bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 6
Genesis 6
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 7 →
1
Nthaŵi imeneyo anthu anali atayamba kuchuluka pa dziko lonse lapansi, ndipo adabereka ana aakazi.
2
Ana aamuna a Mulungu adaona kuti ana aakazi a anthu anali okongola, nayamba kukwatira amene ankaŵakonda.
3
Tsono Chauta adati, “Sindidzalola anthu kukhala ndi moyo mpaka muyaya, popeza kuti munthu ndi thupi limene limafa. Kuyambira tsopano adzangokhala zaka 120.”
4
Pa masiku amenewo, ngakhale pambuyo pakenso, panali anthu amphamvu ataliatali pa dziko lapansi. Anthu ameneŵa ndi amene ankabadwa mwa akazi omwe adaakwatiwa ndi ana a Mulungu aja. Iwoŵa anali ngwazi zomveka ndiponso anthu otchuka pa masiku akalewo.
5
Pamene Chauta adaona kuti anthu a pa dziko lapansi aipa koopsa, ndiponso kuti mitima yao inali yodzaza ndi maganizo oipa,
6
adamva chisoni kuti adalenga anthu ndi kuŵakhazika pa dziko lapansi, ndipo adavutika mu mtima.
7
Tsono adati, “Anthu onse amene ndaŵalenga, ndidzaŵaononga kotheratu. Ndidzaononganso nyama zonse ndi zokwaŵa zomwe pamodzi ndi mbalame, chifukwa ndikumva chisoni kuti ndidalenga zimenezi.”
8
Koma Nowa yekha anali wangwiro pamaso pa Chauta.
9
Nayi mbiri ya Nowa. Nowa anali munthu wochita zokondweretsa Mulungu, wopanda cholakwa, ndipo pa nthaŵi imeneyo adaali yekhayo amene anali wabwino pamaso pa Mulungu.
10
Anali ndi ana aamuna atatu: Semu, Hamu ndi Yafeti.
11
Koma anthu ena onse anali oipa pamaso pa Mulungu, ndipo kuipa kwao kudawanda ponseponse.
12
Mulungu atayang'ana dziko lapansi, adaona kuti ndi lonyansa, chifukwa anthu onse anali oipa kwambiri.
13
Choncho Mulungu adauza Nowa kuti, “Ndatsimikiza mu mtima kuti ndiwononge anthu onse. Ndidzaŵaononga kotheratu chifukwa dziko lonse lapansi ladzaza ndi ntchito zao zoipa.
14
Udzipangire chombo ndipo uchipange ndi matabwa a mtengo wa mnjale. Upange zipinda m'menemo, ndipo uchimate phula kunja kwake ndi m'kati momwe.
15
M'litali mwake mwa chombocho mukhale mamita 140. M'mimba mwake mukhale mamita 23, ndipo msinkhu wake ukhale wa mamita 13 ndi theka.
16
Upange denga la chombocho, ndipo usiye mpata wa masentimita 50 pakati pa dengalo ndi mbali zake. Uchimange mosanjikiza, chikhale cha nyumba zitatu, ndipo m'mbali mwake mukhale chitseko.
17
Ndidzagwetsa mvula yachigumula pa dziko lapansi, kuti iwononge zamoyo zonse. Zonse zapadziko zidzafa,
18
koma iweyo ndidzachita nawe chipangano. Udzaloŵe m'chombomo iwe pamodzi ndi mkazi wako, ndi ana ako pamodzi ndi akazi ao.
19
Ndipo udzatengenso nyama za mtundu uliwonse, yaimuna ndi yaikazi, kuti zisungidwe ndi moyo.
20
Mbalame za mtundu uliwonse ndi nyama zazikulu ndi zokwaŵa zomwe, zidzaloŵe m'chombo kuti zisungidwe ndi moyo.
21
Udzatengenso zakudya za mtundu uliwonse kuti inu ndi nyamazo muzidzadya.”
22
Motero Nowa adachitadi zonse zimene Mulungu adamlamula.
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50