ndi usiku mpaka kuŵagonjetseratu. Adaŵapirikitsa mpaka ku Hoba, kumpoto kwa Damasiko,
16
ndipo adaŵalanda zao zonse. Adabwera naye Loti, mwana wa mbale wake, pamodzi ndi zake zonse, kuphatikizapo akazi ndi anthu ena onse.
17
Pamene Abramu ankabwera kuchokera kumene adakagonjetsa Kedorilaomere ndi mafumu ena ogwirizana naye aja, mfumu ya ku Sodomu idatuluka kukakumana naye ku Chigwa cha Save (ndiye kuti Chigwa cha Mfumu).
18
Ndipo Melkizedeki, mfumu ya ku Salemu, wansembe wa Mulungu Wopambanazonse, adabwera kwa Abramu atatenga buledi ndi vinyo.
19
Adadalitsa Abramuyo, adati, “Mulungu Wopambanazonse, Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi, akudalitse iwe Abramu.
20
Atamandike Mulungu Wopambanazonse, amene adakupatsa mphamvu zogonjetsera adani ako onse.” Pamenepo Abramu adapereka kwa Melkizedeki chigawo chachikhumi cha zinthu zonse zimene adaalanda.
21
Komanso mfumu ya ku Sodomu idapempha Abramu kuti “Zinthu zonse mudatengazi, musunge, koma anthu anga okhaŵa mundipatse.”
22
Koma Abramu adayankha kuti, “Ndikulumbira pamaso pa Chauta, Mulungu Wopambanazonse, Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi
23
kuti sindidzatenga zinthu zako mpang'ono pomwe. Sindidzatenga ngakhale mbota kapena chingwe chomangira nsapato, kuti ungamadzanene kuti, ‘Abramu ndidamulemeza ndine.’
24
Sinditenga kalikonse ai. Nditengako zokhazo zimene anyamata anga adadya, ndi zoyenera kugaŵira amene adandiperekeza, monga Anere, Esikolo ndi Mamure. Iwo atengeko magawo ao.”
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
Recommended Reading
Commentary
Genesis Commentaries
→
Devotional
Genesis Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→