bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 48
Genesis 48
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 47
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 49 →
1
Patapita kanthaŵi, Yosefe adamva kuti “Bambo wanu akudwala.” Adatenga ana ake aŵiri, Manase ndi Efuremu, napita nawo kwa Yakobe.
2
Yakobeyo atamva kuti “Mwana wanu Yosefe wabwera kudzakuzondani,” adadzilimbitsa, nadzuka, nkukhala tsonga pabedi pompo.
3
Adauza Yosefe kuti, “Mulungu Mphambe amene adandiwonekera ku Luzi m'dziko la Kanani, adandidalitsa.
4
Adandiwuza kuti, ‘Ndidzakupatsa ana ambiri kotero kuti zidzukulu zako zidzasanduka mitundu yambiri ya anthu. Dziko lino ndidzapatsa zidzukulu zako kuti likhale lao mpaka muyaya.’
5
Tsono ana ako aŵiri, amene udabereka ku Ejipito kuno, ine ndisanabwere, amenewonso ndi anga. Efuremu ndi Manase adzakhala anga ndithu, monga momwe aliri Rubeni ndi Simeoni.
6
Koma obadwa pambuyo pa iwowo, ndi ako amenewo. Adzalandira choloŵa chao pamodzi ndi achibale ao.
7
Ndachita zimenezi chifukwa chakuti pamene ndinkabwerera kuchokera ku Mesopotamiya, mai wako Rakele adafera m'dziko la Kanani, mtunda wofika ku Efurata ukadalipo. Chisoni changa chinali chachikulu. Tsono ndidamuika komweko pa mseu wa ku Efurata ku Betelehemu.”
8
Yakobe ataona ana a Yosefe, adafunsa kuti, “Nanga anyamata aŵa nga yani?”
9
Yosefe adayankha kuti “Ameneŵa ndi ana anga amene Mulungu adandipatsa ku Ejipito kuno.” Apo Yakobe adati, “Chonde abwere kuno anawo kuti ndiŵadalitse.”
10
Maso a Yakobe sankapenya bwino chifukwa cha ukalamba. Yosefe adabwera nawo kwa iye anawo ndipo Yakobe adaŵakumbatira, naŵampsompsona.
11
Yakobe adauza Yosefe kuti, “Sindinkayembekeza kuti ndingakuwonenso, koma tsopano Mulungu wandilola kuti ndiwone ndi ana ako omwe.”
12
Tsono Yosefe adatenga anawo kuŵachotsa pa maondo a Yakobe. Ndipo adamgwadira.
13
Yosefe adaŵagwira padzanja anawo, Efuremu ku dzanja lamanja kuti pakutero akhale ku dzanja lamanzere la Yakobe. Manase adakhala kumanzere kuti pakutero akhale ku dzanja lamanja la Yakobe.
14
Koma Yakobe adasemphanitsa manja. Motero adasanjika dzanja lake lamanja pamutu pa Efuremu amene anali wamng'ono, dzanja lamanzere adalisanjika pamutu pa Manase amene anali wamkulu.
15
Ndipo adadalitsa Yosefe ndi mau akuti, “Mulungu amene makolo anga Abrahamu ndi Isaki adamtumikira, Mulungu amene wanditsogolera moyo wanga wonse mpaka lero lino, aŵadalitse anaŵa!
16
Mngelo amene wandiwombola ku zoipa zonse, aŵadalitsenso! Podzera mwa anaŵa, dzina langa ndi maina a makolo anga Abrahamu ndi Isaki akhale omveka nthaŵi zonse! Adzakhale ndi ana ambiri iwoŵa, adzasanduke mtundu waukulu pa dziko lapansi!”
17
Yosefe ataona kuti bambo wake wasanjika dzanja lamanja pamutu pa Efuremu, adakhumudwa. Motero adatenga dzanja la bambo wake kulichotsa pamutu pa Efuremu, nalisanjika pamutu pa Manase.
18
Adauza bambo wake kuti, “Musatero atate. Wamkulu ndi uyu. Dzanja lanu lamanja likhale pamutu pa ameneyu.”
19
Koma bambo wakeyo adakana nati, “Ndikudziŵa, mwana wanga, ndikudziŵa. Adzukulu a Manase adzakhalanso anthu otchuka, koma mng'ono wakeyu adzatchuka kupambana iye, ndipo zidzukulu zake zidzakhala mitundu yaikulu ya anthu.”
20
Motero adaŵadalitsa pa tsiku limenelo ndi mau akuti, “Aisraele adzatchula maina anu podalitsa. Adzanena kuti, ‘Mulungu akudalitseni inu monga Efuremu ndi Manase.’ ” Mwa njira imeneyi adaika Efuremu patsogolo pa Manase.
21
Pambuyo pake Yakobe adauza Yosefe kuti, “Ukuwonatu kuti ndili pafupi kufa, koma Mulungu adzakhala nawe, ndipo adzakubweza ku dziko la makolo ako.
22
Ndiponso iweyo, osati abale ako, ndikukupatsa Sekemu, dera lija limene ndidachita cholanda ndi lupanga langa ndi uta wanga kwa Aamori.”
← Chapter 47
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 49 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50